< תהילים 147 >

הללו-יה כי-טוב זמרה אלהינו-- כי-נעים נאוה תהלה 1
Tamandani Yehova. Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu, nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!
בונה ירושלם יהוה נדחי ישראל יכנס 2
Yehova akumanga Yerusalemu; Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.
הרפא לשבורי לב ומחבש לעצבותם 3
Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.
מונה מספר לכוכבים לכלם שמות יקרא 4
Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, ndipo iliyonse amayitchula dzina.
גדול אדונינו ורב-כח לתבונתו אין מספר 5
Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.
מעודד ענוים יהוה משפיל רשעים עדי-ארץ 6
Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa, koma amagwetsa pansi anthu oyipa.
ענו ליהוה בתודה זמרו לאלהינו בכנור 7
Imbirani Yehova ndi mayamiko; imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
המכסה שמים בעבים-- המכין לארץ מטר המצמיח הרים חציר 8
Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo; amapereka mvula ku dziko lapansi ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.
נותן לבהמה לחמה לבני ערב אשר יקראו 9
Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.
לא בגבורת הסוס יחפץ לא-בשוקי האיש ירצה 10
Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo, kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.
רוצה יהוה את-יראיו-- את-המיחלים לחסדו 11
Yehova amakondwera ndi amene amamuopa, amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.
שבחי ירושלם את-יהוה הללי אלהיך ציון 12
Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu; tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
כי-חזק בריחי שעריך ברך בניך בקרבך 13
pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
השם-גבולך שלום חלב חטים ישביעך 14
Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.
השלח אמרתו ארץ עד-מהרה ירוץ דברו 15
Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi; mawu ake amayenda mwaliwiro.
הנתן שלג כצמר כפור כאפר יפזר 16
Amagwetsa chisanu ngati ubweya ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
משליך קרחו כפתים לפני קרתו מי יעמד 17
Amagwetsa matalala ngati miyala. Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
ישלח דברו וימסם ישב רוחו יזלו-מים 18
Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka; amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.
מגיד דברו ליעקב חקיו ומשפטיו לישראל 19
Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo, malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
לא עשה כן לכל-גוי-- ומשפטים בל-ידעום הללו-יה 20
Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu; anthu enawo sadziwa malamulo ake. Tamandani Yehova.

< תהילים 147 >