< תהילים 145 >
תהלה לדוד ארוממך אלוהי המלך ואברכה שמך לעולם ועד | 1 |
Salimo la matamando la Davide. Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga; ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
בכל-יום אברכך ואהללה שמך לעולם ועד | 2 |
Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
גדול יהוה ומהלל מאד ולגדלתו אין חקר | 3 |
Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse; ukulu wake palibe angawumvetsetse.
דור לדור ישבח מעשיך וגבורתיך יגידו | 4 |
Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina; Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
הדר כבוד הודך-- ודברי נפלאתיך אשיחה | 5 |
Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
ועזוז נוראתיך יאמרו וגדלותיך (וגדלתך) אספרנה | 6 |
Iwo adzafotokoza za mphamvu ya ntchito zanu zoopsa kwambiri, ndipo ine ndidzalengeza za ntchito zanu zazikulu.
זכר רב-טובך יביעו וצדקתך ירננו | 7 |
Adzakondwerera kuchuluka kwa ubwino wanu, ndi kuyimba mwachimwemwe za chilungamo chanu.
חנון ורחום יהוה ארך אפים וגדל-חסד | 8 |
Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
טוב-יהוה לכל ורחמיו על-כל-מעשיו | 9 |
Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.
יודוך יהוה כל-מעשיך וחסידיך יברכוכה | 10 |
Zonse zimene munazipanga zidzakutamandani, Inu Yehova; oyera mtima adzakulemekezani.
כבוד מלכותך יאמרו וגבורתך ידברו | 11 |
Iwo adzafotokoza za ulemerero wa ufumu wanu ndi kuyankhula za mphamvu yanu,
להודיע לבני האדם--גבורתיו וכבוד הדר מלכותו | 12 |
kuti anthu onse adziwe za machitidwe anu amphamvu ndi ulemerero wokongola wa ufumu wanu.
מלכותך מלכות כל-עלמים וממשלתך בכל-דור ודר | 13 |
Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ndipo ulamuliro wanu ndi wosatha pa mibado yonse. Yehova ndi wokhulupirika pa malonjezo ake onse ndi wokonda zonse zimene Iye anazipanga.
סומך יהוה לכל-הנפלים וזוקף לכל-הכפופים | 14 |
Yehova amagwiriziza onse amene akugwa ndipo amakweza onse otsitsidwa.
עיני-כל אליך ישברו ואתה נותן-להם את-אכלם בעתו | 15 |
Maso a onse amayangʼana kwa Inu, ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera.
פותח את-ידך ומשביע לכל-חי רצון | 16 |
Mumatsekula dzanja lanu ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.
צדיק יהוה בכל-דרכיו וחסיד בכל-מעשיו | 17 |
Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
קרוב יהוה לכל-קראיו-- לכל אשר יקראהו באמת | 18 |
Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
רצון-יראיו יעשה ואת-שועתם ישמע ויושיעם | 19 |
Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa; amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
שומר יהוה את-כל-אהביו ואת כל-הרשעים ישמיד | 20 |
Yehova amayangʼana onse amene amamukonda koma adzawononga anthu onse oyipa.
תהלת יהוה ידבר-פי ויברך כל-בשר שם קדשו--לעולם ועד | 21 |
Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova. Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera ku nthawi za nthawi.