< תהילים 144 >

לדוד ברוך יהוה צורי-- המלמד ידי לקרב אצבעותי למלחמה 1
Salimo la Davide. Atamandike Yehova Thanthwe langa, amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; zala zanga kumenya nkhondo.
חסדי ומצודתי משגבי ומפלטי-לי מגני ובו חסיתי הרודד עמי תחתי 2
Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa, linga langa ndi mpulumutsi wanga, chishango changa mmene ine ndimathawiramo, amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.
יהוה--מה-אדם ותדעהו בן-אנוש ותחשבהו 3
Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira, mwana wa munthu kuti muzimuganizira?
אדם להבל דמה ימיו כצל עובר 4
Munthu ali ngati mpweya; masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.
יהוה הט-שמיך ותרד גע בהרים ויעשנו 5
Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi; khudzani mapiri kuti atulutse utsi.
ברוק ברק ותפיצם שלח חציך ותהמם 6
Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani; ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.
שלח ידיך ממרום פצני והצילני ממים רבים מיד בני נכר 7
Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba; landitseni ndi kundipulumutsa, ku madzi amphamvu, mʼmanja mwa anthu achilendo,
אשר פיהם דבר-שוא וימינם ימין שקר 8
amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.
אלהים--שיר חדש אשירה לך בנבל עשור אזמרה-לך 9
Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu; ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,
הנותן תשועה למלכים הפוצה את-דוד עבדו--מחרב רעה 10
kwa Iye amene amapambanitsa mafumu, amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.
פצני והצילני מיד בני-נכר אשר פיהם דבר-שוא וימינם ימין שקר 11
Landitseni ndi kundipulumutsa, mʼmanja mwa anthu achilendo, amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza, amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.
אשר בנינו כנטעים-- מגדלים בנעוריהם בנותינו כזוית-- מחטבות תבנית היכל 12
Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino, ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
מזוינו מלאים-- מפיקים מזן אל-זן צאוננו מאליפות מרבבות-- בחוצותינו 13
Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza ndi zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda pa mabusa athu.
אלופינו מסבלים אין-פרץ ואין יוצאת ואין צוחה ברחבתינו 14
Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera. Sipadzakhala mingʼalu pa makoma, sipadzakhalanso kupita ku ukapolo, mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.
אשרי העם שככה לו אשרי העם שיהוה אלהיו 15
Odala anthu amene adzalandira madalitso awa; odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

< תהילים 144 >