< תהילים 143 >

מזמור לדוד יהוה שמע תפלתי-- האזינה אל-תחנוני באמנתך ענני בצדקתך 1
Salimo la Davide. Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza.
ואל-תבוא במשפט את-עבדך כי לא-יצדק לפניך כל-חי 2
Musazenge mlandu mtumiki wanu, pakuti palibe munthu wamoyo amene ndi wolungama pamaso panu.
כי רדף אויב נפשי-- דכא לארץ חיתי הושבני במחשכים כמתי עולם 3
Mdani akundithamangitsa, iye wandipondereza pansi; wachititsa kuti ndikhale mu mdima ngati munthu amene anafa kale.
ותתעטף עלי רוחי בתוכי ישתומם לבי 4
Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga; mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa.
זכרתי ימים מקדם-- הגיתי בכל-פעלך במעשה ידיך אשוחח 5
Ndimakumbukira masiku amakedzana; ndimalingalira za ntchito yanu yonse, ndimaganizira zimene manja anu anachita.
פרשתי ידי אליך נפשי כארץ-עיפה לך סלה 6
Ndatambalitsa manja anga kwa Inu; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu monga nthaka yowuma. (Sela)
מהר ענני יהוה-- כלתה רוחי אל-תסתר פניך ממני ונמשלתי עם-ירדי בור 7
Yehova ndiyankheni msanga; mzimu wanga ukufowoka. Musandibisire nkhope yanu, mwina ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
השמיעני בבקר חסדך-- כי-בך בטחתי הודיעני דרך-זו אלך-- כי-אליך נשאתי נפשי 8
Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika, pakuti ine ndimadalira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo, pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.
הצילני מאיבי יהוה-- אליך כסתי 9
Pulumutseni kwa adani anga, Inu Yehova, pakuti ndimabisala mwa Inu.
למדני לעשות רצונך-- כי-אתה אלוהי רוחך טובה תנחני בארץ מישור 10
Phunzitseni kuchita chifuniro chanu, popeza ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
למען-שמך יהוה תחיני בצדקתך תוציא מצרה נפשי 11
Sungani moyo wanga Inu Yehova chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu tulutseni mʼmasautso anga.
ובחסדך תצמית איבי והאבדת כל-צררי נפשי--כי אני עבדך 12
Mwa chikondi chanu chosasinthika khalitsani chete adani anga; wonongani adani anga, pakuti ndine mtumiki wanu.

< תהילים 143 >