< תהילים 138 >
לדוד אודך בכל-לבי נגד אלהים אזמרך | 1 |
Salimo la Davide. Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
אשתחוה אל-היכל קדשך ואודה את-שמך-- על-חסדך ועל-אמתך כי-הגדלת על-כל-שמך אמרתך | 2 |
Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.
ביום קראתי ותענני תרהבני בנפשי עז | 3 |
Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.
יודוך יהוה כל-מלכי-ארץ כי שמעו אמרי-פיך | 4 |
Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova, pamene amva mawu a pakamwa panu.
וישירו בדרכי יהוה כי-גדול כבוד יהוה | 5 |
Iwo ayimbe za njira za Yehova, pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.
כי-רם יהוה ושפל יראה וגבה ממרחק יידע | 6 |
Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
אם-אלך בקרב צרה-- תחיני על אף איבי תשלח ידך ותושיעני ימינך | 7 |
Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
יהוה יגמר בעדי יהוה חסדך לעולם מעשי ידיך אל-תרף | 8 |
Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine; chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha musasiye ntchito ya manja anu.