< תהילים 130 >

שיר המעלות ממעמקים קראתיך יהוה 1
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
אדני שמעה בקולי תהיינה אזניך קשבות-- לקול תחנוני 2
Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga.
אם-עונות תשמר-יה-- אדני מי יעמד 3
Inu Yehova, mukanamawerengera machimo, Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
כי-עמך הסליחה-- למען תורא 4
Koma kwa Inu kuli chikhululukiro; nʼchifukwa chake mumaopedwa.
קויתי יהוה קותה נפשי ולדברו הוחלתי 5
Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera, ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
נפשי לאדני-- משמרים לבקר שמרים לבקר 6
Moyo wanga umayembekezera Ambuye, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
יחל ישראל אל-יהוה כי-עם-יהוה החסד והרבה עמו פדות 7
Yembekeza Yehova, iwe Israeli, pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
והוא יפדה את-ישראל-- מכל עונתיו 8
Iye mwini adzawombola Israeli ku machimo ake onse.

< תהילים 130 >