< תהילים 119 >

אשרי תמימי-דרך-- ההלכים בתורת יהוה 1
Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa, amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.
אשרי נצרי עדתיו בכל-לב ידרשוהו 2
Odala ndi amene amasunga malamulo ake, amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
אף לא-פעלו עולה בדרכיו הלכו 3
Sachita cholakwa chilichonse; amayenda mʼnjira zake.
אתה צויתה פקדיך-- לשמר מאד 4
Inu mwapereka malangizo ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.
אחלי יכנו דרכי-- לשמר חקיך 5
Aa! Ndikanakonda njira zanga zikanakhala zokhazikika pa kumvera zophunzitsa zanu!
אז לא-אבוש-- בהביטי אל-כל-מצותיך 6
Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi, poganizira malamulo anu onse.
אודך בישר לבב-- בלמדי משפטי צדקך 7
Ndidzakutamandani ndi mtima wolungama, pamene ndikuphunzira malamulo anu olungama.
את-חקיך אשמר אל-תעזבני עד-מאד 8
Ndidzamvera zophunzitsa zanu; musanditaye kwathunthu.
במה יזכה-נער את-ארחו-- לשמר כדברך 9
Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.
בכל-לבי דרשתיך אל-תשגני ממצותיך 10
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
בלבי צפנתי אמרתך-- למען לא אחטא-לך 11
Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.
ברוך אתה יהוה-- למדני חקיך 12
Mutamandike Inu Yehova; phunzitseni malamulo anu.
בשפתי ספרתי-- כל משפטי-פיך 13
Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse amene amachokera pakamwa panu.
בדרך עדותיך ששתי-- כעל כל-הון 14
Ndimakondwera potsatira malamulo anu monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.
בפקודיך אשיחה ואביטה ארחתיך 15
Ndimalingalira malangizo anu ndipo ndimaganizira njira zanu.
בחקתיך אשתעשע לא אשכח דברך 16
Ndimakondwera ndi malamulo anu; sindidzayiwala konse mawu anu.
גמל על-עבדך אחיה ואשמרה דברך 17
Chitirani zokoma mtumiki wanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; kuti tsono ndisunge mawu anu.
גל-עיני ואביטה-- נפלאות מתורתך 18
Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.
גר אנכי בארץ אל-תסתר ממני מצותיך 19
Ine ndine mlendo pa dziko lapansi; musandibisire malamulo anu.
גרסה נפשי לתאבה-- אל-משפטיך בכל-עת 20
Moyo wanga wafowoka polakalaka malamulo anu nthawi zonse.
גערת זדים ארורים-- השגים ממצותיך 21
Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa, amene achoka pa malamulo anu.
גל מעלי חרפה ובוז כי עדתיך נצרתי 22
Mundichotsere chitonzo ndi mnyozo pakuti ndimasunga malamulo anu.
גם ישבו שרים בי נדברו-- עבדך ישיח בחקיך 23
Ngakhale mafumu akhale pamodzi kundinyoza, mtumiki wanu adzalingalirabe zophunzitsa zanu.
גם-עדתיך שעשעי-- אנשי עצתי 24
Malamulo anu amandikondweretsa; ndiwo amene amandilangiza.
דבקה לעפר נפשי חיני כדברך 25
Moyo wanga wakangamira fumbi; tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.
דרכי ספרתי ותענני למדני חקיך 26
Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha; phunzitseni malamulo anu.
דרך-פקודיך הבינני ואשיחה בנפלאותיך 27
Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu; pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.
דלפה נפשי מתוגה קימני כדברך 28
Moyo wanga wafowoka ndi chisoni; limbikitseni monga mwa mawu anu.
דרך-שקר הסר ממני ותורתך חנני 29
Mundichotse mʼnjira zachinyengo; mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.
דרך-אמונה בחרתי משפטיך שויתי 30
Ndasankha njira ya choonadi; ndayika malamulo anu pa mtima panga.
דבקתי בעדותיך יהוה אל-תבישני 31
Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova; musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
דרך-מצותיך ארוץ כי תרחיב לבי 32
Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu, pakuti Inu mwamasula mtima wanga.
הורני יהוה דרך חקיך ואצרנה עקב 33
Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu; ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.
הבינני ואצרה תורתך ואשמרנה בכל-לב 34
Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.
הדריכני בנתיב מצותיך כי-בו חפצתי 35
Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu, pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.
הט-לבי אל-עדותיך ואל אל-בצע 36
Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.
העבר עיני מראות שוא בדרכך חיני 37
Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe; sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.
הקם לעבדך אמרתך-- אשר ליראתך 38
Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu, kuti Inu muopedwe.
העבר חרפתי אשר יגרתי כי משפטיך טובים 39
Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa, pakuti malamulo anu ndi abwino.
הנה תאבתי לפקדיך בצדקתך חיני 40
Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu! Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.
ויבאני חסדך יהוה תשועתך כאמרתך 41
Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova, chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
ואענה חרפי דבר כי-בטחתי בדברך 42
ndipo ndidzayankha amene amandinyoza, popeza ndimadalira mawu anu.
ואל-תצל מפי דבר-אמת עד-מאד כי למשפטך יחלתי 43
Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga, pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
ואשמרה תורתך תמיד-- לעולם ועד 44
Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse, ku nthawi za nthawi.
ואתהלכה ברחבה כי פקדיך דרשתי 45
Ndidzayendayenda mwaufulu, chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
ואדברה בעדתיך נגד מלכים ולא אבוש 46
Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
ואשתעשע במצותיך אשר אהבתי 47
popeza ndimakondwera ndi malamulo anu chifukwa ndimawakonda.
ואשא-כפי--אל-מצותיך אשר אהבתי ואשיחה בחקיך 48
Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda, ndipo ndimalingalira malangizo anu.
זכר-דבר לעבדך-- על אשר יחלתני 49
Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu, popeza mwandipatsa chiyembekezo.
זאת נחמתי בעניי כי אמרתך חיתני 50
Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi: lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
זדים הליצני עד-מאד מתורתך לא נטיתי 51
Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa, koma sindichoka pa malamulo anu.
זכרתי משפטיך מעולם יהוה ואתנחם 52
Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale, ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.
זלעפה אחזתני מרשעים-- עזבי תורתך 53
Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa amene ataya malamulo anu.
זמרות היו-לי חקיך-- בבית מגורי 54
Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga kulikonse kumene ndigonako.
זכרתי בלילה שמך יהוה ואשמרה תורתך 55
Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova, ndipo ndidzasunga malamulo anu.
זאת היתה-לי כי פקדיך נצרתי 56
Ichi ndicho ndakhala ndikuchita: ndimasunga malangizo anu.
חלקי יהוה אמרתי-- לשמר דבריך 57
Yehova, Inu ndiye gawo langa; ndalonjeza kumvera mawu anu.
חליתי פניך בכל-לב חנני כאמרתך 58
Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse; mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.
חשבתי דרכי ואשיבה רגלי אל-עדתיך 59
Ndinalingalira za njira zanga ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.
חשתי ולא התמהמהתי-- לשמר מצותיך 60
Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza kumvera malamulo anu.
חבלי רשעים עודני תורתך לא שכחתי 61
Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe, sindidzayiwala lamulo lanu.
חצות-לילה--אקום להודות לך על משפטי צדקך 62
Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu chifukwa cha malamulo anu olungama.
חבר אני לכל-אשר יראוך ולשמרי פקודיך 63
Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani, kwa onse amene amatsatira malangizo anu.
חסדך יהוה מלאה הארץ חקיך למדני 64
Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu.
טוב עשית עם-עבדך-- יהוה כדברך 65
Inu Yehova, chitirani chabwino mtumiki wanu molingana ndi mawu anu.
טוב טעם ודעת למדני כי במצותיך האמנתי 66
Phunzitseni nzeru ndi chiweruzo chabwino, pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.
טרם אענה אני שגג ועתה אמרתך שמרתי 67
Ndisanayambe kuzunzika ndinasochera, koma tsopano ndimamvera mawu anu.
טוב-אתה ומטיב למדני חקיך 68
Inu ndinu abwino ndipo zimene mumachita ndi zabwino; phunzitseni malamulo anu.
טפלו עלי שקר זדים אני בכל-לב אצר פקודיך 69
Ngakhale odzikuza andipaka mabodza, ine ndimasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
טפש כחלב לבם אני תורתך שעשעתי 70
Mitima yawo ndi yowuma ndi yosakhudzidwa, koma ine ndimakondwera ndi malamulo anu.
טוב-לי כי-עניתי-- למען אלמד חקיך 71
Ndi bwino kuti ndinasautsidwa kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.
טוב-לי תורת-פיך-- מאלפי זהב וכסף 72
Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide.
ידיך עשוני ויכוננוני הבינני ואלמדה מצותיך 73
Manja anu anandilenga ndi kundiwumba; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ndiphunzire malamulo anu.
יראיך יראוני וישמחו כי לדברך יחלתי 74
Iwo amene amakuopani akondwere akandiona, chifukwa chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
ידעתי יהוה כי-צדק משפטיך ואמונה עניתני 75
Ine ndikudziwa, Inu Yehova, kuti malamulo anu ndi olungama ndipo mwandizunza chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
יהי-נא חסדך לנחמני-- כאמרתך לעבדך 76
Chikondi chanu chosasinthika chikhale chitonthozo changa, molingana ndi lonjezo lanu kwa mtumiki wanu.
יבאוני רחמיך ואחיה כי-תורתך שעשעי 77
Chifundo chanu chindifikire kuti ndikhale ndi moyo, popeza malamulo anu ndiye chikondwerero changa.
יבשו זדים כי-שקר עותוני אני אשיח בפקודיך 78
Odzikuza achititsidwe manyazi chifukwa cha kundilakwira popanda chifukwa; koma ine ndidzalingalira malangizo anu.
ישובו לי יראיך וידעו (וידעי) עדתיך 79
Iwo amene amakuopani atembenukire kwa ine, iwo amene amamvetsetsa umboni wanu.
יהי-לבי תמים בחקיך-- למען לא אבוש 80
Mtima wanga ukhale wopanda cholakwa pa chiphunzitso chanu kuti ndisachititsidwe manyazi.
כלתה לתשועתך נפשי לדברך יחלתי 81
Moyo wanga wafowoka ndi kufunafuna chipulumutso chanu, koma chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
כלו עיני לאמרתך-- לאמר מתי תנחמני 82
Maso anga alefuka pofunafuna lonjezo lanu; Ine ndikuti, “Kodi mudzanditonthoza liti?”
כי-הייתי כנאד בקיטור-- חקיך לא שכחתי 83
Ngakhale ndili ngati thumba lachikopa la vinyo pa utsi sindiyiwala zophunzitsa zanu.
כמה ימי-עבדך מתי תעשה ברדפי משפט 84
Kodi mtumiki wanu ayenera kudikira mpaka liti? Kodi mudzawalanga liti amene amandizunza?
כרו-לי זדים שיחות-- אשר לא כתורתך 85
Anthu osalabadira za Mulungu, odzikuza amandikumbira dzenje motsutsana ndi malamulo anu.
כל-מצותיך אמונה שקר רדפוני עזרני 86
Malamulo anu onse ndi odalirika; thandizeni, pakuti anthu akundizunza popanda chifukwa.
כמעט כלוני בארץ ואני לא-עזבתי פקדיך 87
Iwo anatsala pangʼono kundichotsa pa dziko lapansi koma sindinataye malangizo anu.
כחסדך חיני ואשמרה עדות פיך 88
Sungani moyo wanga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika, ndipo ndidzamvera umboni wa pakamwa panu.
לעולם יהוה-- דברך נצב בשמים 89
Mawu anu Yehova ndi amuyaya; akhazikika kumwambako.
לדר ודר אמונתך כוננת ארץ ותעמד 90
Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka ku mibado yonse; Inu munakhazikitsa dziko lapansi ndipo lilipobe.
למשפטיך עמדו היום כי הכל עבדיך 91
Malamulo anu alipobe mpaka lero lino, pakuti zinthu zonse zimatumikira Inu.
לולי תורתך שעשעי-- אז אבדתי בעניי 92
Malamulo anu akanapanda kukhala chikondwerero changa, ndikanawonongeka mʼmasautso anga.
לעולם לא-אשכח פקודיך כי בם חייתני 93
Ine sindidzayiwala konse malangizo anu, pakuti ndi malangizo anuwo munasunga moyo wanga.
לך-אני הושיעני כי פקודיך דרשתי 94
Ndine wanu, ndipulumutseni; pakuti ndasamala malangizo anu.
לי קוו רשעים לאבדני עדתיך אתבונן 95
Anthu oyipa akudikira kuti andiwononge, koma ndidzalingalira umboni wanu.
לכל-תכלה ראיתי קץ רחבה מצותך מאד 96
Ndadziwa kuti zinthu zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe malire konse.
מה-אהבתי תורתך כל-היום היא שיחתי 97
Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu! Ndimalingaliramo tsiku lonse.
מאיבי תחכמני מצותך כי לעולם היא-לי 98
Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga, popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
מכל-מלמדי השכלתי כי עדותיך שיחה לי 99
Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse popeza ndimalingalira umboni wanu.
מזקנים אתבונן כי פקודיך נצרתי 100
Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba, popeza ndimamvera malangizo anu.
מכל-ארח רע כלאתי רגלי-- למען אשמר דברך 101
Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa kuti ndithe kumvera mawu anu.
ממשפטיך לא-סרתי כי-אתה הורתני 102
Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu, pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.
מה-נמלצו לחכי אמרתך-- מדבש לפי 103
Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa, otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!
מפקודיך אתבונן על כן שנאתי כל-ארח שקר 104
Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu; kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.
נר-לרגלי דברך ואור לנתיבתי 105
Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.
נשבעתי ואקימה-- לשמר משפטי צדקך 106
Ndalumbira ndipo ndatsimikiza, kuti ndidzatsatira malamulo anu olungama.
נעניתי עד-מאד יהוה חיני כדברך 107
Ndazunzika kwambiri; Inu Yehova, sungani moyo wanga molingana ndi mawu anu.
נדבות פי רצה-נא יהוה ומשפטיך למדני 108
Inu Yehova, landirani matamando aufulu ochokera pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.
נפשי בכפי תמיד ותורתך לא שכחתי 109
Ngakhale moyo wanga umakhala mʼzoopsa nthawi ndi nthawi, sindidzayiwala malamulo anu.
נתנו רשעים פח לי ומפקודיך לא תעיתי 110
Anthu oyipa anditchera msampha, koma sindinasochere kuchoka pa malangizo anu.
נחלתי עדותיך לעולם כי-ששון לבי המה 111
Umboni wanu ndiye cholowa changa kwamuyaya; Iwo ndiye chimwemwe cha mtima wanga.
נטיתי לבי לעשות חקיך-- לעולם עקב 112
Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu mpaka kumapeto kwenikweni.
סעפים שנאתי ותורתך אהבתי 113
Ndimadana ndi anthu apawiripawiri, koma ndimakonda malamulo anu.
סתרי ומגני אתה לדברך יחלתי 114
Inu ndinu pothawirapo panga ndi chishango changa; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
סורו-ממני מרעים ואצרה מצות אלהי 115
Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa, kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!
סמכני כאמרתך ואחיה ואל-תבישני משברי 116
Mundichirikize molingana ndi lonjezo lanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo; musalole kuti chiyembekezo changa chipite pachabe.
סעדני ואושעה ואשעה בחקיך תמיד 117
Gwirizizeni, ndipo ndidzapulumutsidwa; nthawi zonse ndidzasamalira zophunzitsa zanu.
סלית כל-שוגים מחקיך כי-שקר תרמיתם 118
Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu, pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.
סגים--השבת כל-רשעי-ארץ לכן אהבתי עדתיך 119
Anthu onse oyipa a pa dziko lapansi mumawayesa ngati zinthu zakudzala; nʼchifukwa chake ndimakonda umboni wanu.
סמר מפחדך בשרי וממשפטיך יראתי 120
Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu; ndimachita mantha ndi malamulo anu.
עשיתי משפט וצדק בל-תניחני לעשקי 121
Ndachita zolungama ndi zabwino; musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.
ערב עבדך לטוב אל-יעשקני זדים 122
Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino, musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
עיני כלו לישועתך ולאמרת צדקך 123
Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu, kufunafuna lonjezo lanu lolungama.
עשה עם-עבדך כחסדך וחקיך למדני 124
Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
עבדך-אני הבינני ואדעה עדתיך 125
Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa, kuti ndimvetsetse umboni wanu.
עת לעשות ליהוה-- הפרו תורתך 126
Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu; malamulo anu akuswedwa.
על-כן אהבתי מצותיך-- מזהב ומפז 127
Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,
על-כן כל-פקודי כל ישרתי כל-ארח שקר שנאתי 128
ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka, ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.
פלאות עדותיך על-כן נצרתם נפשי 129
Maumboni anu ndi odabwitsa nʼchifukwa chake ndimawamvera.
פתח דבריך יאיר מבין פתיים 130
Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika; ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.
פי-פערתי ואשאפה כי למצותיך יאבתי 131
Ndimatsekula pakamwa panga ndi kupuma wefuwefu, kufunafuna malamulo anu.
פנה-אלי וחנני-- כמשפט לאהבי שמך 132
Tembenukirani kwa ine ndipo mundichitire chifundo, monga mumachitira nthawi zonse kwa iwo amene amakonda dzina lanu.
פעמי הכן באמרתך ואל-תשלט-בי כל-און 133
Tsogolerani mayendedwe anga molingana ndi mawu anu; musalole kuti tchimo lizindilamulira.
פדני מעשק אדם ואשמרה פקודיך 134
Ndiwomboleni mʼdzanja la anthu ondizunza, kuti ndithe kumvera malangizo anu.
פניך האר בעבדך ולמדני את-חקיך 135
Nkhope yanu iwalire mtumiki wanu ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
פלגי-מים ירדו עיני-- על לא-שמרו תורתך 136
Mitsinje ya misozi ikuyenda kuchoka mʼmaso mwanga, chifukwa anthu sakumvera malamulo anu.
צדיק אתה יהוה וישר משפטיך 137
Yehova ndinu wolungama, ndipo malamulo anu ndi abwino.
צוית צדק עדתיך ואמונה מאד 138
Maumboni amene munatipatsa ndi olungama; ndi odalirika ndithu.
צמתתני קנאתי כי-שכחו דבריך צרי 139
Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.
צרופה אמרתך מאד ועבדך אהבה 140
Mawu anu ndi woyera kwambiri nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.
צעיר אנכי ונבזה פקדיך לא שכחתי 141
Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka, sindiyiwala malangizo anu.
צדקתך צדק לעולם ותורתך אמת 142
Chilungamo chanu nʼchamuyaya, ndipo malamulo anu nʼchoona.
צר-ומצוק מצאוני מצותיך שעשעי 143
Mavuto ndi masautso zandigwera, koma ndimakondwera ndi malamulo anu.
צדק עדותיך לעולם הבינני ואחיה 144
Umboni wanu ndi wabwino nthawi zonse; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ine ndikhale ndi moyo.
קראתי בכל-לב ענני יהוה חקיך אצרה 145
Ndimayitana ndi mtima wanga wonse; ndiyankheni Inu Yehova, ndipo ndidzamvera zophunzitsa zanu.
קראתיך הושיעני ואשמרה עדתיך 146
Ndikuyitana kwa Inu; pulumutseni ndipo ndidzasunga umboni wanu.
קדמתי בנשף ואשועה לדבריך (לדברך) יחלתי 147
Ndimadzuka tambala asanalire kuti ndipemphe thandizo; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
קדמו עיני אשמרות-- לשיח באמרתך 148
Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku, kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.
קולי שמעה כחסדך יהוה כמשפטך חיני 149
Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.
קרבו רדפי זמה מתורתך רחקו 150
Iwo amene amakonza njira zoyipa andiyandikira, koma ali kutali ndi malamulo anu.
קרוב אתה יהוה וכל-מצותיך אמת 151
Koma Inu Yehova muli pafupi, malamulo anu onse ndi woona.
קדם ידעתי מעדתיך כי לעולם יסדתם 152
Ndinaphunzira kalekale kuchokera mʼmaumboni anu kuti maumboni amene munakhazikitsawo ndi amuyaya.
ראה-עניי וחלצני כי-תורתך לא שכחתי 153
Yangʼanani masautso anga ndipo mundipulumutse, pakuti sindinayiwale malamulo anu.
ריבה ריבי וגאלני לאמרתך חיני 154
Mundiyimirire pa mlandu wanga ndi kundiwombola; sungani moyo wanga molingana ndi lonjezo lanu.
רחוק מרשעים ישועה כי חקיך לא דרשו 155
Chipulumutso chili kutali ndi anthu oyipa, pakuti iwowo safunafuna zophunzitsa zanu.
רחמיך רבים יהוה כמשפטיך חיני 156
Chifundo chanu Yehova nʼchachikulu; sungani moyo wanga molingana ndi malamulo anu.
רבים רדפי וצרי מעדותיך לא נטיתי 157
Adani amene akundizunza ndi ambiri, koma ine sindinatembenuke kuchoka pa umboni wanu.
ראיתי בגדים ואתקוטטה-- אשר אמרתך לא שמרו 158
Ndimawayangʼana monyansidwa anthu opanda chikhulupiriro, popeza samvera mawu anu.
ראה כי-פקודיך אהבתי יהוה כחסדך חיני 159
Onani momwe ndimakondera malangizo anu; sungani moyo wanga, Inu Yehova, molingana ndi chikondi chanu chosanthika.
ראש-דברך אמת ולעולם כל-משפט צדקך 160
Mawu anu onse ndi owona; malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.
שרים רדפוני חנם ומדבריך (ומדברך) פחד לבי 161
Olamulira amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umanjenjemera ndi mawu anu.
שש אנכי על-אמרתך-- כמוצא שלל רב 162
Ine ndimakondwa ndi lonjezo lanu, ngati munthu amene wapeza chuma chambiri.
שקר שנאתי ואתעבה תורתך אהבתי 163
Ndimadana ndi chinyengo, kwambiri ndimanyansidwa nacho, koma ndimakonda malamulo anu.
שבע ביום הללתיך-- על משפטי צדקך 164
Ndimakutamandani kasanu ndi kawiri pa tsiku pakuti malamulo anu ndi olungama.
שלום רב לאהבי תורתך ואין-למו מכשול 165
Amene amakonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, ndipo palibe chimene chingawapunthwitse
שברתי לישועתך יהוה ומצותיך עשיתי 166
Ndikudikira chipulumutso chanu, Inu Yehova, ndipo ndimatsatira malamulo anu.
שמרה נפשי עדתיך ואהבם מאד 167
Ndimamvera umboni wanu pakuti ndimawukonda kwambiri.
שמרתי פקודיך ועדתיך כי כל-דרכי נגדך 168
Ndimamvera malangizo anu ndi umboni wanu, pakuti njira zanga zonse ndi zodziwika pamaso panu.
תקרב רנתי לפניך יהוה כדברך הבינני 169
Kulira kwanga kufike pamaso panu Yehova; patseni nzeru zomvetsa zinthu molingana ndi mawu anu.
תבוא תחנתי לפניך כאמרתך הצילני 170
Kupempha kwanga kufike pamaso panu; pulumutseni molingana ndi lonjezo lanu.
תבענה שפתי תהלה כי תלמדני חקיך 171
Matamando asefukire pa milomo yanga, pakuti Inu mumandiphunzitsa malamulo anu.
תען לשוני אמרתך כי כל-מצותיך צדק 172
Lilime langa liyimbe mawu anu, popeza malamulo anu onse ndi olungama.
תהי-ידך לעזרני כי פקודיך בחרתי 173
Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza pakuti ndasankha malangizo anu.
תאבתי לישועתך יהוה ותורתך שעשעי 174
Ndikufunitsitsa chipulumutso chanu Yehova, ndipo ndimakondwera ndi malamulo anu.
תחי-נפשי ותהללך ומשפטך יעזרני 175
Loleni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni, ndipo malamulo anu andichirikize.
תעיתי-- כשה אבד בקש עבדך כי מצותיך לא שכחתי 176
Ndasochera ngati nkhosa yotayika, funafunani mtumiki wanu, pakuti sindinayiwale malamulo anu.

< תהילים 119 >