< תהילים 118 >

הודו ליהוה כי-טוב כי לעולם חסדו 1
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
יאמר-נא ישראל כי לעולם חסדו 2
Israeli anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”
יאמרו-נא בית-אהרן כי לעולם חסדו 3
Banja la Aaroni linene kuti, “Chikondi chake ndi chosatha.”
יאמרו-נא יראי יהוה כי לעולם חסדו 4
Iwo amene amaopa Yehova anene kuti: “Chikondi chake ndi chosatha.”
מן-המצר קראתי יה ענני במרחב יה 5
Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova, ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
יהוה לי לא אירא מה-יעשה לי אדם 6
Yehova ali nane; sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?
יהוה לי בעזרי ואני אראה בשנאי 7
Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa. Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.
טוב לחסות ביהוה-- מבטח באדם 8
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira munthu.
טוב לחסות ביהוה-- מבטח בנדיבים 9
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira mafumu.
כל-גוים סבבוני בשם יהוה כי אמילם 10
Anthu a mitundu yonse anandizinga, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
סבוני גם-סבבוני בשם יהוה כי אמילם 11
Anandizinga mbali zonse, koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
סבוני כדבורים-- דעכו כאש קוצים בשם יהוה כי אמילם 12
Anandizinga ngati njuchi, koma anatha msanga ngati moto wapaminga; mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
דחה דחיתני לנפל ויהוה עזרני 13
Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa, koma Yehova anandithandiza.
עזי וזמרת יה ויהי-לי לישועה 14
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Iye wakhala chipulumutso changa.
קול רנה וישועה--באהלי צדיקים ימין יהוה עשה חיל 15
Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti: “Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
ימין יהוה רוממה ימין יהוה עשה חיל 16
Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”
לא-אמות כי-אחיה ואספר מעשי יה 17
Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
יסר יסרני יה ולמות לא נתנני 18
Yehova wandilanga koopsa, koma sanandipereke ku imfa.
פתחו-לי שערי-צדק אבא-בם אודה יה 19
Tsekulireni zipata zachilungamo, kuti ndifike kudzayamika Yehova.
זה-השער ליהוה צדיקים יבאו בו 20
Ichi ndicho chipata cha Yehova chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
אודך כי עניתני ותהי-לי לישועה 21
Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha; mwakhala chipulumutso changa.
אבן מאסו הבונים-- היתה לראש פנה 22
Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wasanduka wapangodya;
מאת יהוה היתה זאת היא נפלאת בעינינו 23
Yehova ndiye wachita zimenezi ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
זה-היום עשה יהוה נגילה ונשמחה בו 24
Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga; tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.
אנא יהוה הושיעה נא אנא יהוה הצליחה נא 25
Inu Yehova, tipulumutseni; Yehova, tipambanitseni.
ברוך הבא בשם יהוה ברכנוכם מבית יהוה 26
Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova. Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
אל יהוה--ויאר-לנו אסרו-חג בעבתים--עד קרנות המזבח 27
Yehova ndi Mulungu, ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife. Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu, mpaka ku nyanga za guwa.
אלי אתה ואודך אלהי ארוממך 28
Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.
הודו ליהוה כי-טוב כי לעולם חסדו 29
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

< תהילים 118 >