< תהילים 115 >

לא לנו יהוה לא-לנו כי-לשמך תן כבוד--על-חסדך על-אמתך 1
Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi koma ulemerero ukhale pa dzina lanu, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
למה יאמרו הגוים איה-נא אלהיהם 2
Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti, “Mulungu wawo ali kuti?”
ואלהינו בשמים-- כל אשר-חפץ עשה 3
Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
עצביהם כסף וזהב מעשה ידי אדם 4
Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
פה-להם ולא ידברו עינים להם ולא יראו 5
Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya;
אזנים להם ולא ישמעו אף להם ולא יריחון 6
makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
ידיהם ולא ימישון--רגליהם ולא יהלכו לא-יהגו בגרונם 7
manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
כמוהם יהיו עשיהם-- כל אשר-בטח בהם 8
Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
ישראל בטח ביהוה עזרם ומגנם הוא 9
Inu Aisraeli, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
בית אהרן בטחו ביהוה עזרם ומגנם הוא 10
Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova; Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
יראי יהוה בטחו ביהוה עזרם ומגנם הוא 11
Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
יהוה זכרנו יברך יברך את-בית ישראל יברך את-בית אהרן 12
Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israeli, adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
יברך יראי יהוה-- הקטנים עם-הגדלים 13
adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova; aangʼono ndi aakulu omwe.
יסף יהוה עליכם עליכם ועל בניכם 14
Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu.
ברוכים אתם ליהוה-- עשה שמים וארץ 15
Mudalitsidwe ndi Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
השמים שמים ליהוה והארץ נתן לבני-אדם 16
Kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
לא המתים יהללו-יה ולא כל-ירדי דומה 17
Si anthu akufa amene amatamanda Yehova, amene amatsikira kuli chete;
ואנחנו נברך יה-- מעתה ועד-עולם הללו-יה 18
ndi ife amene timatamanda Yehova, kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Yehova.

< תהילים 115 >