< מִשְׁלֵי 8 >

הלא-חכמה תקרא ותבונה תתן קולה 1
Kodi nzeru sikuyitana? Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
בראש-מרמים עלי-דרך בית נתיבות נצבה 2
Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira, imayima pa mphambano ya misewu.
ליד-שערים לפי-קרת מבוא פתחים תרנה 3
Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda, pa makomo olowera imafuwula kuti,
אליכם אישים אקרא וקולי אל-בני אדם 4
Inu anthu, ndikuyitana inu; ndikuyitanatu anthu onse.
הבינו פתאים ערמה וכסילים הבינו לב 5
Inu amene simudziwa kanthunu khalani ochenjera; inu amene ndi opusa, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.
שמעו כי-נגידים אדבר ומפתח שפתי מישרים 6
Mverani, pakuti ndikukuwuzani zinthu zofunika kwambiri; ndatsekula pakamwa panga ndipo payankhula zolungama.
כי-אמת יהגה חכי ותועבת שפתי רשע 7
Pakamwa panga pamayankhula zoona ndimanyansidwa ndi kuyankhula zoyipa.
בצדק כל-אמרי-פי אין בהם נפתל ועקש 8
Mawu onse a pakamwa panga ndi olungama; mʼmawu angawo mulibe zokhotakhota kapena zopotoka.
כלם נכחים למבין וישרים למצאי דעת 9
Kwa anthu ozindikira, mawu anga onse ndi woona; kwa anthu amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu, mawu angawo ndi okhoza.
קחו-מוסרי ואל-כסף ודעת מחרוץ נבחר 10
Landirani malangizo anga mʼmalo mwa siliva, nzeru zomvetsa zinthu mʼmalo mwa golide wabwino.
כי-טובה חכמה מפנינים וכל-חפצים לא ישוו-בה 11
Paja nzeru ndi yabwino kwambiri kuposa miyala yamtengowapatali, ndipo zonse zimene ungazifune sizingafanane ndi nzeru.
אני-חכמה שכנתי ערמה ודעת מזמות אמצא 12
Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera. Ine ndimadziwa zinthu ndiponso ndimalingalira zinthu bwino.
יראת יהוה שנאת-רע גאה וגאון ודרך רע ופי תהפכות שנאתי 13
Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.
לי-עצה ותושיה אני בינה לי גבורה 14
Ndine mwini uphungu ndi maganizo abwino; ndili ndi nzeru yomvetsa zinthu ndiponso mphamvu.
בי מלכים ימלכו ורזנים יחקקו צדק 15
Ndine amene ndimathandiza mafumu kulamulira. Ndimawathandiza olamulira kukhazikitsa malamulo olungama.
בי שרים ישרו ונדיבים כל-שפטי צדק 16
Ndine amene ndimathandiza akalonga polamula. Ndinenso amene ndimathandiza akuluakulu onse kulamulira bwino dziko.
אני אהביה (אהבי) אהב ומשחרי ימצאנני 17
Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.
עשר-וכבוד אתי הון עתק וצדקה 18
Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika.
טוב פריי מחרוץ ומפז ותבואתי מכסף נבחר 19
Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri.
בארח-צדקה אהלך בתוך נתיבות משפט 20
Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo.
להנחיל אהבי יש ואצרתיהם אמלא 21
Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.
יהוה--קנני ראשית דרכו קדם מפעליו מאז 22
“Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
מעולם נסכתי מראש-- מקדמי-ארץ 23
Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
באין-תהמות חוללתי באין מעינות נכבדי-מים 24
Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
בטרם הרים הטבעו לפני גבעות חוללתי 25
Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
עד-לא עשה ארץ וחוצות וראש עפרות תבל 26
lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
בהכינו שמים שם אני בחקו חוג על-פני תהום 27
Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
באמצו שחקים ממעל בעזוז עינות תהום 28
pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
בשומו לים חקו ומים לא יעברו-פיו בחוקו מוסדי ארץ 29
pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
ואהיה אצלו אמון ואהיה שעשועים יום יום משחקת לפניו בכל-עת 30
Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
משחקת בתבל ארצו ושעשעי את-בני אדם 31
Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
ועתה בנים שמעו-לי ואשרי דרכי ישמרו 32
“Ndiye tsono ana inu, ndimvereni; odala anthu amene amasunga njira zanga.
שמעו מוסר וחכמו ואל-תפרעו 33
Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru; musanyozere mawu anga.
אשרי אדם שמע-לי לשקד על-דלתתי יום יום--לשמר מזוזת פתחי 34
Wodala munthu amene amandimvera, amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku, kudikirira pa chitseko changa.
כי מצאי מצאי (מצא) חיים ויפק רצון מיהוה 35
Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo ndipo Yehova amamukomera mtima.
וחטאי חמס נפשו כל-משנאי אהבו מות 36
Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha; onse amene amandida amakonda imfa.”

< מִשְׁלֵי 8 >