< מִשְׁלֵי 29 >
איש תוכחות מקשה-ערף-- פתע ישבר ואין מרפא | 1 |
Munthu amene amawumitsabe khosi lake atadzudzulidwa kwambiri, adzawonongeka mwadzidzidzi popanda chomuchiritsa.
ברבות צדיקים ישמח העם ובמשל רשע יאנח עם | 2 |
Anthu olungama akamalamulira mʼdziko anthu amakondwa, koma ngati dziko lilamulidwa ndi anthu oyipa mtima anthu amadandaula.
איש-אהב חכמה ישמח אביו ורעה זונות יאבד-הון | 3 |
Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake, koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.
מלך--במשפט יעמיד ארץ ואיש תרומות יהרסנה | 4 |
Mfumu imalimbitsa dziko poweruza mwachilungamo, koma mfumu imene imawumiriza anthu kuti ayipatse mphatso imawononga dziko.
גבר מחליק על-רעהו רשת פורש על-פעמיו | 5 |
Munthu woshashalika mnzake, akudziyalira ukonde mapazi ake.
בפשע איש רע מוקש וצדיק ירון ושמח | 6 |
Munthu woyipa amakodwa ndi machimo ake, koma wochita chilungamo amayimba lokoma.
ידע צדיק דין דלים רשע לא-יבין דעת | 7 |
Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.
אנשי לצון יפיחו קריה וחכמים ישיבו אף | 8 |
Anthu onyoza atha kuwutsa ziwawa mu mzinda, koma anthu anzeru amaletsa ukali.
איש-חכם--נשפט את-איש אויל ורגז ושחק ואין נחת | 9 |
Ngati munthu wanzeru atsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimachita phokoso ndi kumangoseka ndipo sipakhala mtendere.
אנשי דמים ישנאו-תם וישרים יבקשו נפשו | 10 |
Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wangwiro koma anthu olungama amasamalira moyo wake.
כל-רוחו יוציא כסיל וחכם באחור ישבחנה | 11 |
Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.
משל מקשיב על-דבר-שקר-- כל-משרתיו רשעים | 12 |
Ngati wolamulira amvera zabodza, akuluakulu ake onse adzakhala oyipa.
רש ואיש תככים נפגשו-- מאיר עיני שניהם יהוה | 13 |
Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanana pa kuti: Yehova ndiye anawapatsa maso onsewa.
מלך שופט באמת דלים-- כסאו לעד יכון | 14 |
Ngati mfumu iweruza osauka moyenera, mpando wake waufumu udzakhazikika nthawi zonse.
שבט ותוכחת יתן חכמה ונער משלח מביש אמו | 15 |
Ndodo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru koma mwana womulekerera amachititsa amayi ake manyazi.
ברבות רשעים ירבה-פשע וצדיקים במפלתם יראו | 16 |
Oyipa akamalamulira zoyipa zimachuluka, koma anthu olungama adzaona kugwa kwa anthu oyipawo.
יסר בנך ויניחך ויתן מעדנים לנפשך | 17 |
Umulange mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere ndi kusangalatsa mtima wako.
באין חזון יפרע עם ושמר תורה אשרהו | 18 |
Ngati uthenga wochokera kwa Yehova supezeka anthu amangochita zofuna zawo; koma wodala ndi amene amasunga malamulo.
בדברים לא-יוסר עבד כי-יבין ואין מענה | 19 |
Munthu wantchito sangalangizidwe ndi mawu okha basi; ngakhale awamvetse mawuwo sadzatha kuchitapo kanthu.
חזית--איש אץ בדבריו תקוה לכסיל ממנו | 20 |
Ngakhale munthu wa uchitsiru nʼkuti ndiponi popeza chikhulupiriro chilipo kuposa munthu wodziyesa yekha kuti ndi wanzeru poyankhula.
מפנק מנער עבדו ואחריתו יהיה מנון | 21 |
Ngati munthu asasatitsa wantchito wake kuyambira ali mwana, potsirizira adzapeza kuti wantchitoyo wasanduka mlowachuma wake.
איש-אף יגרה מדון ובעל חמה רב-פשע | 22 |
Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano, ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.
גאות אדם תשפילנו ושפל-רוח יתמך כבוד | 23 |
Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.
חולק עם-גנב שונא נפשו אלה ישמע ולא יגיד | 24 |
Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe; amalumbira koma osawulula kanthu.
חרדת אדם יתן מוקש ובוטח ביהוה ישגב | 25 |
Kuopa munthu kudzakhala ngati msampha, koma aliyense amene amadalira Yehova adzatetezedwa.
רבים מבקשים פני-מושל ומיהוה משפט-איש | 26 |
Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima, koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.
תועבת צדיקים איש עול ותועבת רשע ישר-דרך | 27 |
Anthu olungama amanyansidwa ndi anthu achinyengo; koma anthu oyipa amanyansidwa ndi anthu a mtima wowongoka.