< מִשְׁלֵי 25 >
גם-אלה משלי שלמה-- אשר העתיקו אנשי חזקיה מלך-יהודה | 1 |
Iyi ndi miyambo inanso ya Solomoni, imene anthu a Hezekiya mfumu ya ku Yuda analemba.
כבד אלהים הסתר דבר וכבד מלכים חקר דבר | 2 |
Ulemerero wa Mulungu uli pa kubisa zinthu; ulemerero wa mafumu uli pa kufufuza zinthuzo.
שמים לרום וארץ לעמק ולב מלכים אין חקר | 3 |
Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi, ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.
הגו סיגים מכסף ויצא לצרף כלי | 4 |
Chotsa zoyipa mʼsiliva ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.
הגו רשע לפני-מלך ויכון בצדק כסאו | 5 |
Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu; ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.
אל-תתהדר לפני-מלך ובמקום גדלים אל-תעמד | 6 |
Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu, ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;
כי טוב אמר-לך עלה-הנה מהשפילך לפני נדיב--אשר ראו עיניך | 7 |
paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,” kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa. Chimene wachiona ndi maso ako,
אל-תצא לרב מהר פן מה-תעשה באחריתה--בהכלים אתך רעך | 8 |
usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu nanga udzachita chiyani pa mapeto pake ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?
ריבך ריב את-רעך וסוד אחר אל-תגל | 9 |
Kamba mlandu ndi mnansi wako, koma osawulula chinsinsi cha munthu wina
פן-יחסדך שמע ודבתך לא תשוב | 10 |
kuopa kuti wina akamva mawu ako adzakuchititsa manyazi ndipo mbiri yako yoyipa sidzatha.
תפוחי זהב במשכיות כסף-- דבר דבר על-אפניו | 11 |
Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.
נזם זהב וחלי-כתם-- מוכיח חכם על-אזן שמעת | 12 |
Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.
כצנת שלג ביום קציר--ציר נאמן לשלחיו ונפש אדניו ישיב | 13 |
Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola kwa anthu amene amutuma; iye amaziziritsa mtima bwana wake.
נשיאים ורוח וגשם אין-- איש מתהלל במתת-שקר | 14 |
Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.
בארך אפים יפתה קצין ולשון רכה תשבר-גרם | 15 |
Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu, ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.
דבש מצאת אכל דיך פן-תשבענו והקאתו | 16 |
Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira, kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.
הקר רגלך מבית רעך פן-ישבעך ושנאך | 17 |
Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako ukawirikiza kupita, udzadana naye.
מפיץ וחרב וחץ שנון-- איש ענה ברעהו עד שקר | 18 |
Munthu wochitira mnzake umboni wonama, ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
שן רעה ורגל מועדת-- מבטח בוגד ביום צרה | 19 |
Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto, kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.
מעדה-בגד ביום קרה--חמץ על-נתר ושר בשרים על לב-רע | 20 |
Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira kapena kuthira mchere pa chilonda.
אם-רעב שנאך האכלהו לחם ואם-צמא השקהו מים | 21 |
Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.
כי גחלים--אתה חתה על-ראשו ויהוה ישלם-לך | 22 |
Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake, ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.
רוח צפון תחולל גשם ופנים נזעמים לשון סתר | 23 |
Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula, chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.
טוב שבת על-פנת-גג-- מאשת מדונים (מדינים) ובית חבר | 24 |
Nʼkwabwino kukhala pa ngodya ya denga kuposa kukhala mʼnyumba ndi mkazi wolongolola.
מים קרים על-נפש עיפה ושמועה טובה מארץ מרחק | 25 |
Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.
מעין נרפש ומקור משחת-- צדיק מט לפני-רשע | 26 |
Munthu wolungama amene amagonjera munthu woyipa ali ngati kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oyipa.
אכל דבש הרבות לא-טוב וחקר כבדם כבוד | 27 |
Sibwino kudya uchi wambiri, sibwinonso kudzifunira wekha ulemu.
עיר פרוצה אין חומה-- איש אשר אין מעצר לרוחו | 28 |
Munthu amene samatha kudziretsa ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.