< מִשְׁלֵי 15 >
מענה-רך ישיב חמה ודבר-עצב יעלה-אף | 1 |
Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.
לשון חכמים תיטיב דעת ופי כסילים יביע אולת | 2 |
Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.
בכל-מקום עיני יהוה צפות רעים וטובים | 3 |
Maso a Yehova ali ponseponse, amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.
מרפא לשון עץ חיים וסלף בה שבר ברוח | 4 |
Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo, koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.
אויל--ינאץ מוסר אביו ושמר תוכחת יערים | 5 |
Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake, koma wochenjera amasamala chidzudzulo.
בית צדיק חסן רב ובתבואת רשע נעכרת | 6 |
Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.
שפתי חכמים יזרו דעת ולב כסילים לא-כן | 7 |
Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru; koma mitima ya zitsiru sitero.
זבח רשעים תועבת יהוה ותפלת ישרים רצונו | 8 |
Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.
תועבת יהוה דרך רשע ומרדף צדקה יאהב | 9 |
Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.
מוסר רע לעזב ארח שונא תוכחת ימות | 10 |
Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Odana ndi chidzudzulo adzafa.
שאול ואבדון נגד יהוה אף כי-לבות בני-אדם (Sheol ) | 11 |
Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova, nanji mitima ya anthu! (Sheol )
לא יאהב-לץ הוכח לו אל-חכמים לא ילך | 12 |
Wonyoza sakonda kudzudzulidwa; iye sapita kwa anthu anzeru.
לב שמח ייטב פנים ובעצבת-לב רוח נכאה | 13 |
Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe, koma mtima wosweka umawawitsa moyo.
לב נבון יבקש-דעת ופני (ופי) כסילים ירעה אולת | 14 |
Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru, koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.
כל-ימי עני רעים וטוב-לב משתה תמיד | 15 |
Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.
טוב-מעט ביראת יהוה-- מאוצר רב ומהומה בו | 16 |
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova, kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.
טוב ארחת ירק ואהבה-שם-- משור אבוס ושנאה-בו | 17 |
Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi, kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.
איש חמה יגרה מדון וארך אפים ישקיט ריב | 18 |
Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano, koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.
דרך עצל כמשכת חדק וארח ישרים סללה | 19 |
Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga, koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.
בן חכם ישמח-אב וכסיל אדם בוזה אמו | 20 |
Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake, koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.
אולת שמחה לחסר-לב ואיש תבונה יישר-לכת | 21 |
Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.
הפר מחשבות באין סוד וברב יועצים תקום | 22 |
Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka, koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.
שמחה לאיש במענה-פיו ודבר בעתו מה-טוב | 23 |
Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera, ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.
ארח חיים למעלה למשכיל-- למען סור משאול מטה (Sheol ) | 24 |
Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo kuti apewe malo okhala anthu akufa. (Sheol )
בית גאים יסח יהוה ויצב גבול אלמנה | 25 |
Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.
תועבת יהוה מחשבות רע וטהרים אמרי-נעם | 26 |
Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova, koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.
עכר ביתו בוצע בצע ושונא מתנת יחיה | 27 |
Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.
לב צדיק יהגה לענות ופי רשעים יביע רעות | 28 |
Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.
רחוק יהוה מרשעים ותפלת צדיקים ישמע | 29 |
Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.
מאור-עינים ישמח-לב שמועה טובה תדשן-עצם | 30 |
Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.
אזן--שמעת תוכחת חיים בקרב חכמים תלין | 31 |
Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo adzakhala pakati pa anthu anzeru.
פורע מוסר מואס נפשו ושומע תוכחת קונה לב | 32 |
Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha, koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.
יראת יהוה מוסר חכמה ולפני כבוד ענוה | 33 |
Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru, ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.