< מִשְׁלֵי 14 >
חכמות נשים בנתה ביתה ואולת בידיה תהרסנו | 1 |
Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.
הולך בישרו ירא יהוה ונלוז דרכיו בוזהו | 2 |
Amene amayenda molungama amaopa Yehova, koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.
בפי-אויל חטר גאוה ושפתי חכמים תשמורם | 3 |
Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana, koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.
באין אלפים אבוס בר ורב-תבואות בכח שור | 4 |
Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya, koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.
עד אמונים לא יכזב ויפיח כזבים עד שקר | 5 |
Mboni yokhulupirika sinama, koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.
בקש-לץ חכמה ואין ודעת לנבון נקל | 6 |
Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza, koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga.
לך מנגד לאיש כסיל ובל-ידעת שפתי-דעת | 7 |
Khala kutali ndi munthu wopusa chifukwa sudzapeza mawu a nzeru.
חכמת ערום הבין דרכו ואולת כסילים מרמה | 8 |
Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake. Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.
אולים יליץ אשם ובין ישרים רצון | 9 |
Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo, koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.
לב--יודע מרת נפשו ובשמחתו לא-יתערב זר | 10 |
Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake, ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.
בית רשעים ישמד ואהל ישרים יפריח | 11 |
Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka, koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.
יש דרך ישר לפני-איש ואחריתה דרכי-מות | 12 |
Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.
גם-בשחק יכאב-לב ואחריתה שמחה תוגה | 13 |
Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa, ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni.
מדרכיו ישבע סוג לב ומעליו איש טוב | 14 |
Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake, koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake.
פתי יאמין לכל-דבר וערום יבין לאשרו | 15 |
Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.
חכם ירא וסר מרע וכסיל מתעבר ובוטח | 16 |
Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa, koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.
קצר-אפים יעשה אולת ואיש מזמות ישנא | 17 |
Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru, ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.
נחלו פתאים אולת וערומים יכתרו דעת | 18 |
Anthu opusa amalandira uchitsiru, koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.
שחו רעים לפני טובים ורשעים על-שערי צדיק | 19 |
Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino, ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.
גם-לרעהו ישנא רש ואהבי עשיר רבים | 20 |
Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda, koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.
בז-לרעהו חוטא ומחונן עניים (ענוים) אשריו | 21 |
Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.
הלוא-יתעו חרשי רע וחסד ואמת חרשי טוב | 22 |
Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.
בכל-עצב יהיה מותר ודבר-שפתים אך-למחסור | 23 |
Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu, koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.
עטרת חכמים עשרם אולת כסילים אולת | 24 |
Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe, koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.
מציל נפשות עד אמת ויפח כזבים מרמה | 25 |
Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo, koma mboni yabodza imaphetsa.
ביראת יהוה מבטח-עז ולבניו יהיה מחסה | 26 |
Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.
יראת יהוה מקור חיים-- לסור ממקשי מות | 27 |
Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo, kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.
ברב-עם הדרת-מלך ובאפס לאם מחתת רזון | 28 |
Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu, koma popanda anthu kalonga amawonongeka.
ארך אפים רב-תבונה וקצר-רוח מרים אולת | 29 |
Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.
חיי בשרים לב מרפא ורקב עצמות קנאה | 30 |
Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imawoletsa mafupa.
עשק דל חרף עשהו ומכבדו חנן אביון | 31 |
Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.
ברעתו ידחה רשע וחסה במותו צדיק | 32 |
Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe, koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo.
בלב נבון תנוח חכמה ובקרב כסילים תודע | 33 |
Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu, koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.
צדקה תרומם-גוי וחסד לאמים חטאת | 34 |
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
רצון-מלך לעבד משכיל ועברתו תהיה מביש | 35 |
Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru, koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.