< במדבר 4 >

וידבר יהוה אל משה ואל אהרן לאמר 1
Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni:
נשא את ראש בני קהת מתוך בני לוי--למשפחתם לבית אבתם 2
“Werengani Akohati omwe ndi gawo limodzi la Alevi monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo.
מבן שלשים שנה ומעלה ועד בן חמשים שנה--כל בא לצבא לעשות מלאכה באהל מועד 3
Werengani amuna onse amene ali ndi zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu amene amabwera kudzagwira ntchito mu tenti ya msonkhano.
זאת עבדת בני קהת באהל מועד--קדש הקדשים 4
“Ntchito ya Akohati mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kusamalira zinthu zopatulika kwambiri.
ובא אהרן ובניו בנסע המחנה והורדו את פרכת המסך וכסו בה--את ארן העדת 5
Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni.
ונתנו עליו כסוי עור תחש ופרשו בגד כליל תכלת מלמעלה ושמו בדיו 6
Ndipo azikuta bokosilo ndi zikopa za akatumbu ndi kuyala pamwamba pake nsalu ya mtundu wa thambo ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.
ועל שלחן הפנים יפרשו בגד תכלת ונתנו עליו את הקערת ואת הכפת ואת המנקית ואת קשות הנסך ולחם התמיד עליו יהיה 7
“Pa tebulo pamene pamakhala buledi wa ansembe aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo, ndipo aziyikapo mbale, mabeseni, zipande ndi mitsuko yoperekera nsembe yachakumwa. Aziyikaponso buledi wokhala pamenepo nthawi zonse.
ופרשו עליהם בגד תולעת שני וכסו אתו במכסה עור תחש ושמו את בדיו 8
Tsono pamwamba pa izi aziyalapo nsalu yofiira, ndi kuzikuta mʼzikopa za akatumbu ndi kuyika mitengo yonyamulira mʼmalo mwake.
ולקחו בגד תכלת וכסו את מנרת המאור ואת נרתיה ואת מלקחיה ואת מחתתיה ואת כל כלי שמנה אשר ישרתו לה בהם 9
“Azitenga nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira choyikapo nyale, pamodzi ndi nyale zake, zopanira zake, zotengera zake ndi mitsuko yonse yosungiramo mafuta.
ונתנו אתה ואת כל כליה אל מכסה עור תחש ונתנו על המוט 10
Kenaka achikulunge pamodzi ndi zipangizo zake zonse mʼzikopa za akatumbu ndi kuchiyika pa chonyamulira chake.
ועל מזבח הזהב יפרשו בגד תכלת וכסו אתו במכסה עור תחש ושמו את בדיו 11
“Pamwamba pa guwa la golide aziyalapo nsalu ya mtundu wa thambo ndi kukutira ndi zikopa za akatumbu ndi kuyika mʼmalo mwake mitengo yonyamulira.
ולקחו את כל כלי השרת אשר ישרתו בם בקדש ונתנו אל בגד תכלת וכסו אותם במכסה עור תחש ונתנו על המוט 12
“Azitenga zipangizo zonse zogwiritsira ntchito ku malo wopatulika, azizikulunga mʼnsalu ya mtundu wa thambo, azizikuta ndi zikopa za akatumbu ndi kuziyika pa zonyamulira zake.
ודשנו את המזבח ופרשו עליו בגד ארגמן 13
“Azichotsa phulusa la pa guwa lansembe lamkuwa ndi kuyalapo nsalu yapepo pamwamba pake.
ונתנו עליו את כל כליו אשר ישרתו עליו בהם את המחתת את המזלגת ואת היעים ואת המזרקת--כל כלי המזבח ופרשו עליו כסוי עור תחש--ושמו בדיו 14
Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake.
וכלה אהרן ובניו לכסת את הקדש ואת כל כלי הקדש בנסע המחנה ואחרי כן יבאו בני קהת לשאת ולא יגעו אל הקדש ומתו אלה משא בני קהת באהל מועד 15
“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.
ופקדת אלעזר בן אהרן הכהן שמן המאור וקטרת הסמים ומנחת התמיד ושמן המשחה פקדת כל המשכן וכל אשר בו בקדש ובכליו 16
“Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.”
וידבר יהוה אל משה ואל אהרן לאמר 17
Yehova anawuzanso Mose ndi Aaroni kuti,
אל תכריתו את שבט משפחת הקהתי מתוך הלוים 18
“Onetsetsani kuti mabanja a fuko la Kohati asachotsedwe kwa Alevi.
וזאת עשו להם וחיו ולא ימתו בגשתם את קדש הקדשים אהרן ובניו יבאו ושמו אותם איש איש על עבדתו ואל משאו 19
Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula.
ולא יבאו לראות כבלע את הקדש ומתו 20
Koma Akohati asalowe kukaona zinthu zopatulika, ngakhale kanthawi pangʼono, chifukwa akatero adzafa.”
וידבר יהוה אל משה לאמר 21
Yehova anawuza Mose kuti,
נשא את ראש בני גרשון--גם הם לבית אבתם למשפחתם 22
“Werenganso Ageresoni monga mwa mabanja ndi mafuko awo.
מבן שלשים שנה ומעלה עד בן חמשים שנה--תפקד אותם כל הבא לצבא צבא לעבד עבדה באהל מועד 23
Uwerenge amuna onse a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu zakubadwa amene amabwera kudzatumikira ku tenti ya msonkhano.
זאת עבדת משפחת הגרשני--לעבד ולמשא 24
“Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi:
ונשאו את יריעת המשכן ואת אהל מועד מכסהו ומכסה התחש אשר עליו מלמעלה ואת מסך--פתח אהל מועד 25
Azinyamula makatani a ku chihema, tenti ya msonkhano, zokutira zake ndi zokutira kunja za zikopa za akatumbu, makatani a pa khomo la ku tenti ya msonkhano,
ואת קלעי החצר ואת מסך פתח שער החצר אשר על המשכן ועל המזבח סביב ואת מיתריהם ואת כל כלי עבדתם ואת כל אשר יעשה להם ועבדו 26
makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi.
על פי אהרן ובניו תהיה כל עבדת בני הגרשני לכל משאם ולכל עבדתם ופקדתם עלהם במשמרת את כל משאם 27
Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira.
זאת עבדת משפחת בני הגרשני--באהל מועד ומשמרתם--ביד איתמר בן אהרן הכהן 28
Iyi ndiye ntchito ya fuko la Ageresoni ku tenti ya msonkhano. Ntchito zawo zichitike motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.
בני מררי--למשפחתם לבית אבתם תפקד אתם 29
“Werenga Amerari monga mwa mafuko awo ndi mabanja awo.
מבן שלשים שנה ומעלה ועד בן חמשים שנה--תפקדם כל הבא לצבא לעבד את עבדת אהל מועד 30
Werenga amuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu zakubadwa amene akatumikire mu tenti ya msonkhano.
וזאת משמרת משאם לכל עבדתם באהל מועד קרשי המשכן ובריחיו ועמודיו ואדניו 31
Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde,
ועמודי החצר סביב ואדניהם ויתדתם ומיתריהם לכל כליהם ולכל עבדתם ובשמת תפקדו את כלי משמרת משאם 32
ndiponso mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema, zingwe ndi zipangizo zake zonse ndiponso zonse zokhudzana ndi ntchito yake. Uwuze munthu aliyense chomwe ayenera kuchita.
זאת עבדת משפחת בני מררי לכל עבדתם באהל מועד--ביד איתמר בן אהרן הכהן 33
Iyi ndiyo ntchito ya mafuko a Amerari pamene akugwira ntchito ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.”
ויפקד משה ואהרן ונשיאי העדה את בני הקהתי למשפחתם ולבית אבתם 34
Mose, Aaroni ndi atsogoleri a magulu a anthu anawerenga Akohati monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
מבן שלשים שנה ומעלה ועד בן חמשים שנה--כל הבא לצבא לעבדה באהל מועד 35
Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano,
ויהיו פקדיהם למשפחתם--אלפים שבע מאות וחמשים 36
atawawerenga mwa mafuko awo, anali 2,750.
אלה פקודי משפחת הקהתי כל העבד באהל מועד אשר פקד משה ואהרן על פי יהוה ביד משה 37
Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.
ופקודי בני גרשון למשפחותם ולבית אבתם 38
Ageresoni anawerengedwanso monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
מבן שלשים שנה ומעלה ועד בן חמשים שנה--כל הבא לצבא לעבדה באהל מועד 39
Amuna onse a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzagwira ntchito ku tenti ya msonkhano,
ויהיו פקדיהם למשפחתם לבית אבתם--אלפים ושש מאות ושלשים 40
atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 2,630.
אלה פקודי משפחת בני גרשון כל העבד באהל מועד--אשר פקד משה ואהרן על פי יהוה 41
Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.
ופקודי משפחת בני מררי למשפחתם לבית אבתם 42
Amerari anawawerenga monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
מבן שלשים שנה ומעלה ועד בן חמשים שנה--כל הבא לצבא לעבדה באהל מועד 43
Amuna onse kuyambira zaka makumi atatu mpaka makumi asanu amene anabwera kudzatumikira ntchito mu tenti ya msonkhano,
ויהיו פקדיהם למשפחתם--שלשת אלפים ומאתים 44
atawawerenga mwa mafuko ndi mabanja awo, anali 3,200.
אלה פקודי משפחת בני מררי אשר פקד משה ואהרן על פי יהוה ביד משה 45
Ichi ndicho chinali chiwerengero cha mabanja a Amerari. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga momwe Yehova anawalamulira kudzera mwa Mose.
כל הפקדים אשר פקד משה ואהרן ונשיאי ישראל--את הלוים למשפחתם ולבית אבתם 46
Kotero Mose, Aaroni ndi atsogoleri a Israeli anawerenga Alevi onse monga mwa mafuko ndi mabanja awo.
מבן שלשים שנה ומעלה ועד בן חמשים שנה כל הבא לעבד עבדת עבדה ועבדת משא--באהל מועד 47
Aamuna onse a zaka makumi atatu mpaka zaka makumi asanu omwe anabwera kudzagwira ntchito yonyamula zinthu ku tenti ya msonkhano
ויהיו פקדיהם--שמנת אלפים וחמש מאות ושמנים 48
analipo 8,580.
על פי יהוה פקד אותם ביד משה--איש איש על עבדתו ועל משאו ופקדיו אשר צוה יהוה את משה 49
Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose.

< במדבר 4 >