< במדבר 32 >
ומקנה רב היה לבני ראובן ולבני גד--עצום מאד ויראו את ארץ יעזר ואת ארץ גלעד והנה המקום מקום מקנה | 1 |
Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo.
ויבאו בני גד ובני ראובן ויאמרו אל משה ואל אלעזר הכהן ואל נשיאי העדה לאמר | 2 |
Choncho Arubeni ndi Agadi anapita kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa atsogoleri a anthu ndi kunena kuti,
עטרות ודיבן ויעזר ונמרה וחשבון ואלעלה ושבם ונבו ובען | 3 |
“Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni,
הארץ אשר הכה יהוה לפני עדת ישראל--ארץ מקנה הוא ולעבדיך מקנה | 4 |
dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto.
ויאמרו אם מצאנו חן בעיניך--יתן את הארץ הזאת לעבדיך לאחזה אל תעברנו את הירדן | 5 |
Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’”
ויאמר משה לבני גד ולבני ראובן האחיכם יבאו למלחמה ואתם תשבו פה | 6 |
Ndipo Mose anati kwa Agadi ndi Arubeni, “Kodi anthu a mtundu wanu apite ku nkhondo inu mutangokhala kuno?
ולמה תנואון (תניאון) את לב בני ישראל--מעבר אל הארץ אשר נתן להם יהוה | 7 |
Chifukwa chiyani mukufowoketsa Aisraeli kupita mʼdziko limene Yehova wawapatsa?
כה עשו אבתיכם בשלחי אתם מקדש ברנע לראות את הארץ | 8 |
Izi ndi zimene makolo anu anachita pamene ndinawatuma kuchokera ku Kadesi kukaona dzikolo.
ויעלו עד נחל אשכול ויראו את הארץ ויניאו את לב בני ישראל--לבלתי בא אל הארץ אשר נתן להם יהוה | 9 |
Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa.
ויחר אף יהוה ביום ההוא וישבע לאמר | 10 |
Yehova anakwiya tsiku limenelo ndipo analumbira kuti,
אם יראו האנשים העלים ממצרים מבן עשרים שנה ומעלה את האדמה אשר נשבעתי לאברהם ליצחק וליעקב כי לא מלאו אחרי | 11 |
‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
בלתי כלב בן יפנה הקנזי ויהושע בן נון כי מלאו אחרי יהוה | 12 |
Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’
ויחר אף יהוה בישראל וינעם במדבר ארבעים שנה--עד תם כל הדור העשה הרע בעיני יהוה | 13 |
Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha.
והנה קמתם תחת אבתיכם--תרבות אנשים חטאים לספות עוד על חרון אף יהוה--אל ישראל | 14 |
“Ndipo onani tsopano, inu mʼbado wochimwa, mwalowa mʼmalo mwa makolo anu ndipo mwachititsa kuti Yehova akwiyire Israeli kwambiri.
כי תשובן מאחריו ויסף עוד להניחו במדבר ושחתם לכל העם הזה | 15 |
Ngati muleka kumutsata, Iye adzawasiyiranso anthu onsewa mʼchipululu ndipo mudzawonongetsa anthu onsewa.”
ויגשו אליו ויאמרו גדרת צאן נבנה למקננו פה וערים לטפנו | 16 |
Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu.
ואנחנו נחלץ חשים לפני בני ישראל עד אשר אם הביאנם אל מקומם וישב טפנו בערי המבצר מפני ישבי הארץ | 17 |
Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli.
לא נשוב אל בתינו--עד התנחל בני ישראל איש נחלתו | 18 |
Sitidzabwerera ku midzi yathu mpaka Mwisraeli aliyense atalandira cholowa chake.
כי לא ננחל אתם מעבר לירדן והלאה כי באה נחלתנו אלינו מעבר הירדן מזרחה | 19 |
Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.”
ויאמר אליהם משה אם תעשון את הדבר הזה אם תחלצו לפני יהוה למלחמה | 20 |
Tsono Mose anati kwa anthuwo, “Ngati inu mudzachita zimenezi, kutenga zida zankhondo pamaso pa Yehova kuti muchite nkhondo,
ועבר לכם כל חלוץ את הירדן לפני יהוה עד הורישו את איביו מפניו | 21 |
ndipo ngati nonsenu mudzapita ndi zida kuwoloka Yorodani pamaso pa Yehova mpaka atachotsa adani ake pamaso pake,
ונכבשה הארץ לפני יהוה ואחר תשבו--והייתם נקים מיהוה ומישראל והיתה הארץ הזאת לכם לאחזה--לפני יהוה | 22 |
dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.
ואם לא תעשון כן הנה חטאתם ליהוה ודעו חטאתכם אשר תמצא אתכם | 23 |
“Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani.
בנו לכם ערים לטפכם וגדרת לצנאכם והיצא מפיכם תעשו | 24 |
Amangireni akazi ndi ana anu mizinda, mangani makola a ziweto zanu, koma chitani zomwe mwalonjeza.”
ויאמר בני גד ובני ראובן אל משה לאמר עבדיך יעשו כאשר אדני מצוה | 25 |
Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira.
טפנו נשינו מקננו וכל בהמתנו--יהיו שם בערי הגלעד | 26 |
Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi,
ועבדיך יעברו כל חלוץ צבא לפני יהוה--למלחמה כאשר אדני דבר | 27 |
koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.”
ויצו להם משה את אלעזר הכהן ואת יהושע בן נון ואת ראשי אבות המטות לבני ישראל | 28 |
Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli.
ויאמר משה אלהם אם יעברו בני גד ובני ראובן אתכם את הירדן כל חלוץ למלחמה לפני יהוה ונכבשה הארץ לפניכם--ונתתם להם את ארץ הגלעד לאחזה | 29 |
Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo.
ואם לא יעברו חלוצים אתכם--ונאחזו בתככם בארץ כנען | 30 |
Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani.
ויענו בני גד ובני ראובן לאמר את אשר דבר יהוה אל עבדיך כן נעשה | 31 |
Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena.
נחנו נעבר חלוצים לפני יהוה ארץ כנען ואתנו אחזת נחלתנו מעבר לירדן | 32 |
Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.”
ויתן להם משה לבני גד ולבני ראובן ולחצי שבט מנשה בן יוסף את ממלכת סיחן מלך האמרי ואת ממלכת עוג מלך הבשן הארץ לעריה בגבלת--ערי הארץ סביב | 33 |
Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira.
ויבנו בני גד את דיבן ואת עטרת ואת ערער | 34 |
Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri,
ואת עטרת שופן ואת יעזר ויגבהה | 35 |
Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha,
ואת בית נמרה ואת בית הרן ערי מבצר וגדרת צאן | 36 |
Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo.
ובני ראובן בנו את חשבון ואת אלעלא ואת קריתים | 37 |
Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu,
ואת נבו ואת בעל מעון מוסבת שם--ואת שבמה ויקראו בשמת את שמות הערים אשר בנו | 38 |
Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo.
וילכו בני מכיר בן מנשה גלעדה--וילכדה ויורש את האמרי אשר בה | 39 |
Zidzukulu za Makiri mwana wa Manase zinapita ku Giliyadi kulanda mzindawo ndi kuthamangitsira kunja Aamori omwe anali kumeneko.
ויתן משה את הגלעד למכיר בן מנשה וישב בה | 40 |
Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko.
ויאיר בן מנשה הלך וילכד את חותיהם ויקרא אתהן חות יאיר | 41 |
Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi.
ונבח הלך וילכד את קנת ואת בנתיה ויקרא לה נבח בשמו | 42 |
Ndipo Noba analanda Kenati ndi midzi yozungulira ndi kuyitcha Noba, kutengera dzina la iye mwini.