< במדבר 3 >

ואלה תולדת אהרן ומשה ביום דבר יהוה את משה--בהר סיני 1
Iyi ndi mbiri ya banja la Aaroni ndi Mose pa nthawi yomwe Yehova anayankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.
ואלה שמות בני אהרן הבכר נדב ואביהוא אלעזר ואיתמר 2
Mayina a ana aamuna a Aaroni anali Nadabu, woyamba kubadwa, Abihu, Eliezara ndi Itamara.
אלה שמות בני אהרן הכהנים המשחים--אשר מלא ידם לכהן 3
Amenewa ndi mayina a ana aamuna a Aaroni, ansembe odzozedwa omwe anapatulidwa kuti azitumikira ngati ansembe.
וימת נדב ואביהוא לפני יהוה בהקרבם אש זרה לפני יהוה במדבר סיני ובנים לא היו להם ויכהן אלעזר ואיתמר על פני אהרן אביהם 4
Koma Nadabu ndi Abihu, anagwa nafa pamaso pa Yehova pamene ankapereka nsembe ndi moto wachilendo pamaso pa Yehova mʼchipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana aamuna. Choncho Eliezara ndi Itamara ndiwo amene ankatumikira ngati ansembe nthawi imene Aaroni abambo awo anali moyo.
וידבר יהוה אל משה לאמר 5
Yehova anati kwa Mose,
הקרב את מטה לוי והעמדת אתו לפני אהרן הכהן ושרתו אתו 6
“Bweretsa fuko la Levi ndipo ulipereke kwa Aaroni wansembe kuti lizimutumikira.
ושמרו את משמרתו ואת משמרת כל העדה לפני אהל מועד--לעבד את עבדת המשכן 7
Azigwira ntchito yothandiza iyeyo ndi gulu lonse ku tenti ya msonkhano pogwira ntchito ya ku Chihema.
ושמרו את כל כלי אהל מועד ואת משמרת בני ישראל--לעבד את עבדת המשכן 8
Azisamalira zipangizo zonse za mu tenti ya msonkhano, ndipo azigwirira ntchito Aisraeli potumikira mu tenti.
ונתתה את הלוים לאהרן ולבניו נתונם נתונם המה לו מאת בני ישראל 9
Pereka Alevi kwa Aaroni ndi kwa ana ake aamuna. Amenewa ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwa iye kwathunthu.
ואת אהרן ואת בניו תפקד ושמרו את כהנתם והזר הקרב יומת 10
Usankhe Aaroni ndi ana ake aamuna kuti azitumikira pa ntchito ya unsembe. Koma wina aliyense woyandikira malo opatulika aphedwe.”
וידבר יהוה אל משה לאמר 11
Yehova anawuzanso Mose kuti,
ואני הנה לקחתי את הלוים מתוך בני ישראל תחת כל בכור פטר רחם מבני ישראל והיו לי הלוים 12
“Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga,
כי לי כל בכור--ביום הכתי כל בכור בארץ מצרים הקדשתי לי כל בכור בישראל מאדם עד בהמה לי יהיו אני יהוה 13
pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.”
וידבר יהוה אל משה במדבר סיני לאמר 14
Yehova anawuza Mose mʼchipululu cha Sinai kuti,
פקד את בני לוי לבית אבתם למשפחתם כל זכר מבן חדש ומעלה תפקדם 15
“Werenga Alevi monga mwa mabanja awo ndi mafuko awo. Werenga mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kapena kupitirirapo.”
ויפקד אתם משה על פי יהוה כאשר צוה 16
Choncho Mose anawawerenga potsatira zomwe Yehova anamulamulira.
ויהיו אלה בני לוי בשמתם--גרשון וקהת ומררי 17
Mayina a ana aamuna a Levi ndi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
ואלה שמות בני גרשון למשפחתם--לבני ושמעי 18
Mayina a ana a Geresoni potsata mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simei.
ובני קהת למשפחתם--עמרם ויצהר חברון ועזיאל 19
Ana a Kohati potsata mabanja awo ndi awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.
ובני מררי למשפחתם--מחלי ומושי אלה הם משפחת הלוי לבית אבתם 20
Ana a Merari potsata mabanja awo ndi awa: Mali ndi Musi. Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi monga mwa makolo awo.
לגרשון--משפחת הלבני ומשפחת השמעי אלה הם משפחת הגרשני 21
Kwa Geresoni kunali banja la Alibini, banja la Asimei. Amenewa ndiwo anali mabanja a Ageresoni.
פקדיהם במספר כל זכר מבן חדש ומעלה פקדיהם שבעת אלפים וחמש מאות 22
Chiwerengero cha amuna onse amene anawawerenga a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 7,500.
משפחת הגרשני אחרי המשכן יחנו ימה 23
Mabanja a Ageresoni azimanga misasa yawo kumadzulo, kumbuyo kwa Chihema.
ונשיא בית אב לגרשני אליסף בן לאל 24
Mtsogoleri wa mabanja a Ageresoni anali Eliyasafu mwana wa Laeli.
ומשמרת בני גרשון באהל מועד המשכן והאהל מכסהו--ומסך פתח אהל מועד 25
Ntchito imene Ageresoni anapatsidwa ku tenti ya msonkhano inali yosamalira Chihema ndi tenti, pamodzi ndi zophimbira zake, katani ya pa khomo la ku tenti ya msonkhano,
וקלעי החצר ואת מסך פתח החצר אשר על המשכן ועל המזבח סביב ואת מיתריו לכל עבדתו 26
ndi makatani wotchinga bwalo, katani ya pa chipata cholowera ku bwalo lozungulira Chihema ndi guwa lansembe, zingwe ndi zonse zokhudzana ndi ntchito yawo.
ולקהת משפחת העמרמי ומשפחת היצהרי ומשפחת החברני ומשפחת העזיאלי אלה הם משפחת הקהתי 27
Kwa Kohati kunali mabanja a Amramu, Aizihara, Ahebroni ndi Auzieli. Awa ndiye anali mabanja a Akohati.
במספר כל זכר מבן חדש ומעלה--שמנת אלפים ושש מאות שמרי משמרת הקדש 28
Chiwerengero cha amuna onse a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 8,600. Akohati ankagwira ntchito yosamalira malo wopatulika.
משפחת בני קהת יחנו על ירך המשכן תימנה 29
Mabanja a ana a Kohati ankamanga misasa yawo kummwera kwa Chihema.
ונשיא בית אב למשפחת הקהתי אליצפן בן עזיאל 30
Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Kohati anali Elizafani mwana wa Uzieli.
ומשמרתם הארן והשלחן והמנרה והמזבחת וכלי הקדש אשר ישרתו בהם והמסך--וכל עבדתו 31
Iwo ankagwira ntchito yosamalira Bokosi la Chipangano, tebulo, choyikapo nyale, maguwa, zipangizo za kumalo wopatulika zimene ansembe ankagwiritsa ntchito, katani, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito.
ונשיא נשיאי הלוי אלעזר בן אהרן הכהן פקדת שמרי משמרת הקדש 32
Mtsogoleri wamkulu wa Alevi anali Eliezara mwana wa Aaroni wansembe. Iye anasankhidwa kukhala woyangʼanira omwe ankasamalira malo wopatulika.
למררי--משפחת המחלי ומשפחת המושי אלה הם משפחת מררי 33
Kwa Merari kunali banja la Mali ndi banja la Musi. Amenewa ndiye anali mabanja a Amerari.
ופקדיהם במספר כל זכר מבן חדש ומעלה--ששת אלפים ומאתים 34
Chiwerengero cha amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 6,200.
ונשיא בית אב למשפחת מררי צוריאל בן אביחיל על ירך המשכן יחנו צפנה 35
Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Amerari anali Zuriyeli mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga misasa yawo kumpoto kwa Chihema.
ופקדת משמרת בני מררי--קרשי המשכן ובריחיו ועמדיו ואדניו וכל כליו--וכל עבדתו 36
Amerari anapatsidwa ntchito yosamalira mitengo ya chihema, nsichi zake, mizati yake, matsinde ake, ndi zida zake zonse, ndi zonse zomwe ankagwiritsa ntchito,
ועמדי החצר סביב ואדניהם ויתדתם ומיתריהם 37
pamodzi ndi mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema ndi zingwe zake.
והחנים לפני המשכן קדמה לפני אהל מועד מזרחה משה ואהרן ובניו שמרים משמרת המקדש למשמרת בני ישראל והזר הקרב יומת 38
Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa.
כל פקודי הלוים אשר פקד משה ואהרן על פי יהוה--למשפחתם כל זכר מבן חדש ומעלה שנים ועשרים אלף 39
Alevi onse amene Mose ndi Aaroni anawawerenga potsatira lamulo la Yehova monga mwa magulu a mabanja awo, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo anali 22,000.
ויאמר יהוה אל משה פקד כל בכר זכר לבני ישראל מבן חדש ומעלה ושא את מספר שמתם 40
Yehova anawuza Mose kuti, “Werenga ana onse aamuna oyamba kubadwa mu Israeli, omwe ali ndi mwezi umodzi kapena kupitirirapo ndipo ulembe mndandanda wa mayina awo.
ולקחת את הלוים לי אני יהוה תחת כל בכר בבני ישראל ואת בהמת הלוים תחת כל בכור בבהמת בני ישראל 41
Unditengere Alevi onse mʼmalo mwa ana oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso ziweto zazimuna za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa za Aisraeli. Ine ndine Yehova.”
ויפקד משה כאשר צוה יהוה אתו את כל בכור בבני ישראל 42
Choncho Mose anawerenga ana aamuna onse oyamba kubadwa a Aisraeli monga momwe Yehova anamulamulira.
ויהי כל בכור זכר במספר שמת מבן חדש ומעלה--לפקדיהם שנים ועשרים אלף שלשה ושבעים ומאתים 43
Chiwerengero chonse cha ana aamuna oyamba kubadwa kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo chinali 22, 273.
וידבר יהוה אל משה לאמר 44
Ndipo Yehova anawuzanso Mose kuti,
קח את הלוים תחת כל בכור בבני ישראל ואת בהמת הלוים תחת בהמתם והיו לי הלוים אני יהוה 45
“Tenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna oyamba kubadwa onse a Aisraeli, ndiponso zoweta zonse za Alevi mʼmalo mwa zoweta za Aisraeli. Alevi ndi anga. Ine ndine Yehova.
ואת פדויי השלשה והשבעים והמאתים--העדפים על הלוים מבכור בני ישראל 46
Pofuna kuwombola ana aamuna 273 oyamba kubadwa a Aisraeli amene anaposa chiwerengero cha aamuna a fuko la Levi,
ולקחת חמשת חמשת שקלים--לגלגלת בשקל הקדש תקח עשרים גרה השקל 47
utenge masekeli asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale ofanana ndi masekeli a ku malo wopatulika, kumene sekeli imodzi imakwanira magera makumi awiri.
ונתתה הכסף לאהרן ולבניו--פדויי העדפים בהם 48
Ndalama zimenezi uzipereke kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kuti ukhale mtengo woombolera Aisraeli woonjezerawo.”
ויקח משה את כסף הפדיום--מאת העדפים על פדויי הלוים 49
Choncho Mose anatenga ndalama zowombolera zija kuchokera kwa Aisraeli amene chiwerengero chawo chinaposa chiwerengero cha omwe anawomboledwa ndi Alevi.
מאת בכור בני ישראל--לקח את הכסף חמשה וששים ושלש מאות ואלף--בשקל הקדש 50
Anatenga masekeli a siliva okwana 1,365 molingana ndi masekeli a ku malo opatulika, kuchokera kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisraeli.
ויתן משה את כסף הפדים לאהרן ולבניו--על פי יהוה כאשר צוה יהוה את משה 51
Mose anapereka ndalama zowombolera zija kwa Aaroni ndi ana ake aamuna monga mwa mawu amene Yehova analamulira.

< במדבר 3 >