< במדבר 1 >
וידבר יהוה אל משה במדבר סיני באהל מועד באחד לחדש השני בשנה השנית לצאתם מארץ מצרים--לאמר | 1 |
Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,
שאו את ראש כל עדת בני ישראל למשפחתם לבית אבתם--במספר שמות כל זכר לגלגלתם | 2 |
“Werengani Aisraeli onse mʼmafuko awo ndi mʼmabanja awo, lemba dzina la munthu wamwamuna aliyense, mmodzimmodzi.
מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא בישראל--תפקדו אתם לצבאתם אתה ואהרן | 3 |
Iwe ndi Aaroni mwawerenge mwa magulu awo mu Israeli, amuna onse a zaka makumi awiri zakubadwa ndi opitirirapo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali.
ואתכם יהיו איש איש למטה--איש ראש לבית אבתיו הוא | 4 |
Munthu mmodzi wochokera ku fuko lililonse yemwe ndi mtsogoleri wa banja lake, ndiye akuthandizeni pa ntchitoyi.
ואלה שמות האנשים אשר יעמדו אתכם לראובן אליצור בן שדיאור | 5 |
Mayina a anthu amene akuthandizeniwo ndi awa: Elizuri mwana wa Sedeuri, kuchokera ku fuko la Rubeni,
לשמעון שלמיאל בן צורישדי | 6 |
Selumieli mwana wa Zurisadai, kuchokera ku fuko la Simeoni,
Naasoni mwana wa Aminadabu, kuchokera ku fuko la Yuda,
Netanieli mwana wa Zuwara, kuchokera ku fuko la Isakara,
Eliabu mwana wa Heloni, kuchokera ku fuko la Zebuloni,
לבני יוסף--לאפרים אלישמע בן עמיהוד למנשה גמליאל בן פדהצור | 10 |
Mwa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efereimu, Elisama mwana wa Amihudi; kuchokera ku fuko la Manase, Gamalieli mwana wa Pedazuri;
Abidani mwana wa Gideoni, kuchokera ku fuko la Benjamini,
Ahiyezeri mwana wa Amisadai, kuchokera ku fuko la Dani,
Pagieli mwana wa Okirani, kuchokera ku fuko la Aseri,
Eliyasafu mwana wa Deuweli, kuchokera ku fuko la Gadi,
Ahira mwana wa Enani, kuchokera ku fuko la Nafutali.”
אלה קריאי (קרואי) העדה נשיאי מטות אבותם ראשי אלפי ישראל הם | 16 |
Amenewa ndi anthu amene anasankhidwa kuchokera mʼmagulu mwawo, eni mbumba a mafuko a makolo awo. Iwowa anali atsogoleri a mafuko a Israeli.
ויקח משה ואהרן את האנשים האלה אשר נקבו בשמת | 17 |
Mose ndi Aaroni anatenga anthu amene mayina awo anaperekedwa,
ואת כל העדה הקהילו באחד לחדש השני ויתילדו על משפחתם לבית אבתם במספר שמות מבן עשרים שנה ומעלה--לגלגלתם | 18 |
ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, anasonkhanitsa anthu onse pamodzi. Anthuwo anafotokoza za makolo awo mwa mafuko awo ndi mabanja awo. Ndipo mayina a amuna onse amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo analembedwa, mmodzimmodzi
כאשר צוה יהוה את משה ויפקדם במדבר סיני | 19 |
monga momwe Yehova analamulira Mose. Motero iyeyo anawawerenga mʼchipululu cha Sinai:
ויהיו בני ראובן בכר ישראל תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמות לגלגלתם--כל זכר מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא | 20 |
Kuchokera mwa ana a Rubeni, mwana wamwamuna woyamba wa Israeli: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali, anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה ראובן--ששה וארבעים אלף וחמש מאות | 21 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Rubeni chinali 46,500.
לבני שמעון תולדתם למשפחתם לבית אבתם פקדיו במספר שמות לגלגלתם--כל זכר מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא | 22 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Simeoni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo, mmodzimmodzi monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה שמעון--תשעה וחמשים אלף ושלש מאות | 23 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Simeoni chinali 59,300.
לבני גד תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמות מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 24 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Gadi: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה גד--חמשה וארבעים אלף ושש מאות וחמשים | 25 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Gadi chinali 45, 650.
לבני יהודה תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 26 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Yuda: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה יהודה--ארבעה ושבעים אלף ושש מאות | 27 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600.
לבני יששכר תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 28 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Isakara: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה יששכר--ארבעה וחמשים אלף וארבע מאות | 29 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Isakara chinali 54,400.
לבני זבולן תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 30 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Zebuloni: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה זבולן--שבעה וחמשים אלף וארבע מאות | 31 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400.
לבני יוסף לבני אפרים תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 32 |
Kuchokera mwa ana aamuna a Yosefe: Kuchokera mwa zidzukulu za Efereimu: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה אפרים--ארבעים אלף וחמש מאות | 33 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Efereimu chinali 40,500.
לבני מנשה תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמות מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 34 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Manase: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה מנשה--שנים ושלשים אלף ומאתים | 35 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Manase chinali 32,200.
לבני בנימן תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 36 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Benjamini: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה בנימן--חמשה ושלשים אלף וארבע מאות | 37 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400.
לבני דן תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 38 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Dani: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה דן--שנים וששים אלף ושבע מאות | 39 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Dani chinali 62,700.
לבני אשר תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 40 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Aseri: Amuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה אשר--אחד וארבעים אלף וחמש מאות | 41 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Aseri chinali 41,500.
בני נפתלי תולדתם למשפחתם לבית אבתם במספר שמת מבן עשרים שנה ומעלה--כל יצא צבא | 42 |
Kuchokera mwa zidzukulu za Nafutali: Aamuna onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali anawalemba mayina awo monga mwa mbiri ya mafuko awo ndi mabanja awo.
פקדיהם למטה נפתלי--שלשה וחמשים אלף וארבע מאות | 43 |
Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Nafutali chinali 53,400.
אלה הפקדים אשר פקד משה ואהרן ונשיאי ישראל--שנים עשר איש איש אחד לבית אבתיו היו | 44 |
Amenewa ndiwo anthu amene Mose ndi Aaroni anawawerenga mothandizidwa ndi atsogoleri khumi ndi awiri a Israeli, aliyense kuyimira fuko lake.
ויהיו כל פקודי בני ישראל לבית אבתם מבן עשרים שנה ומעלה כל יצא צבא בישראל | 45 |
Aisraeli onse a zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, omwe akanatha kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli anawawerenga monga mwa mabanja awo.
ויהיו כל הפקדים--שש מאות אלף ושלשת אלפים וחמש מאות וחמשים | 46 |
Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 603,550.
והלוים למטה אבתם--לא התפקדו בתוכם | 47 |
Koma mabanja a fuko la Levi okha sanawawerenge pamodzi ndi ena.
וידבר יהוה אל משה לאמר | 48 |
Pakuti Yehova anawuza Mose kuti,
אך את מטה לוי לא תפקד ואת ראשם לא תשא בתוך בני ישראל | 49 |
“Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli.
ואתה הפקד את הלוים על משכן העדת ועל כל כליו ועל כל אשר לו--המה ישאו את המשכן ואת כל כליו והם ישרתהו וסביב למשכן יחנו | 50 |
Koma uyike Aleviwo kuti aziyangʼanira tenti yanga yopatulika, zipangizo zake ndi zonse zili mʼmenemo. Azinyamula tentiyo pamodzi ndi zipangizo zake zonse; azisamalira ndi kumanga misasa mozungulira tentiyo.
ובנסע המשכן יורידו אתו הלוים ובחנת המשכן יקימו אתו הלוים והזר הקרב יומת | 51 |
Pamene akusamutsa tentiyo, Alevi ndiwo aziyitsitsa, akafuna kuyimanganso, Alevi ndiwo aziyimiritsa. Wina aliyense amene adzayandikire tentiyo adzaphedwa.
וחנו בני ישראל איש על מחנהו ואיש על דגלו לצבאתם | 52 |
Aisraeli azimanga matenti awo mʼmagulumagulu, munthu aliyense ku gulu lake pansi pa mbendera yake.
והלוים יחנו סביב למשכן העדת ולא יהיה קצף על עדת בני ישראל ושמרו הלוים את משמרת משכן העדות | 53 |
Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”
ויעשו בני ישראל ככל אשר צוה יהוה את משה--כן עשו | 54 |
Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.