< נחום 1 >

משא נינוה--ספר חזון נחום האלקשי 1
Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.
אל קנוא ונקם יהוה נקם יהוה ובעל חמה נקם יהוה לצריו ונוטר הוא לאיביו 2
Yehova ndi Mulungu wansanje ndiponso wobwezera; Yehova amabwezera ndipo ndi waukali. Yehova amabwezera adani ake ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo.
יהוה ארך אפים וגדול (וגדל) כח ונקה לא ינקה יהוה בסופה ובשערה דרכו וענן אבק רגליו 3
Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.
גוער בים ויבשהו וכל הנהרות החריב אמלל בשן וכרמל ופרח לבנון אמלל 4
Amalamulira nyanja ndipo imawuma; amawumitsa mitsinje yonse. Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota.
הרים רעשו ממנו והגבעות התמגגו ותשא הארץ מפניו ותבל וכל יושבי בה 5
Mapiri amagwedera pamaso pake ndipo zitunda zimasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.
לפני זעמו מי יעמוד ומי יקום בחרון אפו חמתו נתכה כאש והצרים נתצו ממנו 6
Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa? Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa? Ukali wake ukuyaka ngati moto; matanthwe akunyeka pamaso pake.
טוב יהוה למעוז ביום צרה וידע חסי בו 7
Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,
ובשטף עבר כלה יעשה מקומה ואיביו ירדף חשך 8
koma ndi madzi achigumula choopsa Iye adzawononga adani ake (Ninive); adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima.
מה תחשבון אל יהוה--כלה הוא עשה לא תקום פעמים צרה 9
Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova adzachiwononga kotheratu; msautso sudzabweranso kachiwiri.
כי עד סירים סבכים וכסבאם סבואים אכלו--כקש יבש מלא 10
Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo; adzatenthedwa ngati ziputu zowuma.
ממך יצא חשב על יהוה רעה--יעץ בליעל 11
Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa, wofuna kuchitira Yehova chiwembu, amene amapereka uphungu woyipa.
כה אמר יהוה אם שלמים וכן רבים וכן נגוזו ועבר וענתך--לא אענך עוד 12
Yehova akuti, “Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi, kaya iwowo ndi ambiri, koma adzawonongedwa ndi kutheratu. Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda, sindidzakuzunzanso.
ועתה אשבר מטהו מעליך ומוסרתיך אנתק 13
Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako ndipo ndidzadula maunyolo ako.”
וצוה עליך יהוה לא יזרע משמך עוד מבית אלהיך אכרית פסל ומסכה אשים קברך--כי קלות 14
Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti, “Sudzakhala ndi zidzukulu zimene zidzadziwike ndi dzina lako. Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba amene ali mʼnyumba ya milungu yako. Ine ndidzakukumbira manda chifukwa ndiwe woyipitsitsa.”
הנה על ההרים רגלי מבשר משמיע שלום--חגי יהודה חגיך שלמי נדריך כי לא יוסיף עוד לעבור (לעבר) בך בליעל כלה נכרת 15
Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu.

< נחום 1 >