< ויקרא 26 >
לא תעשו לכם אלילם ופסל ומצבה לא תקימו לכם ואבן משכית לא תתנו בארצכם להשתחות עליה כי אני יהוה אלהיכם | 1 |
“‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
את שבתתי תשמרו ומקדשי תיראו אני יהוה | 2 |
“‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova.
אם בחקתי תלכו ואת מצותי תשמרו ועשיתם אתם | 3 |
“‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga,
ונתתי גשמיכם בעתם ונתנה הארץ יבולה ועץ השדה יתן פריו | 4 |
ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake. Nthaka yanu idzabala zokolola zake, ndipo mitengo ya mʼmunda idzabala zipatso zake.
והשיג לכם דיש את בציר ובציר ישיג את זרע ואכלתם לחמכם לשבע וישבתם לבטח בארצכם | 5 |
Mudzakhala mukupuntha tirigu mpaka nthawi yothyola mphesa, ndipo mudzakhala mukuthyola mphesa mpaka nthawi yodzala. Mudzadya chakudya chanu mpaka kukhuta ndipo mudzakhala mʼdziko lanu mwamtendere.
ונתתי שלום בארץ ושכבתם ואין מחריד והשבתי חיה רעה מן הארץ וחרב לא תעבר בארצכם | 6 |
“‘Ndidzabweretsa mtendere mʼdziko lanu, ndipo muzidzagona popanda wokuopsezani. Ndidzachotsa nyama zakuthengo zoopsa mʼdziko mwanu, ndipo mʼdzikomo simudzakhala nkhondo.
ורדפתם את איביכם ונפלו לפניכם לחרב | 7 |
Mudzapirikitsa adani anu, ndipo mudzawagonjetsa ndi lupanga pamaso panu.
ורדפו מכם חמשה מאה ומאה מכם רבבה ירדפו ונפלו איביכם לפניכם לחרב | 8 |
Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.
ופניתי אליכם--והפריתי אתכם והרביתי אתכם והקימתי את בריתי אתכם | 9 |
“‘Ndidzakukumbukirani ndi kukupatsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzasunga pangano langa ndi inu.
ואכלתם ישן נושן וישן מפני חדש תוציאו | 10 |
Mudzakhala mukudyabe chakudya chogonera ndipo mudzachotse chakudyacho mʼnkhokwe kuti mupezemo malo woyika chakudya china chatsopano.
ונתתי משכני בתוככם ולא תגעל נפשי אתכם | 11 |
Ndidzakhala pakati panu, ndipo sindidzayipidwa nanu.
והתהלכתי בתוככם והייתי לכם לאלהים ואתם תהיו לי לעם | 12 |
Ine ndidzayendayenda pakati panu ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Inu mudzakhala anthu anga.
אני יהוה אלהיכם אשר הוצאתי אתכם מארץ מצרים מהית להם עבדים ואשבר מטת עלכם ואולך אתכם קוממיות | 13 |
Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti musakhalenso akapolo a Aigupto. Ndinadula mipiringidzo ya goli lanu ndi kukuthandizani kuti muziyenda momasuka.
ואם לא תשמעו לי ולא תעשו את כל המצות האלה | 14 |
“‘Koma mukadzapanda kundimvera ndi kuphwanya malamulo anga onsewa,
ואם בחקתי תמאסו ואם את משפטי תגעל נפשכם לבלתי עשות את כל מצותי להפרכם את בריתי | 15 |
ndipo ngati mudzanyoza malangizo anga ndi kunyansidwa ndi malamulo anga, ndi kulephera kumvera zonse zimene ndakulamulani, ndi kuswa pangano langa,
אף אני אעשה זאת לכם והפקדתי עליכם בהלה את השחפת ואת הקדחת מכלות עינים ומדיבת נפש וזרעתם לריק זרעכם ואכלהו איביכם | 16 |
Ine ndidzakuchitirani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi monga chifuwa chachikulu chowondetsa ndiponso malungo amene adzawononga maso ndi kufowoketsa moyo wanu. Mudzangovutika kudzala mbewu zanu chifukwa adani anu adzazidya.
ונתתי פני בכם ונגפתם לפני איביכם ורדו בכם שנאיכם ונסתם ואין רדף אתכם | 17 |
Ndidzakufulatirani, kotero kuti adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulirani ndipo inu muzidzagothawa popanda wokupirikitsani.
ואם עד אלה--לא תשמעו לי ויספתי ליסרה אתכם שבע על חטאתיכם | 18 |
“‘Ngati simudzandimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu.
ושברתי את גאון עזכם ונתתי את שמיכם כברזל ואת ארצכם כנחשה | 19 |
Ndidzathyola mphamvu zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale yowuma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuwa.
ותם לריק כחכם ולא תתן ארצכם את יבולה ועץ הארץ לא יתן פריו | 20 |
Mphamvu zanu zidzapita pachabe chifukwa nthaka yanu sidzabala kanthu, ngakhale mitengo yake sidzabala zipatso zake.
ואם תלכו עמי קרי ולא תאבו לשמע לי--ויספתי עליכם מכה שבע כחטאתיכם | 21 |
“‘Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu.
והשלחתי בכם את חית השדה ושכלה אתכם והכריתה את בהמתכם והמעיטה אתכם ונשמו דרכיכם | 22 |
Ndidzabweretsa zirombo zolusa pakati panu, ndipo zidzakulandani ana anu ndi kuwononga ngʼombe zanu. Choncho zidzachepetsa chiwerengero chanu kotero kuti mʼnjira mwanu simudzapita anthu.
ואם באלה--לא תוסרו לי והלכתם עמי קרי | 23 |
“‘Mukadzapanda kutembenukira kwa Ine ngakhale nditakulangani motere, ndi kumachitabe zotsutsana ndi Ine,
והלכתי אף אני עמכם בקרי והכיתי אתכם גם אני שבע על חטאתיכם | 24 |
Ine mwini ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha machimo anu.
והבאתי עליכם חרב נקמת נקם ברית ונאספתם אל עריכם ושלחתי דבר בתוככם ונתתם ביד אויב | 25 |
Ndipo ndidzabweretsa lupanga pa inu ndi kukulangani chifukwa chophwanya pangano langa. Mukadzasonkhana mʼmizinda yanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa adani anu.
בשברי לכם מטה לחם ואפו עשר נשים לחמכם בתנור אחד והשיבו לחמכם במשקל ואכלתם ולא תשבעו | 26 |
Ndikadzachepetsa buledi wanu, akazi khumi adzaphika buledi wawo mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani bulediyo pangʼonopangʼono. Choncho mudzadya koma wosakhuta.
ואם בזאת--לא תשמעו לי והלכתם עמי בקרי | 27 |
“‘Mukadzapanda kundimvera ngakhale nditakulangani motere, ndi kumatsutsanabe ndi Ine,
והלכתי עמכם בחמת קרי ויסרתי אתכם אף אני שבע על חטאתיכם | 28 |
pamenepo ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwini ndidzakulangani mochulukitsa kasanu ndi kawiri chifukwa cha kuchimwa kwanu.
ואכלתם בשר בניכם ובשר בנתיכם תאכלו | 29 |
Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi.
והשמדתי את במתיכם והכרתי את חמניכם ונתתי את פגריכם על פגרי גלוליכם וגעלה נפשי אתכם | 30 |
Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu.
ונתתי את עריכם חרבה והשמותי את מקדשיכם ולא אריח בריח ניחחכם | 31 |
Ndidzasandutsa mizinda yanu kukhala mabwinja ndi kuwononga malo anu wopatulika. Sindidzakondweranso ndi fungo lokoma la zopereka zanu.
והשמתי אני את הארץ ושממו עליה איביכם הישבים בה | 32 |
Ndidzawononga dziko kotero kuti adani anu mʼmenemo adzadabwa.
ואתכם אזרה בגוים והריקתי אחריכם חרב והיתה ארצכם שממה ועריכם יהיו חרבה | 33 |
Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzasolola lupanga langa ndi kukupirikitsani. Dziko lanu lidzawonongedwa, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja.
אז תרצה הארץ את שבתתיה כל ימי השמה ואתם בארץ איביכם אז תשבת הארץ והרצת את שבתתיה | 34 |
Nthawi imeneyo nthaka idzasangalalira kuyipumitsa kwake nthawi yonse imene idzakhala yosalimidwa, pamene inu mudzakhala muli mʼdziko la adani anu. Pa nthawi imeneyo dziko lidzapumula ndi kukondwerera kulipumuza kwake.
כל ימי השמה תשבת את אשר לא שבתה בשבתתיכם בשבתכם עליה | 35 |
Nthawi zonse pamene dzikolo lidzakhala lopanda anthu, nthaka idzapumula. Mpumulo umenewu udzakhala umene nthakayo sinapumulepo pa nthawi zimene inu munkapumula muli mʼdzikomo.
והנשארים בכם--והבאתי מרך בלבבם בארצת איביהם ורדף אתם קול עלה נדף ונסו מנסת חרב ונפלו ואין רדף | 36 |
“‘Kunena za amene adzatsale, ndidzayika mantha mʼmitima mwawo mʼdziko la adani awo kotero kuti adzathawa ngakhale mtswatswa wa tsamba lowuluka ndi mphepo. Adzathawa ngati akuthawa lupanga, ndipo adzagwa pansi ngakhale padzakhale wopanda kuwapirikitsa.
וכשלו איש באחיו כמפני חרב ורדף אין ולא תהיה לכם תקומה לפני איביכם | 37 |
Iwo adzaphunthwitsana ngati akuthawa nkhondo, ngakhale padzakhale popanda wowapirikitsa. Choncho simudzatha kuyima pamaso pa adani anu.
ואבדתם בגוים ואכלה אתכם ארץ איביכם | 38 |
Mudzatheratu pakati pa mitundu ya anthu. Dziko la adani anu lidzakudyani.
והנשארים בכם ימקו בעונם בארצת איביכם ואף בעונת אבתם אתם ימקו | 39 |
Ngakhale iwo amene adzatsale adzatheratu mʼdziko la adani awo chifukwa cha machimo awo ndi machimo a makolo awo.
והתודו את עונם ואת עון אבתם במעלם אשר מעלו בי ואף אשר הלכו עמי בקרי | 40 |
“‘Tsono adzawulula machimo awo ndi machimo a makolo awo, kusakhulupirika kwawo ndi mayendedwe awo otsutsana nane,
אף אני אלך עמם בקרי והבאתי אתם בארץ איביהם או אז יכנע לבבם הערל ואז ירצו את עונם | 41 |
zomwe zinandipangitsa kuwafulatira ndi kuwapereka mʼmanja mwa adani awo. Ndipo mitima yawo yowumayo ikadzadzichepetsa ndi kuvomera kulangidwa chifukwa cha machimo awo,
וזכרתי את בריתי יעקוב ואף את בריתי יצחק ואף את בריתי אברהם אזכר--והארץ אזכר | 42 |
Ine ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo, pangano langa ndi Isake, pangano langa ndi Abrahamu. Ndidzakumbukiranso dzikolo.
והארץ תעזב מהם ותרץ את שבתתיה בהשמה מהם והם ירצו את עונם יען וביען--במשפטי מאסו ואת חקתי געלה נפשם | 43 |
Pakuti adzasiya dziko lawo lopanda anthu, nthaka idzakondwerera zaka zake zoyipumuza pamene iwo kudzakhala kulibe. Koma adzalangidwa chifukwa cha machimo awo popeza anakana malamulo anga ndipo mitima yawo inkayipidwa nawo malangizo anga.
ואף גם זאת בהיותם בארץ איביהם לא מאסתים ולא געלתים לכלתם--להפר בריתי אתם כי אני יהוה אלהיהם | 44 |
Komabe ngakhale adzachite zonsezi ali mʼdziko la adani awo, Ine sindidzawakana kapena kuyipidwa nawo kwakuti nʼkuwawononga kwathunthu ndi kuthetsa pangano langa ndi iwo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo.
וזכרתי להם ברית ראשנים אשר הוצאתי אתם מארץ מצרים לעיני הגוים להיות להם לאלהים--אני יהוה | 45 |
Koma powachitira chifundo, ndidzakumbukira pangano langa ndi makolo awo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mitundu ina ikuona kuti Ine ndikhale Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’”
אלה החקים והמשפטים והתורת אשר נתן יהוה בינו ובין בני ישראל--בהר סיני ביד משה | 46 |
Amenewa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anawayika pakati pa Iye mwini ndi Aisraeli pa Phiri la Sinai kudzera mwa Mose.