< ויקרא 14 >

וידבר יהוה אל משה לאמר 1
Yehova anawuza Mose kuti,
זאת תהיה תורת המצרע ביום טהרתו והובא אל הכהן 2
“Malamulo a munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake ndi awa: Abwere naye kwa wansembe.
ויצא הכהן אל מחוץ למחנה וראה הכהן והנה נרפא נגע הצרעת מן הצרוע 3
Wansembe atuluke kunja kwa msasa ndipo amuonetsetse wodwalayo. Ngati munthu wakhateyo wachira,
וצוה הכהן ולקח למטהר שתי צפרים חיות טהרות ועץ ארז ושני תולעת ואזב 4
wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope.
וצוה הכהן ושחט את הצפור האחת--אל כלי חרש על מים חיים 5
Wansembe alamule anthuwo kuti mbalame imodzi ayiphere mu mʼphika wa dothi pamwamba pa madzi abwino.
את הצפר החיה יקח אתה ואת עץ הארז ואת שני התולעת ואת האזב וטבל אותם ואת הצפר החיה בדם הצפר השחטה על המים החיים 6
Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino.
והזה על המטהר מן הצרעת--שבע פעמים וטהרו ושלח את הצפר החיה על פני השדה 7
Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.
וכבס המטהר את בגדיו וגלח את כל שערו ורחץ במים וטהר ואחר יבוא אל המחנה וישב מחוץ לאהלו שבעת ימים 8
“Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri.
והיה ביום השביעי יגלח את כל שערו את ראשו ואת זקנו ואת גבת עיניו ואת כל שערו יגלח וכבס את בגדיו ורחץ את בשרו במים--וטהר 9
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amete tsitsi lake lonse: amete kumutu, ndevu zake, nsidze zake pamodzi ndi tsitsi lina lonse. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba mʼmadzi, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
וביום השמיני יקח שני כבשים תמימם וכבשה אחת בת שנתה תמימה ושלשה עשרנים סלת מנחה בלולה בשמן ולג אחד שמן 10
“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita.
והעמיד הכהן המטהר את האיש המטהר--ואתם לפני יהוה פתח אהל מועד 11
Wansembe amene ati ayeretse munthu wodwalayo amuyimitse munthuyo ali ndi zopereka zake zonse pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.
ולקח הכהן את הכבש האחד והקריב אתו לאשם--ואת לג השמן והניף אתם תנופה לפני יהוה 12
“Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula.
ושחט את הכבש במקום אשר ישחט את החטאת ואת העלה--במקום הקדש כי כחטאת האשם הוא לכהן--קדש קדשים הוא 13
Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana.
ולקח הכהן מדם האשם ונתן הכהן על תנוך אזן המטהר הימנית ועל בהן ידו הימנית ועל בהן רגלו הימנית 14
Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera kupalamula ndi kuwapaka pa msonga pa khutu lakumanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi chala chachikulu cha ku phazi lakumanja.
ולקח הכהן מלג השמן ויצק על כף הכהן השמאלית 15
Wansembe atengeko mafuta pangʼono, nʼkuwathira mʼdzanja lake lamanzere,
וטבל הכהן את אצבעו הימנית מן השמן אשר על כפו השמאלית והזה מן השמן באצבעו שבע פעמים לפני יהוה 16
aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova.
ומיתר השמן אשר על כפו יתן הכהן על תנוך אזן המטהר הימנית ועל בהן ידו הימנית ועל בהן רגלו הימנית--על דם האשם 17
Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja.
והנותר בשמן אשר על כף הכהן יתן על ראש המטהר וכפר עליו הכהן לפני יהוה 18
Mafuta onse otsala mʼdzanja la wansembe awathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja, ndipo potero adzachita mwambo womupepesera pamaso pa Yehova.
ועשה הכהן את החטאת וכפר על המטהר מטמאתו ואחר ישחט את העלה 19
“Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza
והעלה הכהן את העלה ואת המנחה המזבחה וכפר עליו הכהן וטהר 20
ndi kuyipereka pa guwa, pamodzi ndi nsembe yachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera munthu wodzayeretsedwayo, ndipo adzakhala woyera.
ואם דל הוא ואין ידו משגת--ולקח כבש אחד אשם לתנופה לכפר עליו ועשרון סלת אחד בלול בשמן למנחה--ולג שמן 21
“Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
ושתי תרים או שני בני יונה אשר תשיג ידו והיה אחד חטאת והאחד עלה 22
Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
והביא אתם ביום השמיני לטהרתו--אל הכהן אל פתח אהל מועד לפני יהוה 23
“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe.
ולקח הכהן את כבש האשם ואת לג השמן והניף אתם הכהן תנופה לפני יהוה 24
Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
ושחט את כבש האשם ולקח הכהן מדם האשם ונתן על תנוך אזן המטהר הימנית ועל בהן ידו הימנית ועל בהן רגלו הימנית 25
Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja.
ומן השמן יצק הכהן על כף הכהן השמאלית 26
Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere,
והזה הכהן באצבעו הימנית מן השמן אשר על כפו השמאלית--שבע פעמים לפני יהוה 27
ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova.
ונתן הכהן מן השמן אשר על כפו על תנוך אזן המטהר הימנית ועל בהן ידו הימנית ועל בהן רגלו הימנית--על מקום דם האשם 28
Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula.
והנותר מן השמן אשר על כף הכהן יתן על ראש המטהר--לכפר עליו לפני יהוה 29
Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.
ועשה את האחד מן התרים או מן בני היונה מאשר תשיג ידו 30
Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo,
את אשר תשיג ידו את האחד חטאת ואת האחד עלה--על המנחה וכפר הכהן על המטהר לפני יהוה 31
imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.
זאת תורת אשר בו נגע צרעת אשר לא תשיג ידו בטהרתו 32
“Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.
וידבר יהוה אל משה ואל אהרן לאמר 33
“Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti,
כי תבאו אל ארץ כנען אשר אני נתן לכם לאחזה ונתתי נגע צרעת בבית ארץ אחזתכם 34
Mukakalowa mʼdziko la Kanaani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo Ine ndikakabweretsa ndere zoyanga mʼnyumba mʼdziko limenelo,
ובא אשר לו הבית והגיד לכהן לאמר כנגע נראה לי בבית 35
mwini wake nyumbayo adzapite kwa wansembe ndi kukamuwuza kuti, ‘Ndaona chinthu chooneka ngati ndere mʼnyumba mwanga.’
וצוה הכהן ופנו את הבית בטרם יבא הכהן לראות את הנגע ולא יטמא כל אשר בבית ואחר כן יבא הכהן לראות את הבית 36
Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo.
וראה את הנגע והנה הנגע בקירת הבית שקערורת ירקרקת או אדמדמת ומראיהן שפל מן הקיר 37
Iye aonetsetse nderezo. Tsono akapeza kuti nderezo zili mʼkhoma la nyumba, ndipo ngati zili ndi mawanga obiriwira kapena ofiirira, komanso zikuoneka kuti zalowerera mpaka mʼkati mwa khoma,
ויצא הכהן מן הבית אל פתח הבית והסגיר את הבית שבעת ימים 38
wansembe atuluke mʼnyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo ayitseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri.
ושב הכהן ביום השביעי וראה והנה פשה הנגע בקירת הבית 39
Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri wansembe abwerenso kudzayangʼana mʼnyumbamo. Ngati ndere yafalikira mʼmakoma a nyumbayo,
וצוה הכהן וחלצו את האבנים אשר בהן הנגע והשליכו אתהן אל מחוץ לעיר אל מקום טמא 40
wansembe alamule kuti anthu agumule miyala imene muli nderezo ndipo akayitaye kudzala la kunja kwa mzinda.
ואת הבית יקצע מבית סביב ושפכו את העפר אשר הקצו אל מחוץ לעיר אל מקום טמא 41
Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi.
ולקחו אבנים אחרות והביאו אל תחת האבנים ועפר אחר יקח וטח את הבית 42
Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuyilowetsa mʼmalo mwa miyala imene anagumula ija ndipo atenge dothi latsopano ndi kumata nyumbayo.
ואם ישוב הנגע ופרח בבית אחר חלץ את האבנים ואחרי הקצות את הבית ואחרי הטוח 43
“Ngati ndere iwonekanso mʼnyumbamo atagumula kale miyala ndiponso atayipala kale ndi kuyimatanso,
ובא הכהן וראה והנה פשה הנגע בבית--צרעת ממארת הוא בבית טמא הוא 44
wansembe apite kukayionetsetsenso ndipo ngati nderezo zafalikira mʼnyumbamo, ndiye kuti ndere zimenezo ndi zoopsa. Nyumba imeneyo ndi yodetsedwa.
ונתץ את הבית את אבניו ואת עציו ואת כל עפר הבית והוציא אל מחוץ לעיר אל מקום טמא 45
Agwetse nyumbayo, ndipo miyala yake, matabwa pamodzi ndi dothi lake lonse, zonse akazitaye kudzala lodetsedwa, kunja kwa mzinda.
והבא אל הבית כל ימי הסגיר אתו--יטמא עד הערב 46
“Aliyense amene alowa mʼnyumbamo itatsekedwa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
והשכב בבית יכבס את בגדיו והאכל בבית יכבס את בגדיו 47
Munthu amene wagona mʼnyumbamo kapena kudyeramo ayenera kuchapa zovala zake.
ואם בא יבא הכהן וראה והנה לא פשה הנגע בבית אחרי הטח את הבית--וטהר הכהן את הבית כי נרפא הנגע 48
“Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha.
ולקח לחטא את הבית שתי צפרים ועץ ארז ושני תולעת ואזב 49
Kuti nyumbayo iyeretsedwe, mwini wake atenge mbalame ziwiri, kanthambi kamkungudza, kansalu kofiirira ndi kachitsamba ka hisope.
ושחט את הצפר האחת אל כלי חרש על מים חיים 50
Wansembe aphe mbalame imodzi pamwamba pa madzi abwino mu mʼphika wa dothi.
ולקח את עץ הארז ואת האזב ואת שני התולעת ואת הצפר החיה וטבל אתם בדם הצפר השחוטה ובמים החיים והזה אל הבית שבע פעמים 51
Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri
וחטא את הבית--בדם הצפור ובמים החיים ובצפר החיה ובעץ הארז ובאזב--ובשני התולעת 52
Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira.
ושלח את הצפר החיה אל מחוץ לעיר--אל פני השדה וכפר על הבית וטהר 53
Kenaka ayiwulutsire mbalame yamoyo ija kuthengo, kunja kwa mzinda. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”
זאת התורה לכל נגע הצרעת ולנתק 54
Amenewa ndiwo malamulo a nthenda ya khate, bala lonyerenyetsa,
ולצרעת הבגד ולבית 55
nguwi za pa zovala, ndere za mʼnyumba,
ולשאת ולספחת ולבהרת 56
khate la chithupsa, khate la mʼbuko ndi khate la banga
להורת ביום הטמא וביום הטהר זאת תורת הצרעת 57
kuti mudziwe ngati chinthucho ndi choyeretsedwa kapena chodetsedwa. Amenewa ndiwo malamulo a nthenda zonse za khate.

< ויקרא 14 >