< שופטים 7 >

וישכם ירבעל הוא גדעון וכל העם אשר אתו ויחנו על עין חרד ומחנה מדין היה לו מצפון מגבעת המורה בעמק 1
Yeru-Baala (Gideoni) ndi anthu ake onse anadzuka mʼmamawa nakamanga misasa pambali pa kasupe ku Harodi. Misasa ya Amidiyani inali mʼchigwa kumpoto kwa phiri la More.
ויאמר יהוה אל גדעון רב העם אשר אתך מתתי את מדין בידם פן יתפאר עלי ישראל לאמר ידי הושיעה לי 2
Yehova anati kwa Gideoni, “Anthu uli nawowa andichulukira kwambiri kuti ndigonjetse Amidiyani chifukwa Aisraeli angamadzitukumule pamaso panga ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’
ועתה קרא נא באזני העם לאמר מי ירא וחרד ישב ויצפר מהר הגלעד וישב מן העם עשרים ושנים אלף ועשרת אלפים נשארו 3
Tsono lengeza kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera abwerere kwawo, ndipo achoke kuno ku phiri la Giliyadi.’” Choncho anthu 22,000 anachoka, ndipo anatsalira anthu 10,000.
ויאמר יהוה אל גדעון עוד העם רב הורד אותם אל המים ואצרפנו לך שם והיה אשר אמר אליך זה ילך אתך הוא ילך אתך וכל אשר אמר אליך זה לא ילך עמך הוא לא ילך 4
Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.”
ויורד את העם אל המים ויאמר יהוה אל גדעון כל אשר ילק בלשונו מן המים כאשר ילק הכלב תציג אותו לבד וכל אשר יכרע על ברכיו לשתות 5
Choncho Gideoni anatenga anthuwo ndi kupita nawo ku madzi. Kumeneko Yehova anamuwuza kuti, “Amene amwe madzi mokhathira ndi manja ngati galu uwayike pawokha, ndipo amene amwe atagwada pansi uwayikenso pawokha.”
ויהי מספר המלקקים בידם אל פיהם--שלש מאות איש וכל יתר העם כרעו על ברכיהם לשתות מים 6
Ndipo anthu 300 anamwa mokhathira, pamene ena onse anagwada pansi pakumwa.
ויאמר יהוה אל גדעון בשלש מאות האיש המלקקים אושיע אתכם ונתתי את מדין בידך וכל העם--ילכו איש למקמו 7
Yehova anati kwa Gideoni, “Ndi anthu 300 amene anamwa madzi mokhathira ndi manja awo ndidzakupulumutsani ndipo ndidzapereka Amidiyani mʼmanja mwanu. Koma anthu ena onse apite ku nyumba kwawo.”
ויקחו את צדה העם בידם ואת שופרתיהם ואת כל איש ישראל שלח איש לאהליו ובשלש מאות האיש החזיק ומחנה מדין היה לו מתחת בעמק 8
Choncho analola anthu ena onse kuti apite ku nyumba zawo kupatula anthu 300 osankhika aja. Iwowa anatenga zakudya ndi malipenga a anthuwo. Ndipo misasa ya ankhondo Amidiyani inali kumunsi kwa chigwa.
ויהי בלילה ההוא ויאמר אליו יהוה קום רד במחנה כי נתתיו בידך 9
Usiku umenewo Yehova anati kwa Gideoni, “Dzuka, pita kachite nkhondo ku misasayo, chifukwa ndayipereka mʼmanja mwako.
ואם ירא אתה לרדת--רד אתה ופרה נערך אל המחנה 10
Ngati ukuopa, upite ku msasako ndi Pura wantchito wako,
ושמעת מה ידברו ואחר תחזקנה ידיך וירדת במחנה וירד הוא ופרה נערו אל קצה החמשים אשר במחנה 11
ndipo ukamvere zimene akunena ndipo pambuyo pake udzalimba mtima ndi kupita kukayithira nkhondo misasayo.” Choncho iye ndi wantchito wake Pura anapita kumbali ina ya msasawo kumene kunali ankhondo.
ומדין ועמלק וכל בני קדם נפלים בעמק כארבה לרב ולגמליהם אין מספר כחול שעל שפת הים לרב 12
Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena onse akummawa anadzaza chigwa chonse ngati dzombe. Ngamira zawo zinali zambiri zosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
ויבא גדעון--והנה איש מספר לרעהו חלום ויאמר הנה חלום חלמתי והנה צליל לחם שערים מתהפך במחנה מדין ויבא עד האהל ויכהו ויפל ויהפכהו למעלה ונפל האהל 13
Gideoni atafika anangomva munthu wina akuwuza mnzake maloto ake kuti, “Ine ndinalota nditaona dengu la buledi wa barele likugubuduzika kupita ku misasa ya Amidiyani. Litafika linawomba tenti moti inagwa ndi kuphwasukaphwasuka.”
ויען רעהו ויאמר אין זאת בלתי אם חרב גדעון בן יואש איש ישראל נתן האלהים בידו את מדין ואת כל המחנה 14
Ndipo mnzakeyo anamuyankha kuti, “Iyi ndi nkhondo ya Gideoni mwana wa Yowasi, wa ku Israeli. Mulungu wapereka Amidiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse mʼdzanja mwake.”
ויהי כשמע גדעון את מספר החלום ואת שברו--וישתחו וישב אל מחנה ישראל ויאמר קומו כי נתן יהוה בידכם את מחנה מדין 15
Gideoni atamva za malotowo ndi kumasulira kwake, anapembedza Mulungu. Kenaka anabwerera ku msasa wa Israeli nawawuza kuti, “Dzukani popeza Yehova wapereka msasa wa Midiyani mʼmanja mwanu.”
ויחץ את שלש מאות האיש שלשה ראשים ויתן שופרות ביד כלם וכדים ריקים ולפדים בתוך הכדים 16
Anawagawa anthu 300 aja magulu atatu, nawapatsa malipenga mʼmanja mwawo ndi mbiya zimene mʼkati mwake munali nsakali zoyaka.
ויאמר אליהם ממני תראו וכן תעשו והנה אנכי בא בקצה המחנה והיה כאשר אעשה כן תעשון 17
Anawuza anthuwo kuti, “Muzikayangʼana ine ndi kuchita zimene ndizikachita. Ndikakafika kumalire a msasa, mukachite zomwe ndikachita ine.
ותקעתי בשופר--אנכי וכל אשר אתי ותקעתם בשופרות גם אתם סביבות כל המחנה ואמרתם ליהוה ולגדעון 18
Ndikadzaliza lipenga ndi onse amene ali ndi ine, inunso mukalize malipenga kumbali zonse za misasa yonse ndi kufuwula kuti, ‘Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.’”
ויבא גדעון ומאה איש אשר אתו בקצה המחנה ראש האשמרת התיכונה--אך הקם הקימו את השמרים ויתקעו בשופרות ונפוץ הכדים אשר בידם 19
Choncho Gideoni pamodzi ndi amuna 100 omwe anali nawo anafika ku malire a msasa pakati pa usiku, alonda atangosinthana kumene. Iwo analiza malipenga awo ndi kuphwanya mbiya zimene zinali mʼmanja mwawo.
ויתקעו שלשת הראשים בשופרות וישברו הכדים ויחזיקו ביד שמאולם בלפדים וביד ימינם השופרות לתקוע ויקראו חרב ליהוה ולגדעון 20
Magulu awiri ena aja anayimbanso malipenga ndi kuswa mbiya zawo. Aliyense ananyamula nsakali ya moto ku dzanja lamanzere ndi lipenga ku dzanja lamanja ndipo anafuwula kuti, “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.”
ויעמדו איש תחתיו סביב למחנה וירץ כל המחנה ויריעו ויניסו (וינוסו) 21
Aliyense anayima pa malo pake kuzungulira misasa. Ankhondo a mʼmisasa muja anadzuka nayamba kuthawa akufuwula.
ויתקעו שלש מאות השופרות וישם יהוה את חרב איש ברעהו ובכל המחנה וינס המחנה עד בית השטה צררתה--עד שפת אבל מחולה על טבת 22
Anthu 300 aja ataliza malipenga, Yehova anawasokoneza ankhondo a Midiyani aja motero kuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo anathawira ku Beti-Sita cha ku Zerera mpaka ku malire a Abeli-Mehola pafupi ndi Tabati.
ויצעק איש ישראל מנפתלי ומן אשר ומן כל מנשה וירדפו אחרי מדין 23
Aisraeli a fuko la Nafutali, fuko la Aseri, ndi fuko lonse la Manase anayitanidwa, ndipo iwo anathamangitsa Amidiyaniwo.
ומלאכים שלח גדעון בכל הר אפרים לאמר רדו לקראת מדין ולכדו להם את המים עד בית ברה ואת הירדן ויצעק כל איש אפרים וילכדו את המים עד בית ברה ואת הירדן 24
Gideoni anatumiza amithenga ku dziko lonse la ku mapiri la Efereimu kukanena kuti, “Tsikani mumenyane ndi Amidiyani ndipo mulande madooko awo owolokera mpaka ku Beti-Bara.” Choncho anthu onse a fuko la Efereimu anasonkhana ndipo analanda madooko awo owolokera mpaka ku Betibaala.
וילכדו שני שרי מדין את ערב ואת זאב ויהרגו את עורב בצור עורב ואת זאב הרגו ביקב זאב וירדפו אל מדין וראש ערב וזאב--הביאו אל גדעון מעבר לירדן 25
Iwo anagwiranso atsogoleri awiri a nkhondo a Amidiyani, Orebu ndi Zeebu. Anapha Orebu ku thanthwe la Orebu, koma Zeebu anamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zeebu pothamangitsa Amidiyani. Mitu ya Orebu ndi Zeebu anabwera nayo kwa Gideoni kutsidya kwa Yorodani.

< שופטים 7 >