< שופטים 13 >

ויסיפו בני ישראל לעשות הרע בעיני יהוה ויתנם יהוה ביד פלשתים ארבעים שנה 1
Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, kotero Yehova anawapereka mʼmanja mwa Afilisti kwa zaka makumi anayi.
ויהי איש אחד מצרעה ממשפחת הדני ושמו מנוח ואשתו עקרה ולא ילדה 2
Ku Zora kunali munthu wina dzina lake Manowa, wochokera ku fuko la Dani. Mkazi wake analibe ana popeza anali wosabereka.
וירא מלאך יהוה אל האשה ויאמר אליה הנה נא את עקרה ולא ילדת והרית וילדת בן 3
Mngelo wa Yehova anaonekera mkaziyo ndipo anati, “Ndinu wosabereka ndipo mulibedi mwana, komabe mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna.
ועתה השמרי נא ואל תשתי יין ושכר ואל תאכלי כל טמא 4
Tsono mudzisamale bwino, osamwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa ndiponso musamadye chakudya chilichonse chodetsedwa,
כי הנך הרה וילדת בן ומורה לא יעלה על ראשו--כי נזיר אלהים יהיה הנער מן הבטן והוא יחל להושיע את ישראל--מיד פלשתים 5
chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.”
ותבא האשה ותאמר לאישה לאמר איש האלהים בא אלי ומראהו כמראה מלאך האלהים נורא מאד ולא שאלתיהו אי מזה הוא ואת שמו לא הגיד לי 6
Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake.
ויאמר לי הנך הרה וילדת בן ועתה אל תשתי יין ושכר ואל תאכלי כל טמאה--כי נזיר אלהים יהיה הנער מן הבטן עד יום מותו 7
Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Choncho musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, musamadye chakudya chilichonse choyipitsidwa chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri, wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero mpaka tsiku la kufa kwake.’”
ויעתר מנוח אל יהוה ויאמר בי אדוני--איש האלהים אשר שלחת יבוא נא עוד אלינו ויורנו מה נעשה לנער היולד 8
Kenaka Manowa anapemphera kwa Yehova kuti, “Chonde Ambuye, lolani munthu wa Mulungu amene munamutuma abwerenso kwa ife kuti adzatiphunzitse zochita ndi mwanayo akadzabadwa.”
וישמע האלהים בקול מנוח ויבא מלאך האלהים עוד אל האשה והיא יושבת בשדה ומנוח אישה אין עמה 9
Mulungu anamva pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu anabweranso kwa mkaziyo nthawi imene anali ku munda, koma Manowa mwamuna wake sanali naye.
ותמהר האשה ותרץ ותגד לאישה ותאמר אליו--הנה נראה אלי האיש אשר בא ביום אלי 10
Tsono mkaziyo anathamanga kukawuza mwamuna wake kuti, “Wandionekeranso munthu uja amene anabwera kwa ine tsiku lija.”
ויקם וילך מנוח אחרי אשתו ויבא אל האיש ויאמר לו האתה האיש אשר דברת אל האשה ויאמר אני 11
Choncho Manowa ananyamuka namutsatira mkazi wake. Atafika kwa munthuyo anamufunsa kuti, “Kodi ndinu munayankhula ndi mkazi wanga?” Iye anayankha kuti, “Ndine.”
ויאמר מנוח עתה יבא דבריך מה יהיה משפט הנער ומעשהו 12
Kenaka Manowa anafunsa kuti, “Tiyerekeze kuti mawu anuwa akwaniritsidwadi, ndiye mwanayu azidzakhala bwanji ndipo azidzachita chiyani?”
ויאמר מלאך יהוה אל מנוח מכל אשר אמרתי אל האשה תשמר 13
Ndipo mngelo wa Yehova uja anamuyankha kuti, “Zonse zimene ndinawawuza akazi anuwa asamale ndipo adzazichitedi.
מכל אשר יצא מגפן היין לא תאכל ויין ושכר אל תשת וכל טמאה אל תאכל כל אשר צויתיה תשמר 14
Asadzadye chilichonse chochokera ku mphesa. Asadzamwe vinyo kapena choledzeretsa chilichonse, ngakhale kudya chakudya chilichonse chodetsedwa. Zonse zimene ndinawalamula azisunge bwino.”
ויאמר מנוח אל מלאך יהוה נעצרה נא אותך ונעשה לפניך גדי עזים 15
Manowa anamuwuza mngelo wa Yehova uja kuti, “Chonde dikirani pangʼono, timati tikukonzereni mwana wambuzi.”
ויאמר מלאך יהוה אל מנוח אם תעצרני לא אכל בלחמך ואם תעשה עלה ליהוה תעלנה כי לא ידע מנוח כי מלאך יהוה הוא 16
Mngelo wa Yehova anayankha kuti, “Ngakhale mukundidikiritsa, ine sindidya chakudya chanu. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza iperekeni kwa Yehova.” (Manowa nʼkuti asakudziwa kuti munthuyo anali mngelo wa Mulungu).
ויאמר מנוח אל מלאך יהוה מי שמך כי יבא דבריך (דברך) וכבדנוך 17
Tsono Manowa anapempha mngelo wa Yehova kuti, “Chonde tidziwitseni dzina lanu kuti zikadzachitika zimene mwanenazi ife tidzakulemekezeni?”
ויאמר לו מלאך יהוה למה זה תשאל לשמי--והוא פלאי 18
Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.”
ויקח מנוח את גדי העזים ואת המנחה ויעל על הצור ליהוה ומפלא לעשות ומנוח ואשתו ראים 19
Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona.
ויהי בעלות הלהב מעל המזבח השמימה ויעל מלאך יהוה בלהב המזבח ומנוח ואשתו ראים ויפלו על פניהם ארצה 20
Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi.
ולא יסף עוד מלאך יהוה להראה אל מנוח ואל אשתו אז ידע מנוח כי מלאך יהוה הוא 21
Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.
ויאמר מנוח אל אשתו מות נמות כי אלהים ראינו 22
Iye anawuza mkazi wake kuti, “Ife tifa basi pakuti taona Mulungu!”
ותאמר לו אשתו לו חפץ יהוה להמיתנו לא לקח מידנו עלה ומנחה ולא הראנו את כל אלה וכעת לא השמיענו כזאת 23
Koma mkazi wake anamuyankha kuti, “Yehova akanafuna kutipha sakanayilandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu chachakudya chija, ndipo sakanationetsanso zinthu zonsezi kapena kutiwuza zinthu ngati zimenezi nthawi ino.”
ותלד האשה בן ותקרא את שמו שמשון ויגדל הנער ויברכהו יהוה 24
Motero mkaziyo anabereka mwana wa mwamuna, namutcha dzina lake Samsoni. Iye anakula ndipo Yehova anamudalitsa.
ותחל רוח יהוה לפעמו במחנה דן בין צרעה ובין אשתאל 25
Mzimu wa Yehova unayamba kumulimbikitsa pamene ankakhala ku misasa ya anthu a fuko la Dani, malo amene anali pakati pa Zora ndi Esitaoli.

< שופטים 13 >