< יהושע 17 >
ויהי הגורל למטה מנשה כי הוא בכור יוסף--למכיר בכור מנשה אבי הגלעד כי הוא היה איש מלחמה ויהי לו הגלעד והבשן | 1 |
Gawo lina la dzikolo linapatsidwa kwa mabanja ena a fuko la Manase, mwana woyamba kubadwa wa Yosefe. Makiri anali mwana woyamba kubadwa wa Manase ndiponso kholo la anthu okhala ku Giliyadi. Popeza kuti iye anali munthu wankhondo, analandira Giliyadi ndi Basani.
ויהי לבני מנשה הנותרים למשפחתם--לבני אביעזר ולבני חלק ולבני אשריאל ולבני שכם ולבני חפר ולבני שמידע אלה בני מנשה בן יוסף הזכרים--למשפחתם | 2 |
Mabanja ena otsala a fuko la Manase amene analandira dziko ndi awa: Abiezeri, Heleki, Asirieli, Sekemu, Heferi ndi Semida. Izi ndi zidzukulu zina zazimuna za Manase mwana wa Yosefe ndiponso eni mbumba.
ולצלפחד בן חפר בן גלעד בן מכיר בן מנשה לא היו לו בנים--כי אם בנות ואלה שמות בנתיו--מחלה ונעה חגלה מלכה ותרצה | 3 |
Panali Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri mwana wa Manase. Iyeyu analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha ndipo mayina awo ndi awa: Mahila, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.
ותקרבנה לפני אלעזר הכהן ולפני יהושע בן נון ולפני הנשיאים לאמר יהוה צוה את משה לתת לנו נחלה בתוך אחינו ויתן להם אל פי יהוה נחלה בתוך אחי אביהן | 4 |
Iwo anapita kwa Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri ndipo anati: “Yehova analamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse cholowa chathu.” Choncho iwowo pamodzi ndi abale a abambo awo anawapatsa dera lina la dzikolo kuti likhale monga mwa lamulo la Yehova.
ויפלו חבלי מנשה עשרה--לבד מארץ הגלעד והבשן אשר מעבר לירדן | 5 |
Choncho kuwonjezera pa mayiko a Giliyadi ndi Basani kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Manase analandiranso magawo khumi
כי בנות מנשה נחלו נחלה בתוך בניו וארץ הגלעד היתה לבני מנשה הנותרים | 6 |
chifukwa ana aakazi a fuko la Manase analandira cholowa chawo pakati pa ana aamuna. Dziko la Giliyadi linali dziko la zidzukulu zonse za Manase.
ויהי גבול מנשה מאשר המכמתת אשר על פני שכם והלך הגבול אל הימין אל ישבי עין תפוח | 7 |
Malire a dziko la Manase anayambira ku Aseri, ndipo anakafika ku Mikimetati kummawa kwa Sekemu. Tsono malire anapita kummwera kuloza kwa anthu a ku Eni-Tapuwa.
למנשה היתה ארץ תפוח ותפוח אל גבול מנשה לבני אפרים | 8 |
(Manase anatenga dziko la Tapuwa, koma mzinda wa Tapuwawo, umene unali mʼmalire mwa Manase unali wa fuko la Efereimu).
וירד הגבול נחל קנה נגבה לנחל ערים האלה לאפרים בתוך ערי מנשה וגבול מנשה מצפון לנחל ויהי תצאתיו הימה | 9 |
Ndipo malire ake anapitirira kummwera mpaka ku mtsinje wa ku Kana. Mizinda ya kummwera kwa mtsinjewo inali ya fuko la Efereimu ngakhale kuti inali mʼdziko la Manase. Malire a fuko la Manase anapita kumpoto kwa mtsinje wa Kana ndi kukathera ku Nyanja.
נגבה לאפרים וצפונה למנשה ויהי הים גבולו ובאשר יפגעון מצפון וביששכר ממזרח | 10 |
Dziko la kummwera linali la Efereimu ndipo la kumpoto linali la Manase. Dziko la Manase linafika ku nyanja ndipo linachita malire ndi Aseri, kumpoto ndiponso Isakara, kummawa.
ויהי למנשה ביששכר ובאשר בית שאן ובנותיה ויבלעם ובנותיה ואת ישבי דאר ובנותיה וישבי עין דר ובנותיה וישבי תענך ובנתיה וישבי מגדו ובנותיה--שלשת הנפת | 11 |
Mʼdziko la Isakara ndi Aseri, Manase analinso ndi mizinda ya Beti-Seani ndi Ibuleamu pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. Panalinso Akanaani amene ankakhala ku Dori, Endori, Taanaki ndi Megido pamodzi ndi mizinda yozungulira (wachitatu pa mʼndandandawu ndi Nafati Dori).
ולא יכלו בני מנשה להוריש את הערים האלה ויואל הכנעני לשבת בארץ הזאת | 12 |
Komabe anthu a fuko la Manase sanathe kuwapirikitsa anthu okhala mʼmizinda imeneyi. Choncho Akanaani anakhalabe mʼmizindayi.
ויהי כי חזקו בני ישראל ויתנו את הכנעני למס והורש לא הורישו | 13 |
Ngakhale Aisraeli anali a mphamvu mʼdzikomo, sanapirikitse Akanaani onse koma anangowasandutsa kukhala akapolo.
וידברו בני יוסף את יהושע לאמר מדוע נתתה לי נחלה גורל אחד וחבל אחד ואני עם רב עד אשר עד כה ברכני יהוה | 14 |
Anthu a fuko la Yosefe anati kwa Yoswa, “Chifukwa chiyani mwatipatsa gawo limodzi lokha la dziko kuti likhale cholowa chathu? Ife tilipo anthu ambiri popeza Yehova watidalitsa kwambiri.”
ויאמר אליהם יהושע אם עם רב אתה עלה לך היערה ובראת לך שם בארץ הפרזי והרפאים כי אץ לך הר אפרים | 15 |
Yoswa anayankha kuti, “Ngati muli ambiri ndipo dziko la ku mapiri la Efereimu lakucheperani kwambiri, lowani ku nkhalango mudule mitengo, mudzikonzere malo akuti mukhalemo, mʼdziko la Aperezi ndi Arefai.”
ויאמרו בני יוסף לא ימצא לנו ההר ורכב ברזל בכל הכנעני הישב בארץ העמק לאשר בבית שאן ובנותיה ולאשר בעמק יזרעאל | 16 |
Tsono zidzukulu za Yosefe zinati, “Dziko la ku mapiri ndi losatikwaniradi, komanso Akanaani onse amene akukhala ku chigwa pamodzi ndi amene akukhala ku Beti-Seani ndi madera awo ndiponso amene ali ku chigwa cha Yezireeli ali ndi magaleta azitsulo.”
ויאמר יהושע אל בית יוסף לאפרים ולמנשה לאמר עם רב אתה וכח גדול לך--לא יהיה לך גורל אחד | 17 |
Koma Yoswa anawuza zidzukulu za Yosefe, za fuko la Efereimu ndi za fuko la Manase kuti, “Inu mulipodi ambiri ndiponso amphamvu. Simulandira gawo limodzi lokha,
כי הר יהיה לך כי יער הוא ובראתו והיה לך תצאתיו כי תוריש את הכנעני כי רכב ברזל לו--כי חזק הוא | 18 |
dziko la ku mapiri lidzakhalanso lanu. Ngakhale kuti ndi nkhalango yokhayokha koma inu mudzadula mitengo yake ndipo lidzakhala lanu mpaka kumapeto. Ngakhale kuti Akanaani ali ndi magaleta azitsulo ndiponso kuti iwo ndi amphamvu, koma inu mudzawapirikitsa.”