< יואל 1 >

דבר יהוה אשר היה אל יואל בן פתואל 1
Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.
שמעו זאת הזקנים והאזינו כל יושבי הארץ ההיתה זאת בימיכם ואם בימי אבתיכם 2
Inu akuluakulu, imvani izi; mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko. Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu, kapena mʼnthawi ya makolo anu?
עליה לבניכם ספרו ובניכם לבניהם ובניהם לדור אחר 3
Muwafotokozere ana anu, ndipo ana anuwo afotokozere ana awo, ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.
יתר הגזם אכל הארבה ויתר הארבה אכל הילק ויתר הילק אכל החסיל 4
Chimene dzombe losamera mapiko lasiya dzombe lowuluka ladya; chimene dzombe lowuluka lasiya dzombe lalingʼono ladya; chimene dzombe lalingʼono lasiya chilimamine wadya.
הקיצו שכורים ובכו והיללו כל שתי יין על עסיס כי נכרת מפיכם 5
Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire! Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo; lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano, pakuti wachotsedwa pakamwa panu.
כי גוי עלה על ארצי עצום ואין מספר שניו שני אריה ומתלעות לביא לו 6
Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa, wamphamvu ndi wosawerengeka; uli ndi mano a mkango, zibwano za mkango waukazi.
שם גפני לשמה ותאנתי לקצפה חשף חשפה והשליך הלבינו שריגיה 7
Wawononga mphesa zanga ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu. Wakungunula makungwa ake ndi kuwataya, kusiya nthambi zake zili mbee.
אלי כבתולה חגרת שק על בעל נעוריה 8
Lirani ngati namwali wovala chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.
הכרת מנחה ונסך מבית יהוה אבלו הכהנים משרתי יהוה 9
Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova. Ansembe akulira, amene amatumikira pamaso pa Yehova.
שדד שדה אבלה אדמה כי שדד דגן הוביש תירוש אמלל יצהר 10
Minda yaguga, nthaka yauma; tirigu wawonongeka, vinyo watsopano watha, mitengo ya mafuta yauma.
הבישו אכרים הילילו כרמים על חטה ועל שערה כי אבד קציר שדה 11
Khalani ndi nkhawa, inu alimi, lirani mofuwula inu alimi a mphesa; imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele, pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.
הגפן הובישה והתאנה אמללה רמון גם תמר ותפוח כל עצי השדה יבשו--כי הביש ששון מן בני אדם 12
Mpesa wauma ndipo mtengo wamkuyu wafota; makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi, mitengo yonse ya mʼmunda yauma. Ndithudi chimwemwe cha anthu chatheratu.
חגרו וספדו הכהנים הילילו משרתי מזבח--באו לינו בשקים משרתי אלהי כי נמנע מבית אלהיכם מנחה ונסך 13
Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani; lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe. Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse, inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga; pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
קדשו צום קראו עצרה--אספו זקנים כל ישבי הארץ בית יהוה אלהיכם וזעקו אל יהוה 14
Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya, itanani msonkhano wopatulika. Sonkhanitsani akuluakulu ndi anthu onse okhala mʼdziko ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova.
אהה ליום כי קרוב יום יהוה וכשד משדי יבוא 15
Kalanga ine tsikulo! Pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
הלוא נגד עינינו אכל נכרת מבית אלהינו שמחה וגיל 16
Kodi chakudya chathu sichachotsedwa ife tikuona? Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?
עבשו פרדות תחת מגרפתיהם--נשמו אצרות נהרסו ממגרות כי הביש דגן 17
Mbewu zikunyala poti pansi ndi powuma. Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka; nkhokwe zapasuka popeza tirigu wauma.
מה נאנחה בהמה נבכו עדרי בקר--כי אין מרעה להם גם עדרי הצאן נאשמו 18
Taonani mmene zikulirira ziweto; ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa zilibe msipu; ngakhalenso nkhosa zikusauka.
אליך יהוה אקרא כי אש אכלה נאות מדבר ולהבה להטה כל עצי השדה 19
Kwa Inu Yehova ndilirira, pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo, malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.
גם בהמות שדה תערוג אליך כי יבשו אפיקי מים ואש אכלה נאות המדבר 20
Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu; timitsinje tonse taphwa ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.

< יואל 1 >