< יואל 2 >
תקעו שופר בציון והריעו בהר קדשי--ירגזו כל ישבי הארץ כי בא יום יהוה כי קרוב | 1 |
Lizani lipenga mu Ziyoni. Chenjezani pa phiri langa loyera. Onse okhala mʼdziko anjenjemere, pakuti tsiku la Yehova likubwera, layandikira;
יום חשך ואפלה יום ענן וערפל כשחר פרש על ההרים עם רב ועצום--כמהו לא נהיה מן העולם ואחריו לא יוסף עד שני דור ודור | 2 |
tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani. Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri, gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera, gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
לפניו אכלה אש ואחריו תלהט להבה כגן עדן הארץ לפניו ואחריו מדבר שממה וגם פליטה לא היתה לו | 3 |
Patsogolo pawo moto ukupsereza, kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu. Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni, kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu, kulibe kanthu kotsalapo.
כמראה סוסים מראהו וכפרשים כן ירוצון | 4 |
Maonekedwe awo ali ngati akavalo; akuthamanga ngati akavalo ankhondo.
כקול מרכבות על ראשי ההרים ירקדון--כקול להב אש אכלה קש כעם עצום ערוך מלחמה | 5 |
Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso ngati la magaleta, ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu, ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.
מפניו יחילו עמים כל פנים קבצו פארור | 6 |
Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima; nkhope iliyonse imagwa.
כגבורים ירצון כאנשי מלחמה יעלו חומה ואיש בדרכיו ילכון ולא יעבטון ארחותם | 7 |
Amathamanga ngati ankhondo; amakwera makoma ngati asilikali. Onse amayenda pa mizere, osaphonya njira yawo.
ואיש אחיו לא ידחקון גבר במסלתו ילכון ובעד השלח יפלו לא יבצעו | 8 |
Iwo sakankhanakankhana, aliyense amayenda molunjika. Amadutsa malo otchingidwa popanda kumwazikana.
בעיר ישקו בחומה ירצון--בבתים יעלו בעד החלונים יבאו כגנב | 9 |
Amakhamukira mu mzinda, amathamanga mʼmbali mwa khoma. Amakwera nyumba ndi kulowamo; amalowera pa zenera ngati mbala.
לפניו רגזה ארץ רעשו שמים שמש וירח קדרו וכוכבים אספו נגהם | 10 |
Patsogolo pawo dziko limagwedezeka, thambo limanjenjemera, dzuwa ndi mwezi zimachita mdima, ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.
ויהוה נתן קולו לפני חילו--כי רב מאד מחנהו כי עצום עשה דברו כי גדול יום יהוה ונורא מאד ומי יכילנו | 11 |
Yehova amabangula patsogolo pawo, gulu lake lankhondo ndi losawerengeka, ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake. Tsiku la Yehova ndi lalikulu; ndi loopsa. Ndani adzapirira pa tsikulo?
וגם עתה נאם יהוה שבו עדי בכל לבבכם ובצום ובבכי ובמספד | 12 |
“Ngakhale tsopano, bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.
וקרעו לבבכם ואל בגדיכם ושובו אל יהוה אלהיכם כי חנון ורחום הוא--ארך אפים ורב חסד ונחם על הרעה | 13 |
Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
מי יודע ישוב ונחם והשאיר אחריו ברכה--מנחה ונסך ליהוה אלהיכם | 14 |
Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni, nʼkutisiyira madalitso, a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa kwa Yehova Mulungu wanu.
תקעו שופר בציון קדשו צום קראו עצרה | 15 |
Lizani lipenga mu Ziyoni, lengezani tsiku losala zakudya, itanitsani msonkhano wopatulika.
אספו עם קדשו קהל קבצו זקנים--אספו עוללים וינקי שדים יצא חתן מחדרו וכלה מחפתה | 16 |
Sonkhanitsani anthu pamodzi, muwawuze kuti adziyeretse; sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Mkwati atuluke mʼchipinda chake, mkwatibwi atuluke mokhala mwake.
בין האולם ולמזבח יבכו הכהנים משרתי יהוה ויאמרו חוסה יהוה על עמך ואל תתן נחלתך לחרפה למשל בם גוים--למה יאמרו בעמים איה אלהיהם | 17 |
Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova, alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova. Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka, kuti anthu a mitundu ina awalamulire. Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti, ‘Ali kuti Mulungu wawo?’”
ויקנא יהוה לארצו ויחמל על עמו | 18 |
Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake ndi kuchitira chisoni anthu ake.
ויען יהוה ויאמר לעמו הנני שלח לכם את הדגן והתירוש והיצהר ושבעתם אתו ולא אתן אתכם עוד חרפה בגוים | 19 |
Yehova adzawayankha kuti, “Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta ndipo mudzakhuta ndithu; sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo kwa anthu a mitundu ina.
ואת הצפוני ארחיק מעליכם והדחתיו אל ארץ ציה ושממה--את פניו אל הים הקדמני וספו אל הים האחרון ועלה באשו ותעל צחנתו--כי הגדיל לעשות | 20 |
“Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu, kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu, gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo. Ndipo mitembo yawo idzawola, fungo lake lidzamveka.” Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
אל תיראי אדמה גילי ושמחי כי הגדיל יהוה לעשות | 21 |
Iwe dziko usachite mantha; sangalala ndipo kondwera. Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
אל תיראו בהמות שדי כי דשאו נאות מדבר כי עץ נשא פריו תאנה וגפן נתנו חילם | 22 |
Inu nyama zakuthengo, musachite mantha, pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira. Mitengo ikubala zipatso zake; mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.
ובני ציון גילו ושמחו ביהוה אלהיכם כי נתן לכם את המורה לצדקה ויורד לכם גשם מורה ומלקוש--בראשון | 23 |
Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani, kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu, pakuti wakupatsani mvula yoyambirira mwachilungamo chake. Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka, mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
ומלאו הגרנות בר והשיקו היקבים תירוש ויצהר | 24 |
Pa malo opunthira padzaza tirigu; mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.
ושלמתי לכם את השנים אשר אכל הארבה הילק והחסיל והגזם חילי הגדול אשר שלחתי בכם | 25 |
“Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe, dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono, dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka; gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
ואכלתם אכול ושבוע והללתם את שם יהוה אלהיכם אשר עשה עמכם להפליא ולא יבשו עמי לעולם | 26 |
Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa; ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
וידעתם כי בקרב ישראל אני ואני יהוה אלהיכם ואין עוד ולא יבשו עמי לעולם | 27 |
Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli, kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndi kuti palibenso wina; ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
והיה אחרי כן אשפוך את רוחי על כל בשר ונבאו בניכם ובנותיכם זקניכם חלמות יחלמון--בחוריכם חזינות יראו | 28 |
“Ndipo patapita nthawi, ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera, nkhalamba zanu zidzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya.
וגם על העבדים ועל השפחות בימים ההמה אשפוך את רוחי | 29 |
Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.
ונתתי מופתים בשמים ובארץ דם ואש ותימרות עשן | 30 |
Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga ndi pa dziko lapansi, ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
השמש יהפך לחשך והירח לדם--לפני בוא יום יהוה הגדול והנורא | 31 |
Dzuwa lidzadetsedwa ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye.
והיה כל אשר יקרא בשם יהוה--ימלט כי בהר ציון ובירושלם תהיה פליטה כאשר אמר יהוה ובשרידים אשר יהוה קרא | 32 |
Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka; pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu, monga Yehova wanenera, pakati pa otsala amene Yehova wawayitana.