< איוב 9 >

ויען איוב ויאמר 1
Ndipo Yobu anayankha kuti,
אמנם ידעתי כי-כן ומה-יצדק אנוש עם-אל 2
“Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona. Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
אם-יחפץ לריב עמו-- לא-יעננו אחת מני-אלף 3
Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye, Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe.
חכם לבב ואמיץ כח-- מי-הקשה אליו וישלם 4
Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka. Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka?
המעתיק הרים ולא ידעו-- אשר הפכם באפו 5
Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa, ndipo amawagubuduza ali wokwiya.
המרגיז ארץ ממקומה ועמודיה יתפלצון 6
Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake ndipo amanjenjemeretsa mizati yake.
האמר לחרס ולא יזרח ובעד כוכבים יחתם 7
Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala; Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.
נטה שמים לבדו ודורך על-במתי ים 8
Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja.
עשה-עש כסיל וכימה וחדרי תמן 9
Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana, nsangwe ndi kumpotosimpita.
עשה גדלות עד-אין חקר ונפלאות עד-אין מספר 10
Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingawerengeke.
הן יעבר עלי ולא אראה ויחלף ולא-אבין לו 11
Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona; akadutsa, sindingathe kumuzindikira.
הן יחתף מי ישיבנו מי-יאמר אליו מה-תעשה 12
Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa? Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’
אלוה לא-ישיב אפו תחתו שחחו עזרי רהב 13
Mulungu sabweza mkwiyo wake; ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake.
אף כי-אנכי אעננו אבחרה דברי עמו 14
“Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji? Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye?
אשר אם-צדקתי לא אענה למשפטי אתחנן 15
Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe; ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga.
אם-קראתי ויענני-- לא-אאמין כי-יאזין קולי 16
Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera, sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo.
אשר-בשערה ישופני והרבה פצעי חנם 17
Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho, ndipo akanandipweteka popanda chifukwa.
לא-יתנני השב רוחי כי ישבעני ממררים 18
Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso koma akanandichulukitsira zowawa.
אם-לכח אמיץ הנה ואם-למשפט מי יועידני 19
Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi! Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu?
אם-אצדק פי ירשיעני תם-אני ויעקשני 20
Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa; ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa.
תם-אני לא-אדע נפשי אמאס חיי 21
“Ngakhale ine ndili wosalakwa, sindidziyenereza ndekha; moyo wanga ndimawupeputsa.
אחת היא על-כן אמרתי--תם ורשע הוא מכלה 22
Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’
אם-שוט ימית פתאם-- למסת נקים ילעג 23
Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi, Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo.
ארץ נתנה ביד-רשע-- פני-שפטיה יכסה אם-לא אפוא מי-הוא 24
Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa Iye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo, nanga ndani?
וימי קלו מני-רץ ברחו לא-ראו טובה 25
“Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro; masikuwo amapita ine osaonapo zabwino.
חלפו עם-אניות אבה כנשר יטוש עלי-אכל 26
Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja, ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye.
אם-אמרי אשכחה שיחי אעזבה פני ואבליגה 27
Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga, ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’
יגרתי כל-עצבתי ידעתי כי-לא תנקני 28
ndikuopabe mavuto anga onse, popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa.
אנכי ארשע למה-זה הבל איגע 29
Popeza ndapezeka kale wolakwa ndivutikirenji popanda phindu?
אם-התרחצתי במו- (במי-) שלג והזכותי בבר כפי 30
Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri ndi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo,
אז בשחת תטבלני ותעבוני שלמותי 31
mutha kundiponyabe pa dzala, kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa.
כי-לא-איש כמוני אעננו נבוא יחדו במשפט 32
“Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha, sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu.
לא יש-בינינו מוכיח-- ישת ידו על-שנינו 33
Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu, kuti atibweretse ife tonse pamodzi,
יסר מעלי שבטו ואמתו אל-תבעתני 34
munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine kuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha!
אדברה ולא איראנו כי לא-כן אנכי עמדי 35
Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo, koma monga zililimu, sindingathe.

< איוב 9 >