< איוב 36 >

ויסף אליהוא ויאמר 1
Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:
כתר-לי זעיר ואחוך כי עוד לאלוה מלים 2
“Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.
אשא דעי למרחוק ולפעלי אתן-צדק 3
Nzeru zanga ndimazitenga kutali; ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.
כי-אמנם לא-שקר מלי תמים דעות עמך 4
Ndithudi mawu anga si abodza; wanzeru zangwiro ali ndi inu.
הן-אל כביר ולא ימאס כביר כח לב 5
“Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu; Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.
לא-יחיה רשע ומשפט עניים יתן 6
Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.
לא-יגרע מצדיק עיניו ואת-מלכים לכסא וישיבם לנצח ויגבהו 7
Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama; amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.
ואם-אסורים בזקים ילכדון בחבלי-עני 8
Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo, ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,
ויגד להם פעלם ופשעיהם כי יתגברו 9
Iye amawafotokozera zomwe anachita, kuti iwo anachimwa modzikuza.
ויגל אזנם למוסר ויאמר כי-ישובון מאון 10
Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.
אם-ישמעו ויעבדו יכלו ימיהם בטוב ושניהם בנעימים 11
Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira, adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere, adzatsiriza zaka zawo mosangalala.
ואם-לא ישמעו בשלח יעברו ויגועו בבלי-דעת 12
Koma ngati samvera, adzaphedwa ndi lupanga ndipo adzafa osadziwa kanthu.
וחנפי-לב ישימו אף לא ישועו כי אסרם 13
“Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo; akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.
תמת בנער נפשם וחיתם בקדשים 14
Amafa akanali achinyamata, pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.
יחלץ עני בעניו ויגל בלחץ אזנם 15
Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo; Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.
ואף הסיתך מפי-צר-- רחב לא-מוצק תחתיה ונחת שלחנך מלא דשן 16
“Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso, kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani, kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.
ודין-רשע מלאת דין ומשפט יתמכו 17
Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu; chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani.
כי-חמה פן-יסיתך בספק ורב-כפר אל-יטך 18
Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma; musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni.
היערך שועך לא בצר וכל מאמצי-כח 19
Kodi chuma chanu kapena mphamvu zanu zonse zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso?
אל-תשאף הלילה-- לעלות עמים תחתם 20
Musalakalake kuti usiku ubwere, pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka.
השמר אל-תפן אל-און כי-על-זה בחרת מעני 21
Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu.
הן-אל ישגיב בכחו מי כמהו מורה 22
“Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?
מי-פקד עליו דרכו ומי-אמר פעלת עולה 23
Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite, kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’
זכר כי-תשגיא פעלו-- אשר שררו אנשים 24
Kumbukirani kutamanda ntchito zake zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.
כל-אדם חזו-בו אנוש יביט מרחוק 25
Anthu onse amaziona ntchitozo; anthuwo amaziona ali kutali.
הן-אל שגיא ולא נדע מספר שניו ולא-חקר 26
Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe! Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika.
כי יגרע נטפי-מים יזקו מטר לאדו 27
“Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo, timene timasungunuka nʼkukhala mvula;
אשר-יזלו שחקים ירעפו עלי אדם רב 28
mitambo imagwetsa mvulayo ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira.
אף אם-יבין מפרשי-עב תשאות סכתו 29
Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera, momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake?
הן-פרש עליו אורו ושרשי הים כסה 30
Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja.
כי-בם ידין עמים יתן-אכל למכביר 31
Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu ndi kuwapatsa chakudya chochuluka.
על-כפים כסה-אור ויצו עליה במפגיע 32
Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani, ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna.
יגיד עליו רעו מקנה אף על-עולה 33
Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho; ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.

< איוב 36 >