< איוב 28 >

כי יש לכסף מוצא ומקום לזהב יזקו 1
Pali mgodi wa siliva ndiponso malo oyengerapo golide.
ברזל מעפר יקח ואבן יצוק נחושה 2
Chitsulo amachikumba pansi, ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa.
קץ שם לחשך ולכל-תכלית הוא חוקר אבן אפל וצלמות 3
Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale, amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo, kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani.
פרץ נחל מעם-גר--הנשכחים מני-רגל דלו מאנוש נעו 4
Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu, kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko; iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
ארץ--ממנה יצא-לחם ותחתיה נהפך כמו-אש 5
Nthaka, imene imatulutsa zakudya, kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto;
מקום-ספיר אבניה ועפרת זהב לו 6
miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake, ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide.
נתיב לא-ידעו עיט ולא שזפתו עין איה 7
Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi, palibe kamtema amene anayiona.
לא-הדריכוהו בני-שחץ לא-עדה עליו שחל 8
Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo, ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo.
בחלמיש שלח ידו הפך משרש הרים 9
Munthu amaphwanya matanthwe olimba, ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde.
בצורות יארים בקע וכל-יקר ראתה עינו 10
Amabowola njira mʼmatanthwewo; ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo.
מבכי נהרות חבש ותעלמה יצא אור 11
Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso, motero amatulutsira poyera zinthu zobisika.
והחכמה מאין תמצא ואי זה מקום בינה 12
“Koma nzeru zingapezeke kuti? Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
לא-ידע אנוש ערכה ולא תמצא בארץ החיים 13
Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo; nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo.
תהום אמר לא בי-היא וים אמר אין עמדי 14
Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’ Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’
לא-יתן סגור תחתיה ולא ישקל כסף מחירה 15
Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri, mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri.
לא-תסלה בכתם אופיר בשהם יקר וספיר 16
Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri, kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.
לא-יערכנה זהב וזכוכית ותמורתה כלי-פז 17
Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi, sungayigule ndi zokometsera zagolide.
ראמות וגביש לא יזכר ומשך חכמה מפנינים 18
Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe; mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi.
לא-יערכנה פטדת-כוש בכתם טהור לא תסלה 19
Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi; nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri.
והחכמה מאין תבוא ואי זה מקום בינה 20
“Kodi tsono nzeru zimachokera kuti? Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
ונעלמה מעיני כל-חי ומעוף השמים נסתרה 21
Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse, ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga.
אבדון ומות אמרו באזנינו שמענו שמעה 22
Chiwonongeko ndi imfa zikuti, ‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’
אלהים הבין דרכה והוא ידע את-מקומה 23
Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko, ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala,
כי-הוא לקצות-הארץ יביט תחת כל-השמים יראה 24
pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo.
לעשות לרוח משקל ומים תכן במדה 25
Iye atapatsa mphepo mphamvu zake, nayeza kuzama kwa nyanja,
בעשתו למטר חק ודרך לחזיז קלות 26
atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu,
אז ראה ויספרה הכינה וגם-חקרה 27
pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake; nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
ויאמר לאדם--הן יראת אדני היא חכמה וסור מרע בינה 28
Ndipo Iye anati kwa munthu, ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’”

< איוב 28 >