< איוב 17 >

רוחי חבלה ימי נזעכו קברים לי 1
“Mtima wanga wasweka, masiku anga atha, manda akundidikira.
אם-לא התלים עמדי ובהמרותם תלן עיני 2
Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira; maso anga akupenyetsetsa mdani wanga.
שימה-נא ערבני עמך מי הוא לידי יתקע 3
“Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna. Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole?
כי-לבם צפנת משכל על-כן לא תרמם 4
Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu; choncho simudzawalola kuti apambane.
לחלק יגיד רעים ועיני בניו תכלנה 5
Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma, ana ake sadzaona mwayi.
והציגני למשל עמים ותפת לפנים אהיה 6
“Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense, munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake.
ותכה מכעש עיני ויצרי כצל כלם 7
Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni; ndawonda ndi mutu womwe.
ישמו ישרים על-זאת ונקי על-חנף יתערר 8
Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi; anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu.
ויאחז צדיק דרכו וטהר-ידים יסיף אמץ 9
Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo, ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka.
ואולם--כלם תשבו ובאו נא ולא-אמצא בכם חכם 10
“Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo, sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo.
ימי עברו זמתי נתקו-- מורשי לבבי 11
Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka, pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga.
לילה ליום ישימו אור קרוב מפני-חשך 12
Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana, nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’
אם-אקוה שאול ביתי בחשך רפדתי יצועי (Sheol h7585) 13
Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda, ngati ndiyala bedi langa mu mdima, (Sheol h7585)
לשחת קראתי אבי אתה אמי ואחתי לרמה 14
ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’ ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’
ואיה אפו תקותי ותקותי מי ישורנה 15
tsono chiyembekezo changa chili kuti? Ndani angaone populumukira panga?
בדי שאל תרדנה אם-יחד על-עפר נחת (Sheol h7585) 16
Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse, polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.” (Sheol h7585)

< איוב 17 >