< איוב 16 >
Pamenepo Yobu anayankha kuti,
שמעתי כאלה רבות מנחמי עמל כלכם | 2 |
“Ndinamvapo zambiri monga zimenezi; nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.
הקץ לדברי-רוח או מה-ימריצך כי תענה | 3 |
Kodi mawu anu ochulukawo adzatha? Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
גם אנכי-- ככם אדברה לו יש נפשכם תחת נפשי-- אחבירה עליכם במלים ואניעה עליכם במו ראשי | 4 |
Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu, inuyo mukanakhala monga ndilili inemu; Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu ndi kukupukusirani mutu wanga.
אאמצכם במו-פי וניד שפתי יחשך | 5 |
Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani; chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.
אם-אדברה לא-יחשך כאבי ואחדלה מה-מני יהלך | 6 |
“Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa; ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.
אך-עתה הלאני השמות כל-עדתי | 7 |
Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu; mwawononga banja langa lonse.
ותקמטני לעד היה ויקם בי כחשי בפני יענה | 8 |
Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni; kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.
אפו טרף וישטמני--חרק עלי בשניו צרי ילטש עיניו לי | 9 |
Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane, amachita kulumira mano; mdani wanga amandituzulira maso.
פערו עלי בפיהם--בחרפה הכו לחיי יחד עלי יתמלאון | 10 |
Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza; amandimenya pa tsaya mwachipongwe ndipo amagwirizana polimbana nane.
יסגירני אל אל עויל ועל-ידי רשעים ירטני | 11 |
Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.
שלו הייתי ויפרפרני-- ואחז בערפי ויפצפצני ויקימני לו למטרה | 12 |
Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya; anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
יסבו עלי רביו-- יפלח כליותי ולא יחמל ישפך לארץ מררתי | 13 |
anthu ake oponya mauta andizungulira. Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga ndipo akutayira pansi ndulu yanga.
יפרצני פרץ על-פני-פרץ ירץ עלי כגבור | 14 |
Akundivulaza kawirikawiri, akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.
שק תפרתי עלי גלדי ועללתי בעפר קרני | 15 |
“Ndasokerera chiguduli pa thupi langa ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.
פני חמרמרה (חמרמרו) מני-בכי ועל עפעפי צלמות | 16 |
Maso anga afiira ndi kulira, ndipo zikope zanga zatupa;
על לא-חמס בכפי ותפלתי זכה | 17 |
komatu manja anga sanachite zachiwawa ndipo pemphero langa ndi lolungama.
ארץ אל-תכסי דמי ואל-יהי מקום לזעקתי | 18 |
“Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga; kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!
גם-עתה הנה-בשמים עדי ושהדי במרמים | 19 |
Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba; wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.
מליצי רעי אל-אלוה דלפה עיני | 20 |
Wondipembedzera ndi bwenzi langa, pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;
ויוכח לגבר עם-אלוה ובן-אדם לרעהו | 21 |
iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu monga munthu amadandaulira bwenzi lake.
כי-שנות מספר יאתיו וארח לא-אשוב אהלך | 22 |
“Pakuti sipapita zaka zambiri ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”