< איוב 15 >
ויען אליפז התימני ויאמר | 1 |
Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
החכם יענה דעת-רוח וימלא קדים בטנו | 2 |
“Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere, kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?
הוכח בדבר לא-יסכון ומלים לא-יועיל בם | 3 |
Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake, kapena kuyankhula mawu opanda phindu?
אף-אתה תפר יראה ותגרע שיחה לפני-אל | 4 |
Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.
כי יאלף עונך פיך ותבחר לשון ערומים | 5 |
Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo; ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.
ירשיעך פיך ולא-אני ושפתיך יענו-בך | 6 |
Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga; milomo yakoyo ikukutsutsa.
הראישון אדם תולד ולפני גבעות חוללת | 7 |
“Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?
הבסוד אלוה תשמע ותגרע אליך חכמה | 8 |
Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu? Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?
מה-ידעת ולא נדע תבין ולא-עמנו הוא | 9 |
Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa? Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?
גם-שב גם-ישיש בנו-- כביר מאביך ימים | 10 |
Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu, anthu amvulazakale kupambana abambo ako.
המעט ממך תנחומות אל ודבר לאט עמך | 11 |
Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira, mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?
מה-יקחך לבך ומה-ירזמון עיניך | 12 |
Chifukwa chiyani ukupsa mtima, ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,
כי-תשיב אל-אל רוחך והצאת מפיך מלין | 13 |
moti ukupsera mtima Mulungu ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?
מה-אנוש כי-יזכה וכי-יצדק ילוד אשה | 14 |
“Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?
הן בקדשו לא יאמין ושמים לא-זכו בעיניו | 15 |
Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake, ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,
אף כי-נתעב ונאלח איש-שתה כמים עולה | 16 |
nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota, amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.
אחוך שמע-לי וזה-חזיתי ואספרה | 17 |
“Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera; ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,
אשר-חכמים יגידו ולא כחדו מאבותם | 18 |
zimene anandiphunzitsa anthu anzeru, sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.
להם לבדם נתנה הארץ ולא-עבר זר בתוכם | 19 |
(Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).
כל-ימי רשע הוא מתחולל ומספר שנים נצפנו לעריץ | 20 |
Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake, munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.
קול-פחדים באזניו בשלום שודד יבואנו | 21 |
Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake, pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.
לא-יאמין שוב מני-חשך וצפו (וצפוי) הוא אלי-חרב | 22 |
Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa; iyeyo ndi woyenera kuphedwa.
נדד הוא ללחם איה ידע כי-נכון בידו יום-חשך | 23 |
Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya; amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.
יבעתהו צר ומצוקה תתקפהו כמלך עתיד לכידור | 24 |
Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri; zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,
כי-נטה אל-אל ידו ואל-שדי יתגבר | 25 |
chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.
ירוץ אליו בצואר בעבי גבי מגניו | 26 |
Amapita mwa mwano kukalimbana naye atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.
כי-כסה פניו בחלבו ויעש פימה עלי-כסל | 27 |
“Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,
וישכון ערים נכחדות--בתים לא-ישבו למו אשר התעתדו לגלים | 28 |
munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu, nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.
לא-יעשר ולא-יקום חילו ולא-יטה לארץ מנלם | 29 |
Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa, ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.
לא-יסור מני-חשך--ינקתו תיבש שלהבת ויסור ברוח פיו | 30 |
Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo; lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake, ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.
אל-יאמן בשו נתעה כי-שוא תהיה תמורתו | 31 |
Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe, pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.
בלא-יומו תמלא וכפתו לא רעננה | 32 |
Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane, ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.
יחמס כגפן בסרו וישלך כזית נצתו | 33 |
Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse, adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.
כי-עדת חנף גלמוד ואש אכלה אהלי-שחד | 34 |
Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.
הרה עמל וילד און ובטנם תכין מרמה | 35 |
Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa; mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”