< איוב 12 >
Pamenepo Yobu anayankha kuti,
אמנם כי אתם-עם ועמכם תמות חכמה | 2 |
“Ndithudi inuyo ndinu anthu ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!
גם-לי לבב כמוכם--לא-נפל אנכי מכם ואת-מי-אין כמו-אלה | 3 |
Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?
שחק לרעהו אהיה--קרא לאלוה ויענהו שחוק צדיק תמים | 4 |
“Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga, ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha. Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!
לפיד בוז לעשתות שאנן-- נכון למועדי רגל | 5 |
Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
ישליו אהלים לשדדים ובטחות למרגיזי אל-- לאשר הביא אלוה בידו | 6 |
Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere, ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino, amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.
ואולם--שאל-נא בהמות ותרך ועוף השמים ויגד-לך | 7 |
“Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;
או שיח לארץ ותרך ויספרו לך דגי הים | 8 |
kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.
מי לא-ידע בכל-אלה כי יד-יהוה עשתה זאת | 9 |
Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?
אשר בידו נפש כל-חי ורוח כל-בשר-איש | 10 |
Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
הלא-אזן מלין תבחן וחך אכל יטעם-לו | 11 |
Kodi khutu sindiye limene limamva mawu monga mmene lilime limalawira chakudya?
בישישים חכמה וארך ימים תבונה | 12 |
Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba? Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?
עמו חכמה וגבורה לו עצה ותבונה | 13 |
“Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.
הן יהרוס ולא יבנה יסגר על-איש ולא יפתח | 14 |
Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso. Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.
הן יעצר במים ויבשו וישלחם ויהפכו ארץ | 15 |
Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma; akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.
עמו עז ותושיה לו שגג ומשגה | 16 |
Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana; munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.
מוליך יועצים שולל ושפטים יהולל | 17 |
Iye amalanda aphungu nzeru zawo ndipo amapusitsa oweruza.
מוסר מלכים פתח ויאסר אזור במתניהם | 18 |
Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.
מוליך כהנים שולל ואתנים יסלף | 19 |
Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.
מסיר שפה לנאמנים וטעם זקנים יקח | 20 |
Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.
שופך בוז על-נדיבים ומזיח אפיקים רפה | 21 |
Iye amanyoza anthu otchuka ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.
מגלה עמקות מני-חשך ויצא לאור צלמות | 22 |
Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.
משגיא לגוים ויאבדם שטח לגוים וינחם | 23 |
Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso; amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.
מסיר--לב ראשי עם-הארץ ויתעם בתהו לא-דרך | 24 |
Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.
ימששו-חשך ולא-אור ויתעם כשכור | 25 |
Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira; Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.