< ירמיה 33 >
ויהי דבר יהוה אל ירמיהו שנית והוא עודנו עצור בחצר המטרה לאמר | 1 |
Yeremiya akanali mʼndende mʼbwalo la alonda, Yehova anayankhula nayenso kachiwiri nati:
כה אמר יהוה עשה יהוה יוצר אותה להכינה--יהוה שמו | 2 |
“Yehova amene analenga dziko lapansi, kuliwumba ndi kulikhazikitsa; amene dzina lake ndi Yehova, akuti,
קרא אלי ואענך ואגידה לך גדלות ובצרות לא ידעתם | 3 |
‘Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.’
כי כה אמר יהוה אלהי ישראל על בתי העיר הזאת ועל בתי מלכי יהודה--הנתצים אל הסללות ואל החרב | 4 |
Yehova Mulungu wa Israeli akunenapo pa za nyumba za mu mzinda muno ndiponso pa za nyumba za mafumu a Yuda. Zidzagwetsedwa, ndipo palibe chifukwa cholimbana ndi mitumbira ya nkhondo ya Ababuloni.
באים להלחם את הכשדים ולמלאם את פגרי האדם אשר הכיתי באפי ובחמתי ואשר הסתרתי פני מהעיר הזאת על כל רעתם | 5 |
Ababuloni akubwera kudzawuthira nkhondo mzindawu ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzawapha mokwiya ndi mwaukali. Ndawufulatira mzinda uno chifukwa cha zoyipa zake zonse.
הנני מעלה לה ארכה ומרפא ורפאתים וגליתי להם עתרת שלום ואמת | 6 |
“‘Pambuyo pake mzindawu ndidzawupatsanso moyo ndi kuwuchiritsa; ndidzachiritsa anthu anga ndi kuwapatsa chitetezo ndi mtendere weniweni.
והשבתי את שבות יהודה ואת שבות ישראל ובנתים כבראשנה | 7 |
Ndidzawakhazikanso Ayuda ndi Aisraeli ku dziko lawo, ndipo ndidzawabwezera monga mmene analili poyamba.
וטהרתים מכל עונם אשר חטאו לי וסלחתי לכול (לכל) עונותיהם אשר חטאו לי ואשר פשעו בי | 8 |
Ndidzawayeretsa pochotsa zoyipa zonse zimene anandichitira, ndiponso ndidzawakhululukira machimo onse amene anachita pondiwukira.
והיתה לי לשם ששון לתהלה ולתפארת לכל גויי הארץ--אשר ישמעו את כל הטובה אשר אנכי עשה אותם ופחדו ורגזו על כל הטובה ועל כל השלום אשר אנכי עשה לה | 9 |
Mzinda wa Yerusalemu udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemerero. Anthu a mitundu yonse adzanditamanda akadzamva za zabwino zonse zimene ndawuchitira mzindawu. Iwo adzachita mantha ndi kunjenjemera poona madalitso ochuluka ndi mtendere zimene ndapereka kwa mzinda umenewu.’
כה אמר יהוה עוד ישמע במקום הזה אשר אתם אמרים חרב הוא מאין אדם ומאין בהמה--בערי יהודה ובחצות ירושלם הנשמות מאין אדם ומאין יושב ומאין בהמה | 10 |
“Yehova akuti, ‘Inu mumanena za malo ano kuti ndi bwinja,’ malo opandamo anthu kapena nyama. Komatu mizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu mʼmene tsopano muli zii mudzamvekanso
קול ששון וקול שמחה קול חתן וקול כלה קול אמרים הודו את יהוה צבאות כי טוב יהוה כי לעולם חסדו מבאים תודה בית יהוה כי אשיב את שבות הארץ כבראשנה אמר יהוה | 11 |
mfuwu wachimwemwe ndi mawu achisangalalo, mawu a mkwatibwi ndi mkwati. Mʼnyumba ya Mulungu mudzamvekanso nyimbo za anthu amene akudzapereka nsembe zothokoza Yehova. Azidzati, “Yamikani Yehova Wamphamvuzonse, popeza Iye ndi wabwino; pakuti chifundo chake nʼchamuyaya.” Pakuti ndidzabwezeretsa zinthu zabwino za dziko lino monga zinalili poyamba, akutero Yehova.
כה אמר יהוה צבאות עוד יהיה במקום הזה החרב מאין אדם ועד בהמה ובכל עריו--נוה רעים מרבצים צאן | 12 |
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Malo ano, a chipululu ndi wopanda anthu kapena nyama, mʼmizinda yake yonse mudzakhala msipu umene abusa adzadyetserako nkhosa zawo.
בערי ההר בערי השפלה ובערי הנגב ובארץ בנימן ובסביבי ירושלם ובערי יהודה--עד תעברנה הצאן על ידי מונה אמר יהוה | 13 |
Ku mizinda ya kumapiri, ya kuchigwa, ya ku Negevi, ya ku dera la Benjamini, ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzadutsanso pamaso pa munthu woziwerenga,’ akutero Yehova.
הנה ימים באים נאם יהוה והקמתי את הדבר הטוב אשר דברתי אל בית ישראל ועל בית יהודה | 14 |
“‘Taonani masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene ndidzachitadi zokoma zimene ndinalonjeza Aisraeli ndi nyumba ya Yuda.
בימים ההם ובעת ההיא אצמיח לדוד צמח צדקה ועשה משפט וצדקה בארץ | 15 |
“‘Mʼmasiku amenewo ndi pa nthawi imeneyo ndidzaphukitsa Nthambi yolungama kuchokera ku banja la Davide; munthuyo adzachita zolungama ndi zabwino mʼdziko.
בימים ההם תושע יהודה וירושלם תשכון לבטח וזה אשר יקרא לה יהוה צדקנו | 16 |
Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumuka ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere. Dzina limene mzindawu udzadziwike nalo ndi ili: Yehova Chilungamo Chathu.’
כי כה אמר יהוה לא יכרת לדוד--איש ישב על כסא בית ישראל | 17 |
Yehova akunena kuti, ‘Davide sadzasowa mdzukulu wolowa mʼmalo mwake pa mpando waufumu wa Israeli,
ולכהנים הלוים לא יכרת איש מלפני מעלה עולה ומקטיר מנחה ועשה זבח--כל הימים | 18 |
ngakhale ansembe, amene ndi Alevi, sadzasowanso munthu woyima pamaso panga nthawi zonse wopereka nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zina.’”
ויהי דבר יהוה אל ירמיהו לאמור | 19 |
Yehova anawuza Yeremiya kuti:
כה אמר יהוה אם תפרו את בריתי היום ואת בריתי הלילה ולבלתי היות יומם ולילה בעתם | 20 |
Mawu anga ndi awa. Ine ndinachita pangano ndi usana ndi usiku kuti zizibwera pa nthawi yake. Pangano limeneli inu simungaliphwanye.
גם בריתי תפר את דוד עבדי מהיות לו בן מלך על כסאו ואת הלוים הכהנים משרתי | 21 |
Ndinachitanso pangano ndi Davide, mtumiki wanga kuti nthawi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndinachitanso pangano ndi Alevi kuti iwonso adzanditumikira nthawi zonse. Mapangano amenewa sadzaphwanyidwa nthawi zonse.
אשר לא יספר צבא השמים ולא ימד חול הים--כן ארבה את זרע דוד עבדי ואת הלוים משרתי אתי | 22 |
Ndidzachulukitsa ngati nyenyezi zamlengalenga ndiponso ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndiponso za Alevi amene amanditumikira Ine.
ויהי דבר יהוה אל ירמיהו לאמר | 23 |
Yehova anafunsa Yeremiya kuti,
הלוא ראית מה העם הזה דברו לאמר שתי המשפחות אשר בחר יהוה בהם וימאסם ואת עמי ינאצון מהיות עוד גוי לפניהם | 24 |
“Kodi sunamve mmene anthu ena akumanenera kuti, ‘Yehova wakana maufumu awiriwa amene Iye anawasankha.’ Kotero anthuwo akunyoza anthu anga ndipo sakuwayesanso mtundu wa anthu.
כה אמר יהוה אם לא בריתי יומם ולילה--חקות שמים וארץ לא שמתי | 25 |
‘Koma Ine Yehova ndinachita pangano ndi usana ndi usiku. Ndinakhazikitsanso malamulo oyendetsa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi,
גם זרע יעקוב ודוד עבדי אמאס מקחת מזרעו משלים אל זרע אברהם ישחק ויעקב כי אשוב (אשיב) את שבותם ורחמתים | 26 |
monga ndachita zimenezi motsimikiza, choncho ndidzasunga pangano limene ndinachita ndi zidzukulu za Yakobo ndi Davide mtumiki wanga. Ndidzasankha mmodzi mwa ana a Davide kuti alamulire zidzukulu za Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Komatu ndidzawamvera chifundo ndi kuwakhazikanso pabwino.’”