< ירמיה 30 >

הדבר אשר היה אל ירמיהו מאת יהוה לאמר 1
Yehova anawuza Yeremiya kuti,
כה אמר יהוה אלהי ישראל לאמר כתב לך את כל הדברים אשר דברתי אליך--אל ספר 2
“Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza.
כי הנה ימים באים נאם יהוה ושבתי את שבות עמי ישראל ויהודה אמר יהוה והשבתים אל הארץ אשר נתתי לאבותם--וירשוה 3
Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”
ואלה הדברים אשר דבר יהוה אל ישראל--ואל יהודה 4
Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda:
כי כה אמר יהוה קול חרדה שמענו--פחד ואין שלום 5
“Yehova akuti: “Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa, ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
שאלו נא וראו אם ילד זכר מדוע ראיתי כל גבר ידיו על חלציו כיולדה ונהפכו כל פנים לירקון 6
Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti: Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
הוי כי גדול היום ההוא--מאין כמהו ועת צרה היא ליעקב וממנה יושע 7
Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri! Sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo, koma adzapulumuka ku masautsowo.”
והיה ביום ההוא נאם יהוה צבאות אשבר עלו מעל צוארך ומוסרותיך אנתק ולא יעבדו בו עוד זרים 8
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo ndipo ndidzadula zingwe zowamanga; Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
ועבדו את יהוה אלהיהם ואת דוד מלכם אשר אקים להם 9
Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo ndiponso Davide mfumu yawo, amene ndidzawasankhira.
ואתה אל תירא עבדי יעקב נאם יהוה ואל תחת ישראל--כי הנני מושיעך מרחוק ואת זרעך מארץ שבים ושב יעקב ושקט ושאנן ואין מחריד 10
“‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo; usade nkhawa, iwe Israeli,’ akutero Yehova. ‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali, zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo. Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere, ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.
כי אתך אני נאם יהוה להושיעך כי אעשה כלה בכל הגוים אשר הפצותיך שם אך אתך לא אעשה כלה ויסרתיך למשפט ונקה לא אנקך 11
Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’ akutero Yehova. ‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu kumene ndinakubalalitsirani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa. Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’”
כי כה אמר יהוה אנוש לשברך--נחלה מכתך 12
Yehova akuti, “Chilonda chanu nʼchosachizika, bala lanu ndi lonyeka.
אין דן דינך למזור רפאות תעלה אין לך 13
Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu, palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira, palibe mankhwala ochiritsa inu.
כל מאהביך שכחוך אותך לא ידרשו כי מכת אויב הכיתיך מוסר אכזרי--על רב עונך עצמו חטאתיך 14
Abwenzi anu onse akuyiwalani; sasamalanso za inu. Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira. Ndipo ndakulangani mwa nkhanza, chifukwa machimo anu ndi ambiri, ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
מה תזעק על שברך אנוש מכאבך על רב עונך עצמו חטאתיך--עשיתי אלה לך 15
Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu? Bala lanu silingapole ayi. Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
לכן כל אכליך יאכלו וכל צריך כלם בשבי ילכו והיו שאסיך למשסה וכל בזזיך אתן לבז 16
“Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa; adani anu onse adzapita ku ukapolo. Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso; onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
כי אעלה ארכה לך וממכותיך ארפאך נאם יהוה כי נדחה קראו לך--ציון היא דרש אין לה 17
Ndidzachiza matenda anu ndi kupoletsa zilonda zanu, akutero Yehova, ‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika. Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’”
כה אמר יהוה הנני שב שבות אהלי יעקוב ומשכנתיו ארחם ונבנתה עיר על תלה וארמון על משפטו ישב 18
Yehova akuti, “Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo; mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake, nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
ויצא מהם תודה וקול משחקים והרבתים ולא ימעטו והכבדתים ולא יצערו 19
Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo. Ndidzawachulukitsa, ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika; ndidzawapatsa ulemerero, ndipo sadzanyozedwanso.
והיו בניו כקדם ועדתו לפני תכון ופקדתי על כל לחציו 20
Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale, ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga; ndidzalanga onse owazunza.
והיה אדירו ממנו ומשלו מקרבו יצא והקרבתיו ונגש אלי כי מי הוא זה ערב את לבו לגשת אלי--נאם יהוה 21
Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo. Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo. Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira. Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane popanda kuyitanidwa?” akutero Yehova.
והייתם לי לעם ואנכי אהיה לכם לאלהים 22
“Choncho inu mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”
הנה סערת יהוה חמה יצאה--סער מתגורר על ראש רשעים יחול 23
Taonani ukali wa Yehova wowomba ngati mphepo ya mkuntho. Mphepo ya namondwe ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.
לא ישוב חרון אף יהוה עד עשתו ועד הקימו מזמות לבו באחרית הימים תתבוננו בה 24
Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka mpaka atakwaniritsa zolinga za mu mtima mwake. Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.

< ירמיה 30 >