< ירמיה 25 >

הדבר אשר היה על ירמיהו על כל עם יהודה בשנה הרבעית ליהויקים בן יאשיהו מלך יהודה היא השנה הראשנית לנבוכדראצר מלך בבל 1
Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni.
אשר דבר ירמיהו הנביא על כל עם יהודה ואל כל ישבי ירושלם לאמר 2
Choncho mneneri Yeremiya anawuza anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi onse amene amakhala mu Yerusalemu kuti:
מן שלש עשרה שנה ליאשיהו בן אמון מלך יהודה ועד היום הזה זה שלש ועשרים שנה היה דבר יהוה אלי ואדבר אליכם אשכים ודבר ולא שמעתם 3
Kwa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda mpaka lero lino, Yehova wakhala akundipatsa mauthenga ake ndipo ine ndakhala ndikuyankhula ndi inu kawirikawiri, koma inu simunamvere.
ושלח יהוה אליכם את כל עבדיו הנבאים השכם ושלח--ולא שמעתם ולא הטיתם את אזנכם לשמע 4
Ndipo ngakhale Yehova kawirikawiri wakhala akukutumizirani atumiki ake onse, aneneri, inuyo simunamvere kapena kutchera khutu.
לאמר שובו נא איש מדרכו הרעה ומרע מעלליכם ושבו על האדמה אשר נתן יהוה לכם ולאבותיכם--למן עולם ועד עולם 5
Aneneriwo ankanena kuti, “Ngati aliyense wa inu abwerere, kusiya njira zake zoyipa ndi machitidwe ake oyipa, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko limene Yehova anapereka kwa makolo anu kwamuyaya.
ואל תלכו אחרי אלהים אחרים לעבדם ולהשתחות להם ולא תכעיסו אותי במעשה ידיכם ולא ארע לכם 6
Musatsatire milungu ina nʼkuyitumikira ndi kuyipembedza. Musapute mkwiyo wanga ndi mafano amene mwapanga ndi manja anu. Mukatero Ine sindidzakuwonongani.
ולא שמעתם אלי נאם יהוה למען הכעסוני (הכעיסני) במעשה ידיכם לרע לכם 7
“Koma inu simunandimvere,” akutero Yehova, “ndipo munaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene munapanga ndi manja anu. Choncho munadziwononga nokha.”
לכן כה אמר יהוה צבאות יען אשר לא שמעתם את דברי 8
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Chifukwa simunamvere mawu anga,
הנני שלח ולקחתי את כל משפחות צפון נאם יהוה ואל נבוכדראצר מלך בבל עבדי והבאתים על הארץ הזאת ועל ישביה ועל כל הגוים האלה סביב והחרמתים--ושמתים לשמה ולשרקה ולחרבות עולם 9
ndidzayitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni,” akutero Yehova, “ndipo adzathira nkhondo dziko lino ndi anthu ake pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ozungulira dzikoli. Ndidzawawononga kwathunthu ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka, mpaka muyaya.
והאבדתי מהם קול ששון וקול שמחה קול חתן וקול כלה--קול רחים ואור נר 10
Ndidzathetsa mfuwu wachimwemwe ndi wachisangalalo, mawu a mkwati ndi mkwatibwi, phokoso la mphero ndi kuwala kwa nyale.
והיתה כל הארץ הזאת לחרבה לשמה ועבדו הגוים האלה את מלך בבל--שבעים שנה 11
Dziko lonse lidzakhala bwinja ndi chipululu, ndipo mitundu ina idzatumikira mfumu ya ku Babuloni kwa 70.
והיה כמלאות שבעים שנה אפקד על מלך בבל ועל הגוי ההוא נאם יהוה את עונם--ועל ארץ כשדים ושמתי אתו לשממות עולם 12
“Koma zaka 70 zikadzatha, ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi anthu ake, chifukwa cha zolakwa zawo,” akutero Yehova, “ndipo dziko lawo lidzakhala chipululu mpaka muyaya.
והבאותי (והבאתי) על הארץ ההיא את כל דברי אשר דברתי עליה--את כל הכתוב בספר הזה אשר נבא ירמיהו על כל הגוים 13
Ndidzachita zinthu zonse zimene ndinayankhula zotsutsa dzikolo, zonse zimene zalembedwa mʼbuku lino, ndiponso zonse zimene Yeremiya analosera zotsutsa anthu amenewa.
כי עבדו בם גם המה גוים רבים ומלכים גדולים ושלמתי להם כפעלם וכמעשה ידיהם 14
Iwo eni adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi mafumu amphamvu. Ndidzawabwezera molingana ndi zochita zawo ndi ntchito za manja awo.”
כי כה אמר יהוה אלהי ישראל אלי קח את כוס היין החמה הזאת מידי והשקיתה אתו את כל הגוים אשר אנכי שלח אותך אליהם 15
Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma.
ושתו והתגעשו והתהללו מפני החרב אשר אנכי שלח בינתם 16
Akadzamwa adzayamba kudzandira ndi kuchita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikuyitumiza pakati pawo.”
ואקח את הכוס מיד יהוה ואשקה את כל הגוים אשר שלחני יהוה אליהם 17
Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako:
את ירושלם ואת ערי יהודה ואת מלכיה את שריה לתת אתם לחרבה לשמה לשרקה ולקללה--כיום הזה 18
Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino.
את פרעה מלך מצרים ואת עבדיו ואת שריו ואת כל עמו 19
Ananditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Igupto, kwa atumiki ake, nduna zake ndi kwa anthu ake onse,
ואת כל הערב ואת כל מלכי ארץ העוץ ואת כל מלכי ארץ פלשתים ואת אשקלון ואת עזה ואת עקרון ואת שארית אשדוד 20
ndi kwa anthu ena onse a mitundu yachilendo; mafumu onse a ku Uzi; mafumu onse a Afilisti, a ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekroni ndiponso kwa anthu a ku chigwa chotsala cha Asidodi;
את אדום ואת מואב ואת בני עמון 21
Edomu, Mowabu ndi Amoni.
ואת כל מלכי צר ואת כל מלכי צידון ואת מלכי האי אשר בעבר הים 22
Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Turo ndi ku Sidoni; kwa mafumu a kutsidya la nyanja;
ואת דדן ואת תימא ואת בוז ואת כל קצוצי פאה 23
ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa chamʼmbali.
ואת כל מלכי ערב ואת כל מלכי הערב השכנים במדבר 24
Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi mafumu onse a anthu achilendo amene amakhala mʼchipululu.
ואת כל מלכי זמרי ואת כל מלכי עילם ואת כל מלכי מדי 25
Anandituma kwa mafumu onse a ku Zimuri, Elamu ndi Mediya;
ואת כל מלכי הצפון הקרבים והרחקים איש אל אחיו ואת כל הממלכות הארץ אשר על פני האדמה ומלך ששך ישתה אחריהם 26
ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.
ואמרת אליהם כה אמר יהוה צבאות אלהי ישראל שתו ושכרו וקיו ונפלו ולא תקומו--מפני החרב אשר אנכי שלח ביניכם 27
“Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Imwani, ledzerani ndipo musanze, mugwe osadzukanso chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’
והיה כי ימאנו לקחת הכוס מידך--לשתות ואמרת אליהם כה אמר יהוה צבאות--שתו תשתו 28
Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’”
כי הנה בעיר אשר נקרא שמי עליה אנכי מחל להרע ואתם הנקה תנקו לא תנקו--כי חרב אני קרא על כל ישבי הארץ נאם יהוה צבאות 29
Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.
ואתה תנבא אליהם את כל הדברים האלה ואמרת אליהם יהוה ממרום ישאג וממעון קדשו יתן קולו--שאג ישאג על נוהו הידד כדרכים יענה אל כל ישבי הארץ 30
“Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti, “‘Yehova adzabangula kumwamba; mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika. Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake. Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa, kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.
בא שאון עד קצה הארץ--כי ריב ליהוה בגוים נשפט הוא לכל בשר הרשעים נתנם לחרב נאם יהוה 31
Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi, chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse; adzaweruza mtundu wonse wa anthu ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’” akutero Yehova.
כה אמר יהוה צבאות הנה רעה יצאת מגוי אל גוי וסער גדול יעור מירכתי ארץ 32
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani! Mavuto akuti akachoka pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina; mphepo ya mkuntho ikuyambira ku malekezero a dziko.”
והיו חללי יהוה ביום ההוא מקצה הארץ ועד קצה הארץ לא יספדו ולא יאספו ולא יקברו--לדמן על פני האדמה יהיו 33
Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Yehova adzangoti mbwee ponseponse, pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzawalire kapena kusonkhanitsa mitemboyo kuti ikayikidwe mʼmanda, koma idzakhala mbwee ngati ndowe.
הילילו הרעים וזעקו והתפלשו אדירי הצאן--כי מלאו ימיכם לטבוח ותפוצותיכם ונפלתם ככלי חמדה 34
Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu; gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa. Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika; mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.
ואבד מנוס מן הרעים ופליטה מאדירי הצאן 35
Abusa adzasowa kothawira, atsogoleri a nkhosa adzasowa malo opulumukira.
קול צעקת הרעים ויללת אדירי הצאן--כי שדד יהוה את מרעיתם 36
Imvani kulira kwa abusa, atsogoleri a nkhosa akulira, chifukwa Yehova akuwononga msipu wawo.
ונדמו נאות השלום מפני חרון אף יהוה 37
Makola awo a nkhosa amene anali pamtendere adzasanduka bwinja chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
עזב ככפיר סכו--כי היתה ארצם לשמה מפני חרון היונה ומפני חרון אפו 38
Ngati mkango, Yehova wasiya phanga lake, pakuti dziko lawo lasanduka chipululu chifukwa cha nkhondo ya owazunza ndiponso chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

< ירמיה 25 >