< ירמיה 16 >

ויהי דבר יהוה אלי לאמר 1
Kenaka Yehova anandiwuza kuti,
לא תקח לך אשה ולא יהיו לך בנים ובנות במקום הזה 2
“Usadzakwatire ndi kubereka ana aamuna kapena aakazi malo ano
כי כה אמר יהוה על הבנים ועל הבנות הילודים במקום הזה ועל אמתם הילדות אותם ועל אבותם המולדים אותם--בארץ הזאת 3
pakuti ana aamuna ndi ana aakazi obadwira mʼdziko muno, komanso amayi awo ndi abambo awo amene anabereka anawo mʼdziko muno,
ממותי תחלאים ימתו לא יספדו ולא יקברו--לדמן על פני האדמה יהיו ובחרב וברעב יכלו והיתה נבלתם למאכל לעוף השמים ולבהמת הארץ 4
adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.”
כי כה אמר יהוה אל תבוא בית מרזח ואל תלך לספוד ואל תנד להם כי אספתי את שלומי מאת העם הזה נאם יהוה--את החסד ואת הרחמים 5
Yehova akuti, “Usalowe mʼnyumba ya maliro; usapite kukalira maliro kapena kukapepesa, chifukwa Ine ndawachotsera madalitso anga, chikondi changa ndi chifundo changa.”
ומתו גדלים וקטנים בארץ הזאת לא יקברו ולא יספדו להם--ולא יתגדד ולא יקרח להם 6
Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo.
ולא יפרסו להם על אבל לנחמו על מת ולא ישקו אותם כוס תנחומים על אביו ועל אמו 7
Palibe amene adzapereka chakudya kutonthoza amene akulira maliro, ngakhale kuti womwalirayo ndi abambo ake kapena amayi ake.
ובית משתה לא תבוא לשבת אותם לאכל ולשתות 8
“Ndipo usalowe mʼnyumba mmene muli madyerero, nʼkukhala pansi ndi kudya ndi kumwa nawo.
כי כה אמר יהוה צבאות אלהי ישראל הנני משבית מן המקום הזה לעיניכם ובימיכם--קול ששון וקול שמחה קול חתן וקול כלה 9
Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Pa nthawi yanu, inu mukuona ndidzathetsa mawu achimwemwe ndi achisangalalo ndiponso mawu a mkwati ndi mkwatibwi pa malo ano.’
והיה כי תגיד לעם הזה את כל הדברים האלה ואמרו אליך על מה דבר יהוה עלינו את כל הרעה הגדולה הזאת ומה עוננו ומה חטאתנו אשר חטאנו ליהוה אלהינו 10
“Ukawawuza anthu awa zinthu zonsezi akakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wanena kuti tsoka lalikulu lotere lidzatigwere? Kodi talakwa chiyani? Kodi tamuchimwira tchimo lotani Yehova Mulungu wathu?’
ואמרת אליהם על אשר עזבו אבותיכם אותי נאם יהוה וילכו אחרי אלהים אחרים ויעבדום וישתחוו להם ואתי עזבו ואת תורתי לא שמרו 11
Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa.
ואתם הרעתם לעשות מאבותיכם והנכם הלכים איש אחרי שררות לבו הרע לבלתי שמע אלי 12
Komanso inu munachimwa kwambiri kupambana makolo anu. Aliyense wa inu akutsatira zoyipa ndi mtima wake wokanikawo mʼmalo mondimvera Ine.
והטלתי אתכם מעל הארץ הזאת על הארץ אשר לא ידעתם אתם ואבותיכם ועבדתם שם את אלהים אחרים יומם ולילה אשר לא אתן לכם חנינה 13
Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’”
לכן הנה ימים באים נאם יהוה ולא יאמר עוד חי יהוה אשר העלה את בני ישראל מארץ מצרים 14
Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’
כי אם חי יהוה אשר העלה את בני ישראל מארץ צפון ומכל הארצות אשר הדיחם שמה והשבתים על אדמתם אשר נתתי לאבותם 15
koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku mayiko onse kumene anawabalalitsirako.’ Pakuti ndidzawabwezera ku dziko limene ndinalipereka kwa makolo awo.”
הנני שלח לדוגים (לדיגים) רבים נאם יהוה--ודיגום ואחרי כן אשלח לרבים צידים וצדום מעל כל הר ומעל כל גבעה ומנקיקי הסלעים 16
Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe.
כי עיני על כל דרכיהם לא נסתרו מלפני ולא נצפן עונם מנגד עיני 17
Maso anga akuona makhalidwe awo onse; sanabisike pamaso panga. Palibe tchimo limene sindikulidziwa.
ושלמתי ראשונה משנה עונם וחטאתם על חללם את ארצי בנבלת שקוציהם ותועבותיהם מלאו את נחלתי 18
Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”
יהוה עזי ומעזי ומנוסי--ביום צרה אליך גוים יבאו מאפסי ארץ ויאמרו אך שקר נחלו אבותינו הבל ואין בם מועיל 19
Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa, pothawirapo panga nthawi ya masautso, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti, “Makolo anthu anali ndi milungu yonama, anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.
היעשה לו אדם אלהים והמה לא אלהים 20
Kodi anthu nʼkudzipangira milungu? Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”
לכן הנני מודיעם בפעם הזאת אודיעם את ידי ואת גבורתי וידעו כי שמי יהוה 21
“Choncho Ine ndidzawaphunzitsa, kokha kano kuti adziwe za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga. Pamenepo adzadziwa kuti dzina langa ndi Yehova.

< ירמיה 16 >