< ישעה 66 >
כה אמר יהוה השמים כסאי והארץ הדם רגלי אי זה בית אשר תבנו לי ואי זה מקום מנוחתי | 1 |
Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
ואת כל אלה ידי עשתה ויהיו כל אלה נאם יהוה ואל זה אביט--אל עני ונכה רוח וחרד על דברי | 2 |
Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi, motero zonsezi ndi zanga?” Akutero Yehova. “Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu: amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima, ndipo amamvera mawu anga.
שוחט השור מכה איש זובח השה ערף כלב מעלה מנחה דם חזיר מזכיר לבנה מברך און--גם המה בחרו בדרכיהם ובשקוציהם נפשם חפצה | 3 |
Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna amaphanso munthu, ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa, amaphanso galu. Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya amaperekanso magazi a nkhumba. Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso amapembedzanso fano. Popeza iwo asankha njira zawozawo, ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.
גם אני אבחר בתעלליהם ומגורתם אביא להם--יען קראתי ואין עונה דברתי ולא שמעו ויעשו הרע בעיני ובאשר לא חפצתי בחרו | 4 |
Inenso ndawasankhira chilango chowawa ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija. Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha, pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu. Anachita zoyipa pamaso panga ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”
שמעו דבר יהוה החרדים אל דברו אמרו אחיכם שנאיכם מנדיכם למען שמי יכבד יהוה--ונראה בשמחתכם והם יבשו | 5 |
Imvani mawu a Yehova, inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake: “Abale anu amene amakudani, ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti, ‘Yehova alemekezeke kuti ife tione chimwemwe chanu!’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
קול שאון מעיר קול מהיכל קול יהוה משלם גמול לאיביו | 6 |
Imvani mfuwu mu mzinda, imvani phokoso mʼNyumba ya Mulungu! Limenelo ndi liwu la Yehova, kulanga adani ake onse.
בטרם תחיל ילדה בטרם יבוא חבל לה והמליטה זכר | 7 |
“Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa wachira kale; asanayambe kumva ululu, wabala kale mwana wamwamuna.
מי שמע כזאת מי ראה כאלה--היוחל ארץ ביום אחד אם יולד גוי פעם אחת כי חלה גם ילדה ציון את בניה | 8 |
Ndani anamvapo zinthu zoterezi? Ndani anazionapo zinthu zoterezi? Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi, kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi? Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa nthawi yomweyo anabereka ana ake.
האני אשביר ולא אוליד יאמר יהוה אם אני המוליד ועצרתי אמר אלהיך | 9 |
Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira, koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova. “Kodi ndingatseke mimba pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
שמחו את ירושלם וגילו בה כל אהביה שישו אתה משוש כל המתאבלים עליה | 10 |
“Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye, inu nonse amene mumakonda Yerusalemu, kondwera nayeni kwambiri, nonse amene mumamulira.
למען תינקו ושבעתם משד תנחמיה למען תמצו והתענגתם מזיז כבודה | 11 |
Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri wa mʼmawere a chitonthozo chake.”
כי כה אמר יהוה הנני נטה אליה כנהר שלום וכנחל שוטף כבוד גוים--וינקתם על צד תנשאו ועל ברכים תשעשעו | 12 |
Yehova akuti, “Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje wa madzi, ndiponso chuma cha anthu a mitundu ina ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene amayi ake amunyamulira pambalipa, kapena kumufungata pa miyendo yake.
כאיש אשר אמו תנחמנו--כן אנכי אנחמכם ובירושלם תנחמו | 13 |
Monga momwe amayi amasangalatsira mwana wawo, moteronso Ine ndidzakusangalatsani; ndipo mudzasangalala chifukwa cha Yerusalemu.”
וראיתם ושש לבכם ועצמותיכם כדשא תפרחנה ונודעה יד יהוה את עבדיו וזעם את איביו | 14 |
Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu. Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira ndi kuti ndimakwiyira adani anga.
כי הנה יהוה באש יבוא וכסופה מרכבתיו--להשיב בחמה אפו וגערתו בלהבי אש | 15 |
Taonani, Yehova akubwera ngati moto, ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu; Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake ndi malawi amoto.
כי באש יהוה נשפט ובחרבו את כל בשר ורבו חללי יהוה | 16 |
Pakuti Yehova adzalanga anthu onse ndi moto ndi lupanga, Yehova adzapha anthu ambiri.
המתקדשים והמטהרים אל הגנות אחר אחד (אחת) בתוך אכלי בשר החזיר והשקץ והעכבר--יחדו יספו נאם יהוה | 17 |
Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”
ואנכי מעשיהם ומחשבתיהם--באה לקבץ את כל הגוים והלשנות ובאו וראו את כבודי | 18 |
“Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.
ושמתי בהם אות ושלחתי מהם פליטים אל הגוים תרשיש פול ולוד משכי קשת--תבל ויון האיים הרחקים אשר לא שמעו את שמעי ולא ראו את כבודי--והגידו את כבודי בגוים | 19 |
“Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.
והביאו את כל אחיכם מכל הגוים מנחה ליהוה בסוסים וברכב ובצבים ובפרדים ובכרכרות על הר קדשי ירושלם--אמר יהוה כאשר יביאו בני ישראל את המנחה בכלי טהור בית יהוה | 20 |
Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.
וגם מהם אקח לכהנים ללוים אמר יהוה | 21 |
Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.
כי כאשר השמים החדשים והארץ החדשה אשר אני עשה עמדים לפני--נאם יהוה כן יעמד זרעכם ושמכם | 22 |
“Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova.
והיה מדי חדש בחדשו ומדי שבת בשבתו יבוא כל בשר להשתחות לפני אמר יהוה | 23 |
“Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova.
ויצאו וראו--בפגרי האנשים הפשעים בי כי תולעתם לא תמות ואשם לא תכבה והיו דראון לכל בשר | 24 |
“Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”