< ישעה 6 >
בשנת מות המלך עזיהו ואראה את אדני ישב על כסא רם ונשא ושוליו מלאים את ההיכל | 1 |
Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
שרפים עמדים ממעל לו שש כנפים שש כנפים לאחד בשתים יכסה פניו ובשתים יכסה רגליו--ובשתים יעופף | 2 |
Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira.
וקרא זה אל זה ואמר קדוש קדוש קדוש יהוה צבאות מלא כל הארץ כבודו | 3 |
Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
וינעו אמות הספים מקול הקורא והבית ימלא עשן | 4 |
Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.
ואמר אוי לי כי נדמיתי כי איש טמא שפתים אנכי ובתוך עם טמא שפתים אנכי יושב כי את המלך יהוה צבאות--ראו עיני | 5 |
Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
ויעף אלי אחד מן השרפים ובידו רצפה במלקחים--לקח מעל המזבח | 6 |
Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe.
ויגע על פי--ויאמר הנה נגע זה על שפתיך וסר עונך וחטאתך תכפר | 7 |
Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
ואשמע את קול אדני אמר את מי אשלח ומי ילך לנו ואמר הנני שלחני | 8 |
Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?” Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”
ויאמר לך ואמרת לעם הזה שמעו שמוע ואל תבינו וראו ראו ואל תדעו | 9 |
Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa: “‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa; kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’
השמן לב העם הזה ואזניו הכבד ועיניו השע פן יראה בעיניו ובאזניו ישמע ולבבו יבין ושב--ורפא לו | 10 |
Tsono anthu amenewa uwaphe mtima; uwagonthetse makutu, ndipo uwatseke mʼmaso. Mwina angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi mitima yawo, kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
ואמר עד מתי אדני ויאמר עד אשר אם שאו ערים מאין יושב ובתים מאין אדם והאדמה תשאה שממה | 11 |
Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?” Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti, “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja nʼkusowa wokhalamo, mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,
ורחק יהוה את האדם ורבה העזובה בקרב הארץ | 12 |
mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali, dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.
ועוד בה עשריה ושבה והיתה לבער כאלה וכאלון אשר בשלכת מצבת בם--זרע קדש מצבתה | 13 |
Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko, nachonso chidzawonongedwa. Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu imasiyira chitsa pamene ayidula, chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”