< ישעה 54 >

רני עקרה לא ילדה פצחי רנה וצהלי לא חלה כי רבים בני שוממה מבני בעולה אמר יהוה 1
“Sangalala, iwe mayi wosabala, iwe amene sunabalepo mwana; imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe, iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka; chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri kuposa mkazi wokwatiwa,” akutero Yehova.
הרחיבי מקום אהלך ויריעות משכנותיך יטו--אל תחשכי האריכי מיתריך ויתדתיך חזקי 2
Kulitsa malo omangapo tenti yako, tambasula kwambiri nsalu zake, usaleke; talikitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.
כי ימין ושמאול תפרצי וזרעך גוים יירש וערים נשמות יושיבו 3
Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere; ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina ndipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa.
אל תיראי כי לא תבושי ואל תכלמי כי לא תחפירי כי בשת עלומיך תשכחי וחרפת אלמנותיך לא תזכרי עוד 4
“Usachite mantha; sadzakunyozanso. Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso. Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.
כי בעליך עשיך יהוה צבאות שמו וגאלך קדוש ישראל אלהי כל הארץ יקרא 5
Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu; dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.
כי כאשה עזובה ועצובת רוח קראך יהוה ואשת נעורים כי תמאס אמר אלהיך 6
Yehova wakuyitananso, uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima, mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,” akutero Mulungu wako.
ברגע קטן עזבתיך וברחמים גדלים אקבצך 7
“Kwa kanthawi kochepa, Ine ndinakusiya, koma ndidzakutenganso chifukwa ndimakukonda kwambiri.
בשצף קצף הסתרתי פני רגע ממך ובחסד עולם רחמתיך--אמר גאלך יהוה 8
Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa ndili wokwiya kwambiri. Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya, ndidzakuchitira chifundo,” akutero Yehova Mpulumutsi wako.
כי מי נח זאת לי אשר נשבעתי מעבר מי נח עוד על הארץ--כן נשבעתי מקצף עליך ומגער בך 9
“Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa. Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi. Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima, sindidzakudzudzulaninso.
כי ההרים ימושו והגבעות תמוטינה--וחסדי מאתך לא ימוש וברית שלומי לא תמוט אמר מרחמך יהוה 10
Ngakhale mapiri atagwedezeka ndi zitunda kusunthidwa, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Pangano langa lamtendere silidzasintha,” akutero Yehova amene amakuchitira chifundo.
עניה סערה לא נחמה הנה אנכי מרביץ בפוך אבניך ויסדתיך בספירים 11
“Iwe mzinda wozunzika, wokunthidwa ndi namondwe ndiponso wopanda wokutonthoza, Ine ndidzakongoletsa miyala yako. Maziko ako ndidzamanga ndi miyala ya safiro.
ושמתי כדכד שמשתיך ושעריך לאבני אקדח וכל גבולך לאבני חפץ 12
Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto, ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali.
וכל בניך למודי יהוה ורב שלום בניך 13
Yehova adzaphunzitsa ana ako onse, ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.
בצדקה תכונני רחקי מעשק כי לא תיראי וממחתה כי לא תקרב אליך 14
Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni: Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse. Sudzakhalanso ndi mantha chifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe.
הן גור יגור אפס מאותי--מי גר אתך עליך יפול 15
Ngati wina adzakuthirani nkhondo, si ndine amene ndachititsa; aliyense amene adzalimbana nanu adzagonja chifukwa cha iwe.
הן (הנה) אנכי בראתי חרש--נפח באש פחם ומוציא כלי למעשהו ואנכי בראתי משחית לחבל 16
“Taona, ndi Ine amene ndinalenga munthu wosula zitsulo amene amakoleza moto wamakala ndi kusula zida zoti azigwiritse ntchito. Ndipo ndine amene ndinalenga munthu wosakaza kuti awononge;
כל כלי יוצר עליך לא יצלח וכל לשון תקום אתך למשפט תרשיעי זאת נחלת עבדי יהוה וצדקתם מאתי--נאם יהוה 17
palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke, ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa. Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova. Chipambano chawo chichokera kwa Ine,” akutero Yehova.

< ישעה 54 >

A Dove is Sent Forth from the Ark
A Dove is Sent Forth from the Ark