< ישעה 49 >
שמעו איים אלי והקשיבו לאמים מרחוק יהוה מבטן קראני ממעי אמי הזכיר שמי | 1 |
Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali: Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe, ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
וישם פי כחרב חדה בצל ידו החביאני וישימני לחץ ברור באשפתו הסתירני | 2 |
Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa, anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake; Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa ndipo anandibisa mʼchimake.
ויאמר לי עבדי אתה--ישראל אשר בך אתפאר | 3 |
Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
ואני אמרתי לריק יגעתי לתהו והבל כחי כליתי אכן משפטי את יהוה ופעלתי את אלהי | 4 |
Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe, koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova, ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
ועתה אמר יהוה יוצרי מבטן לעבד לו לשובב יעקב אליו וישראל לא (לו) יאסף ואכבד בעיני יהוה ואלהי היה עזי | 5 |
Yehova anandiwumba ine mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye, choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova, ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
ויאמר נקל מהיותך לי עבד להקים את שבטי יעקב ונצירי (ונצורי) ישראל להשיב ונתתיך לאור גוים להיות ישועתי עד קצה הארץ | 6 |
Yehovayo tsono akuti, “Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobo ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka. Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira, udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”
כה אמר יהוה גאל ישראל קדושו לבזה נפש למתעב גוי לעבד משלים מלכים יראו וקמו שרים וישתחוו--למען יהוה אשר נאמן קדש ישראל ויבחרך | 7 |
Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula, Woyerayo wa Israeli akunena, amene mitundu ya anthu inamuda, amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti, “Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira. Akalonga nawonso adzagwada pansi. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
כה אמר יהוה בעת רצון עניתיך וביום ישועה עזרתיך ואצרך ואתנך לברית עם להקים ארץ להנחיל נחלות שממות | 8 |
Yehova akuti, “Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza; ndinakusunga ndi kukusandutsa kuti ukhale pangano kwa anthu, kuti dziko libwerere mwakale ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
לאמר לאסורים צאו לאשר בחשך הגלו על דרכים ירעו ובכל שפיים מרעיתם | 9 |
Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke ndi a mu mdima kuti aonekere poyera. “Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira ndi msipu pa mʼmalo owuma.
לא ירעבו ולא יצמאו ולא יכם שרב ושמש כי מרחמם ינהגם ועל מבועי מים ינהלם | 10 |
Iwo sadzamva njala kapena ludzu, kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza; chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
ושמתי כל הרי לדרך ומסלתי ירמון | 11 |
Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo, ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.
הנה אלה מרחוק יבאו והנה אלה מצפון ומים ואלה מארץ סינים | 12 |
Taonani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kumadzulo, enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”
רנו שמים וגילי ארץ יפצחו (ופצחו) הרים רנה כי נחם יהוה עמו וענייו ירחם | 13 |
Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga; kondwera, iwe dziko lapansi; imbani nyimbo inu mapiri! Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.
ותאמר ציון עזבני יהוה ואדני שכחני | 14 |
Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya, Ambuye wandiyiwala.”
התשכח אשה עולה מרחם בן בטנה גם אלה תשכחנה ואנכי לא אשכחך | 15 |
“Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni? Ngakhale iye angathe kuyiwala, Ine sindidzakuyiwala iwe!
הן על כפים חקתיך חומתיך נגדי תמיד | 16 |
Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga; makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
מהרו בניך מהרסיך ומחריביך ממך יצאו | 17 |
Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira, ndipo amene anakupasula akuchokapo.
שאי סביב עיניך וראי כלם נקבצו באו לך חי אני נאם יהוה כי כלם כעדי תלבשי ותקשרים ככלה | 18 |
Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe. Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo, anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
כי חרבתיך ושממתיך וארץ הרסתך כי עתה תצרי מיושב ורחקו מבלעיך | 19 |
“Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa ndipo dziko lako ndi kusakazidwa, chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
עוד יאמרו באזניך בני שכליך צר לי המקום גשה לי ואשבה | 20 |
Ana obadwa nthawi yako yachisoni adzanena kuti, ‘Malo ano atichepera, tipatse malo ena woti tikhalemo.’
ואמרת בלבבך מי ילד לי את אלה ואני שכולה וגלמודה גלה וסורה ואלה מי גדל--הן אני נשארתי לבדי אלה איפה הם | 21 |
Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa? Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena; ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa. Ndani anawalera ana amenewa? Ndinatsala ndekha, nanga awa, achokera kuti?’”
כה אמר אדני יהוה הנה אשא אל גוים ידי ואל עמים ארים נסי והביאו בניך בחצן ובנתיך על כתף תנשאנה | 22 |
Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi, “Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere. Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere. Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
והיו מלכים אמניך ושרותיהם מיניקתיך--אפים ארץ ישתחוו לך ועפר רגליך ילחכו וידעת כי אני יהוה אשר לא יבשו קוי | 23 |
Mafumu adzakhala abambo wongokulera ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera. Iwo adzagwetsa nkhope zawo pansi. Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova; iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”
היקח מגבור מלקוח ואם שבי צדיק ימלט | 24 |
Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo, kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?
כי כה אמר יהוה גם שבי גבור יקח ומלקוח עריץ ימלט ואת יריבך אנכי אריב ואת בניך אנכי אושיע | 25 |
Koma zimene Yehova akunena ndi izi, “Ankhondo adzawalanda amʼndende awo, ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo; ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
והאכלתי את מוניך את בשרם וכעסיס דמם ישכרון וידעו כל בשר כי אני יהוה מושיעך וגאלך אביר יעקב | 26 |
Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe; adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu, Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”