< ישעה 48 >
שמעו זאת בית יעקב הנקראים בשם ישראל וממי יהודה יצאו הנשבעים בשם יהוה ובאלהי ישראל יזכירו--לא באמת ולא בצדקה | 1 |
“Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo, inu amene amakutchani dzina lanu Israeli, ndinu a fuko la Yuda, inu mumalumbira mʼdzina la Yehova, ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli, ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
כי מעיר הקדש נקראו ועל אלהי ישראל נסמכו יהוה צבאות שמו | 2 |
Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
הראשנות מאז הגדתי ומפי יצאו ואשמיעם פתאם עשיתי ותבאנה | 3 |
Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale, zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza; tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
מדעתי כי קשה אתה וגיד ברזל ערפך ומצחך נחושה | 4 |
Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve wa nkhongo gwaa, wa mutu wowuma.
ואגיד לך מאז בטרם תבוא השמעתיך--פן תאמר עצבי עשם ופסלי ונסכי צום | 5 |
Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe; zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe kuti unganene kuti, ‘Fano langa ndilo lachita zimenezi, kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
שמעת חזה כלה ואתם הלוא תגידו השמעתיך חדשות מעתה ונצרות ולא ידעתם | 6 |
Inu munamva zinthu zimenezi. Kodi inu simungazivomereze? “Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.
עתה נבראו ולא מאז ולפני יום ולא שמעתם--פן תאמר הנה ידעתין | 7 |
Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale; munali musanazimve mpaka lero lino. Choncho inu simunganene kuti, ‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’
גם לא שמעת גם לא ידעת--גם מאז לא פתחה אזנך כי ידעתי בגוד תבגוד ופשע מבטן קרא לך | 8 |
Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa; makutu anu sanali otsekuka. Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
למען שמי אאריך אפי ותהלתי אחטם לך--לבלתי הכריתך | 9 |
Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa. Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze. Sindidzakuwonongani kotheratu.
הנה צרפתיך ולא בכסף בחרתיך בכור עני | 10 |
Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva; ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.
למעני למעני אעשה כי איך יחל וכבודי לאחר לא אתן | 11 |
Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi. Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke? Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.
שמע אלי יעקב וישראל מקראי אני הוא אני ראשון אף אני אחרון | 12 |
“Tamvera Ine, iwe Yakobo, Israeli, amene ndinakuyitana: Mulungu uja Woyamba ndi Wotsiriza ndine.
אף ידי יסדה ארץ וימיני טפחה שמים קרא אני אליהם יעמדו יחדו | 13 |
Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga. Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
הקבצו כלכם ושמעו מי בהם הגיד את אלה יהוה אהבו--יעשה חפצו בבבל וזרעו כשדים | 14 |
“Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani: Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi? Wokondedwa wa Yehova uja adzachita zomwe Iye anakonzera Babuloni; dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
אני אני דברתי אף קראתיו הבאתיו והצליח דרכו | 15 |
Ine, Inetu, ndayankhula; ndi kumuyitana ndidzamubweretsa ndine ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.
קרבו אלי שמעו זאת לא מראש בסתר דברתי--מעת היותה שם אני ועתה אדני יהוה שלחני--ורוחו | 16 |
“Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi: “Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa; pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.” Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake ndi kundituma.
כה אמר יהוה גאלך קדוש ישראל אני יהוה אלהיך מלמדך להועיל מדריכך בדרך תלך | 17 |
Yehova, Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti, “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsa kuti upindule, ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
לוא הקשבת למצותי ויהי כנהר שלומך וצדקתך כגלי הים | 18 |
Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga, bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
ויהי כחול זרעך וצאצאי מעיך כמעתיו לא יכרת ולא ישמד שמו מלפני | 19 |
Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga, ana ako akanachuluka ngati fumbi; dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga ndipo silikanafafanizidwa konse.”
צאו מבבל ברחו מכשדים בקול רנה הגידו השמיעו זאת הוציאוה עד קצה הארץ אמרו גאל יהוה עבדו יעקב | 20 |
Tulukani mʼdziko la Babuloni! Thawani dziko la Kaldeya! Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo ndipo muzilalikire mpaka kumathero a dziko lapansi; muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
ולא צמאו בחרבות הוליכם--מים מצור הזיל למו ויבקע צור--ויזבו מים | 21 |
Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu; anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe; anangʼamba thanthwelo ndipo munatuluka madzi.
אין שלום אמר יהוה לרשעים | 22 |
“Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.