< ישעה 29 >
הוי אריאל אריאל קרית חנה דוד ספו שנה על שנה חגים ינקפו | 1 |
Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli, mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo! Papite chaka chimodzi kapena ziwiri ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
והציקותי לאריאל והיתה תאניה ואניה והיתה לי כאריאל | 2 |
Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula, mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
וחניתי כדור עליך וצרתי עליך מצב והקימתי עליך מצרת | 3 |
Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo; ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
ושפלת מארץ תדברי ומעפר תשח אמרתך והיה כאוב מארץ קולך ומעפר אמרתך תצפצף | 4 |
Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka, mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi, adzamveka ngati a mzukwa. Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
והיה כאבק דק המון זריך וכמץ עבר המון עריצים והיה לפתע פתאם | 5 |
Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti. Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo. Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
מעם יהוה צבאות תפקד ברעם וברעש וקול גדול סופה וסערה ולהב אש אוכלה | 6 |
Yehova Wamphamvuzonse adzabwera ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu, kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
והיה כחלום חזון לילה המון כל הגוים הצבאים על אריאל וכל צביה ומצדתה והמציקים לה | 7 |
Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga, chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto, gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
והיה כאשר יחלם הרעב והנה אוכל והקיץ וריקה נפשו וכאשר יחלם הצמא והנה שתה והקיץ והנה עיף ונפשו שוקקה--כן יהיה המון כל הגוים הצבאים על הר ציון | 8 |
Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya, koma podzuka ali nayobe njala; kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa, koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa. Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
התמהמהו ותמהו השתעשעו ושעו שכרו ולא יין נעו ולא שכר | 9 |
Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa. Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya, ledzerani, koma osati ndi vinyo, dzandirani, koma osati ndi mowa.
כי נסך עליכם יהוה רוח תרדמה ויעצם את עיניכם את הנביאים ואת ראשיכם החזים כסה | 10 |
Yehova wakugonetsani tulo tofa nato. Watseka maso anu, inu aneneri; waphimba mitu yanu, inu alosi.
ותהי לכם חזות הכל כדברי הספר החתום אשר יתנו אתו אל יודע הספר (ספר) לאמר קרא נא זה ואמר לא אוכל כי חתום הוא | 11 |
Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.”
ונתן הספר על אשר לא ידע ספר לאמר--קרא נא זה ואמר לא ידעתי ספר | 12 |
Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
ויאמר אדני יען כי נגש העם הזה בפיו ובשפתיו כבדוני ולבו רחק ממני--ותהי יראתם אתי מצות אנשים מלמדה | 13 |
Ambuye akuti, “Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo, ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso. Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
לכן הנני יוסף להפליא את העם הזה--הפלא ופלא ואבדה חכמת חכמיו ובינת נבניו תסתתר | 14 |
Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira kuwachitira ntchito zodabwitsa; nzeru za anthu anzeru zidzatha, luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
הוי המעמיקים מיהוה לסתר עצה והיה במחשך מעשיהם ויאמרו מי ראנו ומי ידענו | 15 |
Tsoka kwa amene amayesetsa kubisira Yehova maganizo awo, amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti, “Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
הפככם--אם כחמר היצר יחשב כי יאמר מעשה לעשהו לא עשני ויצר אמר ליצרו לא הבין | 16 |
Inu mumazondotsa zinthu ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya. Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti “Sunandipange ndi iwe?” Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti, “Iwe sudziwa chilichonse?”
הלוא עוד מעט מזער ושב לבנון לכרמל והכרמל ליער יחשב | 17 |
Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde, ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?
ושמעו ביום ההוא החרשים דברי ספר ומאפל ומחשך עיני עורים תראינה | 18 |
Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku, ndipo anthu osaona amene ankakhala mu mdima adzapenya.
ויספו ענוים ביהוה שמחה ואביוני אדם בקדוש ישראל יגילו | 19 |
Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova; ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.
כי אפס עריץ וכלה לץ ונכרתו כל שקדי און | 20 |
Koma anthu ankhanza adzazimirira, oseka anzawo sadzaonekanso, ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.
מחטיאי אדם בדבר ולמוכיח בשער יקשון ויטו בתהו צדיק | 21 |
Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa, kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.
לכן כה אמר יהוה אל בית יעקב אשר פדה את אברהם לא עתה יבוש יעקב ולא עתה פניו יחורו | 22 |
Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti, “Anthu anga sadzachitanso manyazi; nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
כי בראתו ילדיו מעשה ידי בקרבו--יקדישו שמי והקדישו את קדוש יעקב ואת אלהי ישראל יעריצו | 23 |
Akadzaona ana awo ndi ntchito ya manja anga pakati pawo, adzatamanda dzina langa loyera; adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo, ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
וידעו תעי רוח בינה ורוגנים ילמדו לקח | 24 |
Anthu opusa adzapeza nzeru; onyinyirika adzalandira malangizo.”