< ישעה 28 >

הוי עטרת גאות שכרי אפרים וציץ נבל צבי תפארתו--אשר על ראש גיא שמנים הלומי יין 1
Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu. Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa limene lili pa mutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde.
הנה חזק ואמץ לאדני כזרם ברד שער קטב כזרם מים כבירים שטפים הניח לארץ--ביד 2
Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga. Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga, ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho; ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
ברגלים תרמסנה עטרת גאות שכורי אפרים 3
Ulamuliro wa atsogoleri oledzera a ku Efereimu adzawuthetsa.
והיתה ציצת נבל צבי תפארתו אשר על ראש גיא שמנים--כבכורה בטרם קיץ אשר יראה הראה אותה בעודה בכפו יבלענה 4
Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja, udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa imene munthu akangoyiona amayithyola nthawi yokolola isanakwane.
ביום ההוא יהיה יהוה צבאות לעטרת צבי ולצפירת תפארה--לשאר עמו 5
Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse adzakhala ngati nkhata yaufumu, chipewa chokongola kwa anthu ake otsala.
ולרוח משפט--ליושב על המשפט ולגבורה משיבי מלחמה שערה 6
Iye adzapereka mtima wachilungamo kwa oweruza, adzakhala chilimbikitso kwa amene amabweza adani pa zipata za mzinda.
וגם אלה ביין שגו ובשכר תעו כהן ונביא שגו בשכר נבלעו מן היין תעו מן השכר שגו בראה פקו פליליה 7
Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo ndipo akusochera chifukwa cha mowa: ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo; akusochera chifukwa cha mowa, akudzandira pamene akuona masomphenya, kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
כי כל שלחנות מלאו קיא צאה בלי מקום 8
Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.
את מי יורה דעה ואת מי יבין שמועה--גמולי מחלב עתיקי משדים 9
Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani? Uthengawu akufuna kufotokozera yani? Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa, kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
כי צו לצו צו לצו קו לקו קו לקו--זעיר שם זעיר שם 10
Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”
כי בלעגי שפה ובלשון אחרת ידבר אל העם הזה 11
Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino. Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
אשר אמר אליהם זאת המנוחה הניחו לעיף וזאת המרגעה ולא אבוא שמוע 12
anakuwuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo owusira ndi ano.” Koma inu simunamvere.
והיה להם דבר יהוה צו לצו צו לצו קו לקו קו לקו זעיר שם זעיר שם--למען ילכו וכשלו אחור ונשברו ונוקשו ונלכדו 13
Choncho Yehova adzakuphunzitsani pangʼonopangʼono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo, adzapweteka ndi kukodwa mu msampha ndipo adzakutengani ku ukapolo.
לכן שמעו דבר יהוה אנשי לצון--משלי העם הזה אשר בירושלם 14
Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova, inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
כי אמרתם כרתנו ברית את מות ועם שאול עשינו חזה שיט (שוט) שוטף כי עבר (יעבר) לא יבואנו כי שמנו כזב מחסנו ובשקר נסתרנו (Sheol h7585) 15
Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa, ife tachita mgwirizano ndi manda. Pamene mliri woopsa ukadzafika sudzatikhudza ife, chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.” (Sheol h7585)
לכן כה אמר אדני יהוה הנני יסד בציון אבן אבן בחן פנת יקרת מוסד מוסד--המאמין לא יחיש 16
Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi: “Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri ngati maziko mu Ziyoni, mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu; munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
ושמתי משפט לקו וצדקה למשקלת ויעה ברד מחסה כזב וסתר מים ישטפו 17
Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake, ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere; matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza, ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
וכפר בריתכם את מות וחזותכם את שאול לא תקום שוט שוטף כי יעבר והייתם לו למרמס (Sheol h7585) 18
Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa; mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa. Pakuti mliri woopsa udzafika, ndipo udzakugonjetsani. (Sheol h7585)
מדי עברו יקח אתכם כי בבקר בבקר יעבר ביום ובלילה והיה רק זועה הבין שמועה 19
Ndipo ukadzangofika udzakutengani. Udzafika mmawa uliwonse, usiku ndi usana.” Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu adzaopsedwa kwambiri.
כי קצר המצע מהשתרע והמסכה צרה כהתכנס 20
Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo; ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.
כי כהר פרצים יקום יהוה כעמק בגבעון ירגז--לעשות מעשהו זר מעשהו ולעבד עבדתו נכריה עבדתו 21
Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni; adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo, ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
ועתה אל תתלוצצו פן יחזקו מוסריכם כי כלה ונחרצה שמעתי מאת אדני יהוה צבאות--על כל הארץ 22
Tsopano lekani kunyoza, mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri; Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”
האזינו ושמעו קולי הקשיבו ושמעו אמרתי 23
Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga; mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.
הכל היום יחרש החרש לזרע יפתח וישדד אדמתו 24
Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?
הלוא אם שוה פניה והפיץ קצח וכמן יזרק ושם חטה שורה ושערה נסמן וכסמת גבלתו 25
Pamene iye wasalaza mundawo, kodi samafesa mawere ndi chitowe? Kodi suja samadzala tirigu ndi barele mʼmizere yake, nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
ויסרו למשפט אלהיו יורנו 26
Mulungu wake amamulangiza ndi kumuphunzitsa njira yabwino.
כי לא בחרוץ יודש קצח ואופן עגלה על כמן יוסב כי במטה יחבט קצח וכמן בשבט 27
Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero, kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta; mawere amapuntha ndi ndodo ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.
לחם יודק כי לא לנצח אדוש ידושנו והמם גלגל עגלתו ופרשיו לא ידקנו 28
Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi, komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke. Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta, koma akavalo ake satekedza tiriguyo.
גם זאת מעם יהוה צבאות יצאה הפלא עצה הגדיל תושיה 29
Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.

< ישעה 28 >