< ישעה 26 >
ביום ההוא יושר השיר הזה בארץ יהודה עיר עז לנו ישועה ישית חומות וחל | 1 |
Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi. Tili ndi mzinda wolimba. Mulungu amawuteteza ndi zipupa ndi malinga.
פתחו שערים ויבא גוי צדיק שמר אמנים | 2 |
Tsekulani zipata za mzinda kuti mtundu wolungama ndi wokhulupirika ulowemo.
יצר סמוך תצר שלום שלום כי בך בטוח | 3 |
Inu mudzamupatsa munthu wa mtima wokhazikika mtendere weniweni.
בטחו ביהוה עדי עד כי ביה יהוה צור עולמים | 4 |
Mudalireni Yehova mpaka muyaya, chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.
כי השח ישבי מרום קריה נשגבה ישפילנה ישפילה עד ארץ יגיענה עד עפר | 5 |
Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba, iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula, amagumula makoma ake ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
תרמסנה רגל רגלי עני פעמי דלים | 6 |
Mapazi a anthu akuwupondereza, mapazi a anthu oponderezedwa, mapazi anthu osauka.
ארח לצדיק מישרים ישר מעגל צדיק תפלס | 7 |
Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza, Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.
אף ארח משפטיך יהוה קוינוך--לשמך ולזכרך תאות נפש | 8 |
Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama, ife timayembekezera Inu; mitima yathu imakhumba kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu.
נפשי אויתך בלילה אף רוחי בקרבי אשחרך כי כאשר משפטיך לארץ--צדק למדו ישבי תבל | 9 |
Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse; nthawi yammawa ndimafunafuna Inu. Pamene muweruza dziko lapansi anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
יחן רשע בל למד צדק בארץ נכחות יעול ובל יראה גאות יהוה | 10 |
Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa, saphunzira chilungamo. Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo, ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
יהוה רמה ידך בל יחזיון יחזו ויבשו קנאת עם אף אש צריך תאכלם | 11 |
Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange, koma iwo sakuliona dzanjalo. Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu; ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
יהוה תשפת שלום לנו כי גם כל מעשינו פעלת לנו | 12 |
Yehova, mumatipatsa mtendere; ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.
יהוה אלהינו בעלונו אדנים זולתך לבד בך נזכיר שמך | 13 |
Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu, koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.
מתים בל יחיו--רפאים בל יקמו לכן פקדת ותשמידם ותאבד כל זכר למו | 14 |
Iwo tsopano sadzadzukanso; mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga; palibenso amene amawakumbukira.
יספת לגוי יהוה יספת לגוי נכבדת רחקת כל קצוי ארץ | 15 |
Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu; mwauchulukitsa ndithu ndipo mwalandirapo ulemu; mwaukuza mbali zonse za dziko.
יהוה בצר פקדוך צקון לחש מוסרך למו | 16 |
Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso; pamene munawalanga, iwo anapemphera kwa Inu.
כמו הרה תקריב ללדת תחיל תזעק בחבליה--כן היינו מפניך יהוה | 17 |
Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu, ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.
הרינו חלנו כמו ילדנו רוח ישועת בל נעשה ארץ ובל יפלו ישבי תבל | 18 |
Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana, koma sitinapindulepo kanthu, kapena kupulumutsa dziko lapansi; sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
יחיו מתיך נבלתי יקומון הקיצו ורננו שכני עפר כי טל אורת טלך וארץ רפאים תפיל | 19 |
Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo; matupi awo adzadzuka. Iwo amene ali ku fumbi tsopano adzadzuka ndi kuyimba mosangalala. Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera, momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
לך עמי בא בחדריך וסגר דלתיך (דלתך) בעדך חבי כמעט רגע עד יעבור (יעבר) זעם | 20 |
Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanu ndipo mukadzitsekere; mukabisale kwa kanthawi kochepa mpaka ukali wake utatha.
כי הנה יהוה יצא ממקומו לפקד עון ישב הארץ עליו וגלתה הארץ את דמיה ולא תכסה עוד על הרוגיה | 21 |
Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala; akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo. Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo; dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.