< ישעה 24 >
הנה יהוה בוקק הארץ ובולקה ועוה פניה והפיץ ישביה | 1 |
Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi ndi kulisandutsa chipululu; Iye adzasakaza maonekedwe ake ndi kumwaza anthu ake onse.
והיה כעם ככהן כעבד כאדניו כשפחה כגברתה כקונה כמוכר כמלוה כלוה כנשה כאשר נשא בו | 2 |
Aliyense zidzamuchitikira mofanana: wansembe chimodzimodzi munthu wamba, antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna, antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi, wogula chimodzimodzi wogulitsa, wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa, okongola chimodzimodzi okongoza.
הבוק תבוק הארץ והבוז תבז כי יהוה דבר את הדבר הזה | 3 |
Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu ndi kusakazikiratu. Yehova wanena mawu awa.
אבלה נבלה הארץ אמללה נבלה תבל אמללו מרום עם הארץ | 4 |
Dziko lapansi likulira ndipo likufota, dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma, anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.
והארץ חנפה תחת ישביה כי עברו תורת חלפו חק הפרו ברית עולם | 5 |
Anthu ayipitsa dziko lapansi; posamvera malangizo ake; pophwanya mawu ake ndi pangano lake lamuyaya.
על כן אלה אכלה ארץ ויאשמו ישבי בה על כן חרו ישבי ארץ ונשאר אנוש מזער | 6 |
Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi; anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo, iwo asakazika ndipo atsala ochepa okha.
אבל תירוש אמללה גפן נאנחו כל שמחי לב | 7 |
Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota; onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.
שבת משוש תפים חדל שאון עליזים שבת משוש כנור | 8 |
Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha, phokoso la anthu osangalala latha, zeze wosangalatsa wati zii.
בשיר לא ישתו יין ימר שכר לשתיו | 9 |
Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo; akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.
נשברה קרית תהו סגר כל בית מבוא | 10 |
Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka; nyumba iliyonse yatsekedwa.
צוחה על היין בחוצות ערבה כל שמחה גלה משוש הארץ | 11 |
Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo; chimwemwe chonse chatheratu, palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.
נשאר בעיר שמה ושאיה יכת שער | 12 |
Mzinda wasanduka bwinja zipata zake zagumuka.
כי כה יהיה בקרב הארץ בתוך העמים כנקף זית כעוללת אם כלה בציר | 13 |
Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi ndiponso pakati pa mitundu ya anthu. Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa, kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.
המה ישאו קולם ירנו בגאון יהוה צהלו מים | 14 |
Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe; anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
על כן בארים כבדו יהוה באיי הים שם יהוה אלהי ישראל | 15 |
Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova; ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
מכנף הארץ זמרת שמענו צבי לצדיק ואמר רזי לי רזי לי אוי לי בגדים בגדו ובגד בוגדים בגדו | 16 |
Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda “Wolungamayo.” Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo, inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
פחד ופחת ופח עליך יושב הארץ | 17 |
Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje ndi msampha zikukudikirani.
והיה הנס מקול הפחד יפל אל הפחת והעולה מתוך הפחת ילכד בפח כי ארבות ממרום נפתחו וירעשו מוסדי ארץ | 18 |
Aliyense wothawa phokoso la zoopsa adzagwa mʼdzenje; ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo adzakodwa ndi msampha. Zitseko zakumwamba zatsekulidwa, ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.
רעה התרעעה הארץ פור התפוררה ארץ מוט התמוטטה ארץ | 19 |
Dziko lapansi lathyokathyoka, ndipo lagawika pakati, dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.
נוע תנוע ארץ כשכור והתנודדה כמלונה וכבד עליה פשעה ונפלה ולא תסיף קום | 20 |
Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba; lalemedwa ndi machimo ake. Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.
והיה ביום ההוא יפקד יהוה על צבא המרום במרום ועל מלכי האדמה על האדמה | 21 |
Tsiku limenelo Yehova adzalanga amphamvu a kumwamba ndiponso mafumu apansi pano.
ואספו אספה אסיר על בור וסגרו על מסגר ומרב ימים יפקדו | 22 |
Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi ngati amʼndende amene ali mʼdzenje. Adzawatsekera mʼndende ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.
וחפרה הלבנה ובושה החמה כי מלך יהוה צבאות בהר ציון ובירושלם ונגד זקניו כבוד | 23 |
Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira; pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.