< ישעה 18 >
הוי ארץ צלצל כנפים אשר מעבר לנהרי כוש | 1 |
Tsoka kwa anthu a ku Kusi. Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.
השלח בים צירים ובכלי גמא על פני מים לכו מלאכים קלים אל גוי ממשך ומורט אל עם נורא מן הוא והלאה--גוי קו קו ומבוסה אשר בזאו נהרים ארצו | 2 |
Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo, mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi, ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro, kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala, ndi woopedwa ndi anthu. Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena. Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
כל ישבי תבל ושכני ארץ כנשא נס הרים תראו וכתקע שופר תשמעו | 3 |
Inu nonse anthu a pa dziko lonse, inu amene mumakhala pa dziko lapansi, pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri yangʼanani, ndipo pamene lipenga lilira mumvere.
כי כה אמר יהוה אלי אשקוטה (אשקטה) ואביטה במכוני כחם צח עלי אור כעב טל בחם קציר | 4 |
Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti, “Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana, monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha, monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”
כי לפני קציר כתם פרח ובסר גמל יהיה נצה וכרת הזלזלים במזמרות ואת הנטישות הסיר התז | 5 |
Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka ndiponso mphesa zitayamba kupsa, Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira, ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
יעזבו יחדו לעיט הרים ולבהמת הארץ וקץ עליו העיט וכל בהמת הארץ עליו תחרף | 6 |
Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama ndiponso zirombo zakuthengo; mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe, ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
בעת ההיא יובל שי ליהוה צבאות עם ממשך ומורט ומעם נורא מן הוא והלאה גוי קו קו ומבוסה אשר בזאו נהרים ארצו אל מקום שם יהוה צבאות הר ציון | 7 |
Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse, zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala, kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe, mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo, anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje. Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.