< הושע 5 >

שמעו זאת הכהנים והקשיבו בית ישראל ובית המלך האזינו--כי לכם המשפט כי פח הייתם למצפה ורשת פרושה על תבור 1
“Ansembe inu, imvani izi! Inu Aisraeli, tcherani khutu! Inu nyumba yaufumu, mvetserani! Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu: Inu munali ngati msampha ku Mizipa, munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
ושחטה שטים העמיקו ואני מוסר לכלם 2
Owukira azama mʼmoyo wakupha, Ine ndidzawalanga onsewo.
אני ידעתי אפרים וישראל לא נכחד ממני כי עתה הזנית אפרים נטמא ישראל 3
Ndimadziwa zonse za Efereimu; Aisraeli ndi osabisika kwa Ine. Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere; Israeli wadziyipitsa.
לא יתנו מעלליהם לשוב אל אלהיהם כי רוח זנונים בקרבם ואת יהוה לא ידעו 4
“Ntchito zawo siziwalola kubwerera kwa Mulungu wawo. Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere; Iwo sadziwa Yehova.
וענה גאון ישראל בפניו וישראל ואפרים יכשלו בעונם--כשל גם יהודה עמם 5
Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa; Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo; Yudanso anagwa nawo pamodzi.
בצאנם ובבקרם ילכו לבקש את יהוה--ולא ימצאו חלץ מהם 6
Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo kukapereka nsembe kwa Yehova, iwo sadzamupeza; Iye wawachokera.
ביהוה בגדו כי בנים זרים ילדו עתה יאכלם חדש את חלקיהם 7
Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova; amabereka ana amʼchigololo ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.
תקעו שופר בגבעה חצצרה ברמה הריעו בית און אחריך בנימין 8
“Womba lipenga mu Gibeya, liza mbetete mu Rama. Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni; iwe Benjamini tsogolera.
אפרים לשמה תהיה ביום תוכחה בשבטי ישראל הודעתי נאמנה 9
Efereimu adzasanduka bwinja pa tsiku la chilango. Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi pakati pa mafuko a Israeli.
היו שרי יהודה כמסיגי גבול עליהם אשפוך כמים עברתי 10
Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu amene amasuntha miyala ya mʼmalire. Ndidzawakhutulira ukali wanga ngati madzi a chigumula.
עשוק אפרים רצוץ משפט כי הואיל הלך אחרי צו 11
Efereimu waponderezedwa, akulangidwa chifukwa chotsatira mafano.
ואני כעש לאפרים וכרקב לבית יהודה 12
Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu, ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.
וירא אפרים את חליו ויהודה את מזרו וילך אפרים אל אשור וישלח אל מלך ירב והוא לא יוכל לרפא לכם ולא יגהה מכם מזור 13
“Efereimu ataona nthenda yake, ndi Yuda ataona zilonda zake, pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya, ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza. Koma mfumuyo singathe kukuchizani, singathe kuchiritsa mabala anu.
כי אנכי כשחל לאפרים וככפיר לבית יהודה אני אני אטרף ואלך אשא ואין מציל 14
Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu. Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda. Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo; ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
אלך אשובה אל מקומי עד אשר יאשמו ובקשו פני בצר להם ישחרנני 15
Ndipo ndidzabwerera ku malo anga mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo. Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga; mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”

< הושע 5 >