< הושע 13 >

כדבר אפרים רתת נשא הוא בישראל ויאשם בבעל וימת 1
Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera; anali wolemekezeka mu Israeli. Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
ועתה יוספו לחטא ויעשו להם מסכה מכספם כתבונם עצבים מעשה חרשים כלה להם הם אמרים זבחי אדם עגלים ישקון 2
Tsopano akunka nachimwirachimwirabe; akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo, zifanizo zopangidwa mwaluso, zonsezo zopangidwa ndi amisiri. Amanena za anthu awa kuti, “Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
לכן יהיו כענן בקר וכטל משכים הלך כמץ יסער מגרן וכעשן מארבה 3
Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa, ngati mame amene amakamuka msanga, ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu, ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
ואנכי יהוה אלהיך מארץ מצרים ואלהים זולתי לא תדע ומושיע אין בלתי 4
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mu Igupto. Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha, palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
אני ידעתיך במדבר--בארץ תלאבות 5
Ndinakusamalira mʼchipululu, mʼdziko lotentha kwambiri.
כמרעיתם וישבעו--שבעו וירם לבם על כן שכחוני 6
Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta; iwo atakhuta anayamba kunyada; ndipo anandiyiwala Ine.
ואהי להם כמו שחל--כנמר על דרך אשור 7
Motero ndidzawalumphira ngati mkango, ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
אפגשם כדב שכול ואקרע סגור לבם ואכלם שם כלביא חית השדה תבקעם 8
Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake, ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola. Ndidzawapwepweta ngati mkango; chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
שחתך ישראל כי בי בעזרך 9
“Iwe Israeli, wawonongedwa, chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
אהי מלכך אפוא ויושיעך בכל עריך ושפטיך--אשר אמרת תנה לי מלך ושרים 10
Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse? Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti, amene iwe unanena za iwo kuti, ‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
אתן לך מלך באפי ואקח בעברתי 11
Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima, ndipo ndinayichotsa mwaukali.
צרור עון אפרים צפונה חטאתו 12
Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa, machimo ake alembedwa mʼbuku.
חבלי יולדה יבאו לו הוא בן לא חכם כי עת לא יעמד במשבר בנים 13
Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera, koma iye ndi mwana wopanda nzeru, pamene nthawi yake yobadwa yafika iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.
מיד שאול אפדם ממות אגאלם אהי דבריך מות אהי קטבך שאול--נחם יסתר מעיני (Sheol h7585) 14
“Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda; ndidzawawombola ku imfa. Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? “Sindidzachitanso chifundo, (Sheol h7585)
כי הוא בין אחים יפריא יבוא קדים רוח יהוה ממדבר עלה ויבוש מקורו ויחרב מעינו--הוא ישסה אוצר כל כלי חמדה 15
ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake, mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera, ikuwomba kuchokera ku chipululu. Kasupe wake adzaphwa ndipo chitsime chake chidzawuma. Chuma chake chonse chamtengowapatali chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
תאשם שמרון כי מרתה באלהיה בחרב יפלו--עלליהם ירטשו והריותיו יבקעו 16
Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo, chifukwa anawukira Mulungu wawo. Adzaphedwa ndi lupanga; ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi, akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”

< הושע 13 >