< חבקוק 1 >

המשא אשר חזה חבקוק הנביא 1
Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.
עד אנה יהוה שועתי ולא תשמע אזעק אליך חמס ולא תושיע 2
Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani, koma wosayankha? Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!” koma wosatipulumutsa?
למה תראני און ועמל תביט ושד וחמס לנגדי ויהי ריב ומדון ישא 3
Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa? Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa? Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa; pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
על כן תפוג תורה ולא יצא לנצח משפט כי רשע מכתיר את הצדיק על כן יצא משפט מעקל 4
Kotero malamulo anu atha mphamvu, ndipo chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oyipa aposa olungama, kotero apotoza chilungamo.
ראו בגוים והביטו והתמהו תמהו כי פעל פעל בימיכם לא תאמינו כי יספר 5
“Yangʼanani pakati pa mitundu ya anthu, ndipo penyetsetsani, ndipo muthedwe nazo nzeru. Pakuti ndidzachitadi zinthu pa nthawi yanu zimene inu simudzazikhulupirira, ngakhale wina atakufotokozerani.
כי הנני מקים את הכשדים הגוי המר והנמהר ההולך למרחבי ארץ לרשת משכנות לא לו 6
Pakuti taonani, Ine ndikuwutsa Ababuloni, anthu ankhanza ndiponso amphamvu, amene amapita pa dziko lonse lapansi kukalanda malo amene si awo.
אים ונורא הוא ממנו משפטו ושאתו יצא 7
Iwowa ndi anthu ochititsa mantha, ndipo ndi owopsa; amadzipangira okha malamulo ndi kudzipezera okha ulemu.
וקלו מנמרים סוסיו וחדו מזאבי ערב ופשו פרשיו ופרשיו מרחוק יבאו--יעפו כנשר חש לאכול 8
Akavalo awo ndi aliwiro kwambiri kupambana akambuku ndi owopsa kupambana mimbulu yolusa nthawi ya madzulo. Okwerapo awo akuthamanga molunjika; a pa akavalo awo ndi ochokera kutali, akuwuluka ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama;
כלה לחמס יבוא מגמת פניהם קדימה ויאסף כחול שבי 9
onse akubwera atakonzekera zachiwawa. Gulu la ankhondo likubwera ngati mphepo ya mʼchipululu ndi kugwira akapolo ochuluka ngati mchenga.
והוא במלכים יתקלס ורזנים משחק לו הוא לכל מבצר ישחק ויצבר עפר וילכדה 10
Akunyoza mafumu ndiponso kuchitira chipongwe olamulira. Akupeputsa mizinda yonse yotetezedwa; akumanga mitumbira ndi kulanda mizindayo.
אז חלף רוח ויעבר ואשם זו כחו לאלהו 11
Kenaka amasesa mofulumira ngati mphepo nʼkumangopitirirabe, anthu ochimwa, amene mphamvu zawo ndiye mulungu wawo.”
הלוא אתה מקדם יהוה אלהי קדשי--לא נמות יהוה למשפט שמתו וצור להוכיח יסדתו 12
Inu Yehova, kodi sindinu wachikhalire? Mulungu wanga, Woyera wanga, ife sitidzafa. Inu Yehova, munawasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo; Inu Thanthwe, munawayika iwowo kuti atilange.
טהור עינים מראות רע והביט אל עמל לא תוכל למה תביט בוגדים--תחריש בבלע רשע צדיק ממנו 13
Maso anu ndi oyera kwambiri safuna kuona choyipa; Inu simulekerera cholakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu ochita zachinyengowa? Chifukwa chiyani muli chete pamene anthu oyipa akuwononga anthu olungama kupambana iwowo?
ותעשה אדם כדגי הים--כרמש לא משל בו 14
Mwasandutsa anthu kukhala ngati nsomba zamʼnyanja, ngati zolengedwa zamʼnyanja zimene zilibe wolamulira.
כלה בחכה העלה--יגרהו בחרמו ויאספהו במכמרתו על כן ישמח ויגיל 15
Mdani wawo woyipa amakoka anthu onse ndi mbedza, amawakola mu ukonde wake, amawasonkhanitsa mu khoka lake; kotero iyeyo amakondwa ndi kusangalala.
על כן יזבח לחרמו ויקטר למכמרתו כי בהמה שמן חלקו ומאכלו בראה 16
Choncho iye amaperekera nsembe ukonde wake ndiponso kufukizira lubani khoka lake, popeza ukonde wakewo ndiye umamubweretsera moyo wapamwamba ndipo amadya chakudya chabwino kwambiri.
העל כן יריק חרמו ותמיד להרג גוים לא יחמול 17
Kodi iye azipitirabe kugwiritsa ntchito makoka akewo, kuwononga mitundu ya anthu mopanda chifundo?

< חבקוק 1 >